Chivumbulutso 11:1-19
11 Ndiyeno ndinapatsidwa bango lokhala ngati ndodo+ ndipo ndinauzidwa kuti: “Nyamuka, kayeze nyumba yopatulika ya pakachisi+ wa Mulungu, guwa lansembe, ndi amene akulambira mmenemo.
2 Koma bwalo lakunja+ kwa nyumba yopatulika ya pakachisi ulisiye, usaliyeze m’pang’ono pomwe chifukwa laperekedwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo iwo adzapondaponda mzinda woyera+ kwa miyezi 42.+
3 Ndiyeno ndidzachititsa mboni zanga ziwiri+ kunenera+ kwa masiku 1,260, zitavala ziguduli.”+
4 Mboni zimenezi zikuimiridwa ndi mitengo iwiri ya maolivi,+ ndi zoikapo nyale ziwiri,+ ndipo mbonizo zaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.+
5 Ngati wina aliyense akufuna kuzivulaza, moto umatuluka m’kamwa mwawo ndi kupsereza adani awo.+ Ngati wina angafune kuzivulaza, ayenera kuphedwa mwanjira imeneyi.
6 Mboni zimenezi zili ndi ulamuliro wotseka kumwamba+ kuti mvula isagwe+ m’masiku onse amene zikunenera. Zilinso ndi ulamuliro pamadzi, woti ziwasandutse magazi.+ Komanso zili ndi ulamuliro wokantha dziko lapansi ndi mliri wamtundu uliwonse, maulendo ambirimbiri mogwirizana ndi mmene zingafunire.
7 Zikamaliza kuchitira umboni wawo, chilombo chotuluka muphompho+ chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa ndi kuzipha.+
8 Mitembo yawo idzagona pamsewu waukulu mumzinda waukulu, umene mophiphiritsira ukutchedwa Sodomu+ ndi Iguputo, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwa.+
9 Mitundu ya anthu, mafuko, zinenero, ndi mayiko,+ adzayang’anitsitsa mitembo yawo masiku atatu ndi hafu,+ ndipo sadzalola kuti mitemboyo iikidwe m’manda.
10 Okhala padziko lapansi adzakondwera+ kwambiri ndi imfa yawoyo. Iwo adzatumizirana+ mphatso, chifukwa aneneri awiriwa anazunza okhala padziko lapansi.
11 Masiku atatu ndi hafu+ aja atatha, mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unalowa mwa mboni zija.+ Ndiyeno mbonizo zinaimirira, ndipo amene anali kuziona anagwidwa ndi mantha aakulu.
12 Kenako mbonizo zinamva mawu ofuula+ ochokera kumwamba akuziuza kuti: “Kwerani kuno.”+ Ndipo zinakwera kumwamba mumtambo, moti adani awo anaziona.
13 Mu ola limenelo, kunachitika chivomezi chachikulu, ndipo gawo limodzi mwa magawo khumi+ a mzindawo linagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomezicho, ndipo ena onse anachita mantha n’kupereka ulemerero kwa Mulungu wakumwamba.+
14 Tsoka+ lachiwiri linapita. Koma tsoka lachitatu linali kubwera mofulumira.
15 Mngelo wa 7 analiza lipenga+ lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu+ ndi wa Khristu wake.+ Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.”+
16 Ndipo akulu 24 aja,+ amene anali atakhala pamipando yawo yachifumu pamaso pa Mulungu, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo analambira Mulungu+
17 ndi mawu akuti: “Tikukuyamikani+ inu Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse,+ Inu amene mulipo+ ndi amene munalipo, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu+ ndi kuyamba kulamulira monga mfumu.+
18 Koma mitundu ya anthu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika. Inafikanso nthawi yoikidwiratu yakuti akufa aweruzidwe, nthawi yopereka mphoto+ kwa akapolo anu aneneri,+ ndiponso kwa oyerawo, ndi oopa dzina lanu, olemekezeka ndi onyozeka omwe.+ Komanso, nthawi yowononga+ amene akuwononga dziko lapansi.”+
19 Nyumba yopatulika ya pakachisi wa Mulungu imene ili kumwamba+ inatsegulidwa, ndipo likasa+ la pangano lake linaonekera m’nyumba yake yopatulika+ ya pakachisi. Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu, kunachita chivomezi, ndipo kunagwa matalala ambiri zedi.