Chivumbulutso 3:1-22
3 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Sade, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena iye amene ali ndi mizimu 7+ ya Mulungu, ndi nyenyezi 7.+ ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti uli ndi dzina lakuti uli moyo, pamene ndiwe wakufa.+
2 Khala maso,+ ndipo limbikitsa+ otsala amene atsala pang’ono kufa, chifukwa ndapeza kuti ntchito zako sizinachitidwe mokwanira pamaso pa Mulungu wanga.+
3 Choncho, pitiriza kukumbukira zimene unalandira+ ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira,+ ndipo ulape.+ Ndithudi, ukapanda kudzuka,+ ndidzabwera ngati mbala,+ ndipo sudzadziwa ngakhale pang’ono ola limene ndidzafike kwa iwe.+
4 “‘Ngakhale zili choncho, uli ndi mayina+ angapo mu Sade a anthu amene sanaipitse+ malaya awo akunja. Amenewa adzayenda ndi ine atavala malaya oyera,+ chifukwa ndi oyenerera.+
5 Choncho amene wapambana pa nkhondo+ adzavekedwa malaya akunja oyera.+ Ndipo sindidzafafaniza dzina lake m’buku la moyo,+ koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga,+ ndi pamaso pa angelo ake.+
6 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena+ ku mipingo.’
7 “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Filadefiya, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena woyerayo,+ amene ali woona,+ yemwe ali ndi kiyi wa Davide.+ Iye amene amati akatsegula palibe wina amene angatseke, ndipo akatseka palibe wina amene angatsegule.
8 ‘Ndikudziwa ntchito zako.+ Taona! Ndakutsegulira khomo+ pamaso pako, limene wina sangalitseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa, ndiponso kuti unasunga mawu anga. Ndikudziwanso kuti wakhala wokhulupirika ku dzina langa.+
9 Taona! Anthu ochokera m’sunagoge wa Satana, amene amanama+ kuti ndi Ayuda+ pamene si Ayuda, ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada ndi kuwerama+ pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kudziwa kuti ndimakukonda.
10 Popeza unasunga mawu onena za kupirira kwanga,+ inenso ndidzakusunga+ pa ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Ndidzakusunga pa ola limene likubwera kudzayesa okhala padziko lapansi.+
11 Ndikubwera mofulumira.+ Gwirabe mwamphamvu chimene uli nacho,+ kuti wina asakulande mphoto* yako.+
12 “‘Wopambana pa nkhondo, ndidzamuika kukhala mzati+ m’kachisi+ wa Mulungu wanga,+ ndipo sadzachokamonso. Ndidzamulemba dzina la Mulungu wanga, ndiponso dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano,+ wotsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga. Ndidzamulembanso dzina langa latsopano.+
13 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’
14 “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Laodikaya,+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena Ame,+ mboni+ yokhulupirika+ ndi yoona,+ woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.+
15 ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti si iwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha.
16 Choncho, chifukwa choti ndiwe wofunda, osati wotentha+ kapena wozizira,+ ndikulavula m’kamwa mwanga.
17 Iwe ukunena kuti: “Ndine wolemera,+ ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu,” koma sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu,+ ndi wamaliseche.
18 Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone.
19 “‘Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.+ Choncho, khala wodzipereka ndipo ulape.+
20 Taona! Ndaima pakhomo,+ ndipo ndikugogoda. Wina akamva mawu anga ndi kutsegula chitseko,+ ndidzalowa m’nyumba mwake ndipo iye ndi ine tidzadyera limodzi chakudya chamadzulo.
21 Wopambana pa nkhondo+ ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu,+ monga mmene ine ndinakhalira+ ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu+ nditapambana pa nkhondo.
22 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”