Chivumbulutso 4:1-11

4  Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khomo lotseguka kumwamba. Ndipo mawu oyamba amene ndinawamva akundilankhula anali ngati kulira kwa lipenga.+ Mawuwo anali akuti: “Kwera kumwamba kuno,+ ndikuonetse zinthu zimene ziyenera kuchitika.”+  Zitatero, nthawi yomweyo ndinakhala mumphamvu ya mzimu, ndipo mpando wachifumu+ unaoneka uli pamalo ake kumwamba,+ wina atakhalapo.+  Wokhala pampandoyo, anali wooneka+ ngati mwala wa yasipi,+ ndi mwala wofiira wamtengo wapatali. Utawaleza+ wooneka ngati mwala wa emarodi+ unazungulira mpando wachifumuwo.  Kuzungulira mpando wachifumuwo, panalinso mipando yachifumu yokwanira 24. Pamipando yachifumuyo,+ ndinaona patakhala akulu+ 24+ ovala malaya akunja oyera,+ ndi zisoti zachifumu+ zagolide pamitu pawo.  Kumpando wachifumuko kunali kutuluka mphezi,+ mawu, ndi mabingu.+ Panalinso nyale+ zamoto 7 zikuyaka patsogolo pa mpando wachifumuwo. Zimenezo zikuimira mizimu 7+ ya Mulungu.  Patsogolo pa mpando wachifumuwo, panali nyanja yoyera mbee! ngati galasi,+ yooneka ngati mwala wa kulusitalo. Pakati m’pakati pa mpando wachifumuwo, ndiponso mouzungulira, panali zamoyo zinayi+ zokhala ndi maso ambirimbiri, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.  Chamoyo choyamba chinali ngati mkango.+ Chamoyo chachiwiri chinali ngati mwana wa ng’ombe wamphongo.+ Chamoyo+ chachitatu chinali ndi nkhope ngati ya munthu, ndipo chamoyo+ chachinayi chinali ngati chiwombankhanga+ chimene chikuuluka.  Zamoyo zinayizo,+ chilichonse chinali ndi mapiko 6.+ Zinali ndi maso thupi lonse ngakhalenso kunsi kwa mapiko.+ Zamoyo zimenezi sizinali kupuma usana ndi usiku. Zinali kunena kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova+ Mulungu, Wamphamvuyonse,+ amene analipo, amene alipo,+ ndi amene akubwera.”  Nthawi zonse zamoyozo zikamapereka ulemerero, ndi ulemu, ndiponso zikamayamikira+ Wokhala pampando wachifumuyo,+ Iye amene adzakhalabe ndi moyo kwamuyaya,+ 10  akulu 24 aja+ anali kugwada ndi kuwerama pamaso pa Wokhala pampando wachifumuyo, ndi kulambira+ wokhala ndi moyo kwamuyayayo. Iwo anali kuponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa mpando wachifumuwo, ndi kunena kuti: 11  “Ndinu woyenera, inu Yehova* Mulungu wathu wamphamvu,+ kulandira ulemerero+ ndi ulemu,+ chifukwa munalenga zinthu zonse,+ ndipo mwa kufuna kwanu,+ zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.