Chivumbulutso 17:1-18

17  Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7+ aja, anabwera n’kundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikulu+ lokhala pamadzi ambiri,+  limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo dama,+ ndipo linaledzeretsa anthu okhala padziko lapansi ndi vinyo wa dama* lake.”+  Mu mphamvu ya mzimu,+ mngeloyo ananditengera kuchipululu. Ndipo ndinaona mkazi atakhala pachilombo+ chofiira kwambiri, chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu.+ Chinali ndi mitu 7,+ ndi nyanga 10.  Mkaziyo anavala zovala zofiirira+ ndi zofiira kwambiri.+ Anadzikongoletsa ndi golide, ndi mwala winawake wamtengo wapatali, ndiponso ngale.+ M’dzanja lake, anali ndi kapu yagolide+ yodzaza ndi zonyansa+ ndi zinthu zodetsedwa zokhudzana ndi dama lake.+  Pamphumi pake panalembedwa dzina lachinsinsi+ lakuti: “Babulo Wamkulu, mayi wa mahule+ ndi wa zonyansa za padziko lapansi.”+  Ndipo ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi+ a oyera, ndiponso magazi a mboni za Yesu.+ Nditamuona mkaziyo, ndinadabwa kwambiri.+  Koma mngelo uja anandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukudabwa? Ndikuuza chinsinsi cha mkazi ameneyu,+ ndi cha chilombo chimene wakwerapo, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10:+  Chilombo chimene waona, chinalipo,+ tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho,+ ndipo chidzapita ku chiwonongeko. Anthu okhala padziko lapansi akaona kuti chilombocho chinalipo, tsopano palibe, komabe chidzakhalapo, adzadabwa kwambiri pochita nacho chidwi. Koma mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo+ kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+  “Apa m’pamene pakufunika kuchenjera ndiponso kukhala ndi nzeru:+ Mitu 7+ ikuimira mapiri 7,+ amene mkazi uja amakhala pamwamba pake. 10  Palinso mafumu 7. Asanu agwa,+ imodzi ilipo,+ inayo sinafikebe.+ Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.+ 11  Ndipo chilombo chimene chinalipo, koma tsopano palibe,+ n’chimenenso chili mfumu ya 8, koma yotuluka mwa mafumu 7 aja, ndipo ikupita ku chiwonongeko. 12  “Nyanga 10 zimene unaona zija, zikuimira mafumu 10+ amene sanalandirebe ufumu wawo. Koma adzalandira ulamuliro monga mafumu ndipo adzalamulira limodzi ndi chilombo kwa ola limodzi. 13  Mafumuwa maganizo awo ndi amodzi, choncho adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombocho.+ 14  Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa,+ koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu,+ Mwanawankhosayo adzawagonjetsa.+ Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.”+ 15  Kenako mngeloyo anandiuza kuti: “Madzi amene wawaona aja, pamene hule lija lakhala, akuimira mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero.+ 16  Nyanga 10+ waziona zija, komanso chilombo,+ zimenezi zidzadana nalo hulelo.+ Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto.+ 17  Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake,+ kuti zikwaniritse maganizo awo amodzi, mwa kupereka ufumu wawo kwa chilombo,+ kufikira mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.+ 18  Ndipo mkazi+ amene unamuonayo akuimira mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.