Chivumbulutso 12:1-17

12  Kenako chizindikiro chachikulu+ chinaoneka kumwamba. Ndicho mkazi+ atavala dzuwa, ndipo mwezi unali kunsi kwa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12,  ndipo mkaziyo anali ndi pakati. Iye analira pomva ululu+ chifukwa cha zowawa za pobereka.  Chizindikiro chinanso chinaoneka kumwamba, ndipo ndinaona chinjoka chachikulu+ chofiira, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10, ndipo pamitupo panali zisoti zachifumu 7.  Mchira+ wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi+ zakumwamba n’kuzigwetsera kudziko lapansi.+ Ndipo chinjokacho chinangoimabe pamaso pa mkazi uja,+ amene anali pafupi kubereka,+ kuti akabereka chidye+ mwana wakeyo.  Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.+  Koma mkaziyo anathawira kuchipululu,+ kumene Mulungu anamukonzera malo, kuti akadyetsedwe+ masiku 1,260.+  Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli+ ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo,  koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba.  Choncho chinjokacho+ chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija,+ iye wotchedwa Mdyerekezi+ ndi Satana,+ amene akusocheretsa dziko lonse lapansi+ kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi,+ ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. 10  Ndipo ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti: “Tsopano chipulumutso,+ mphamvu,+ ufumu wa Mulungu wathu,+ ndi ulamuliro wa Khristu+ wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11  Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa,+ ndiponso chifukwa cha mawu a umboni wawo.+ Ndipo iwo sanaone kuti miyoyo yawo ndi yofunika,+ ngakhale pamene anali pa ngozi yoti akhoza kufa. 12  Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!+ Tsoka+ dziko lapansi ndi nyanja,+ chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”+ 13  Tsopano chinjoka chitaona kuti achigwetsera kudziko lapansi,+ chinazunza mkazi+ amene anabereka mwana wamwamuna uja. 14  Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri+ a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu,+ kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa+ kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi njoka ija.+ 15  Kenako njokayo inalavula madzi+ ngati mtsinje kuchokera m’kamwa mwake, kulavulira mkazi uja, kuti amizidwe ndi mtsinjewo.+ 16  Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo.+ Dzikolo linatsegula pakamwa pake ndi kumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera m’kamwa mwake. 17  Ndipo chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja,+ moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene amasunga malamulo a Mulungu, amenenso ali ndi ntchito yochitira umboni+ za Yesu.

Mawu a M'munsi