Chivumbulutso 16:1-21

16  Kenako, ndinamva mawu ofuula+ ochokera m’malo opatulika akuuza angelo 7 aja kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo+ wa Mulunguzo kudziko lapansi.”  Mngelo woyamba+ anapita n’kukathira mbale yake padziko lapansi.+ Pamenepo mliri wa zilonda zopweteka ndi zonyeka+ unagwa pakati pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chilombo,+ amenenso anali kulambira chifaniziro chake.+  Mngelo wachiwiri+ anathira mbale yake m’nyanja.+ Ndipo nyanja inasanduka magazi+ ngati a munthu wakufa, moti chamoyo chilichonse m’nyanjamo chinafa.+  Mngelo wachitatu+ anathira mbale yake pamitsinje+ ndi pa akasupe amadzi, ndipo zonse zinasanduka magazi.+  Ndiye ndinamva mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti: “Inu Amene mulipo ndi amene munalipo,+ inu Wokhulupirika,+ ndinu wolungama chifukwa mwapereka zigamulo zimenezi,+  pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri.+ Ndipo inu mwawapatsa magazi+ kuti amwe, ndipo n’zowayenereradi.”+  Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: “Inde, Yehova Mulungu, inu Wamphamvuyonse,+ zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.”+  Mngelo wachinayi+ anathira mbale yake padzuwa. Ndipo dzuwa linaloledwa kutentha+ anthu ndi moto.  Choncho anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu. Koma iwo ananyoza dzina la Mulungu,+ amene ali ndi ulamuliro+ pa miliri imeneyi, ndipo sanalape kuti amupatse ulemerero.+ 10  Mngelo wachisanu anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo.+ Pamenepo ufumu wake unachita mdima,+ ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. 11  Koma iwo ananyoza+ Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu wawo ndi zilonda zawo, ndipo sanalape ntchito zawo. 12  Mngelo wa 6+ anathira mbale yake pamtsinje waukulu wa Firate,+ ndipo madzi ake anauma,+ kuti njira ya mafumu+ ochokera kotulukira dzuwa ikonzedwe. 13  Kenako ndinaona mauthenga atatu onyansa ouziridwa,+ ooneka ngati achule,+ akutuluka m’kamwa mwa chinjoka,+ m’kamwa mwa chilombo,+ ndi m’kamwa mwa mneneri wonyenga.+ 14  Kwenikweni amenewa ndi mauthenga ouziridwa+ ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro.+ Mauthengawo akupita kwa mafumu+ a dziko lonse lapansi+ kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi kunkhondo+ ya tsiku lalikulu+ la Mulungu Wamphamvuyonse.+ 15  “Taona! Ndikubwera ngati mbala.+ Wodala ndi amene akhalabe maso+ ndi kukhalabe chivalire malaya ake akunja, kuti asayende wosavala anthu n’kuona maliseche ake.”+ 16  Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.*+ 17  Ndiyeno mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya.+ Atatero, kunamveka mawu ofuula+ kuchokera m’malo opatulika, kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Zachitika!” 18  Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, ndipo kunagunda mabingu. Kunachitanso chivomezi chachikulu+ chimene sichinachitikepo chikhalire anthu padziko lapansi,+ chivomezi+ champhamvu kwambiri, chachikulu zedi. 19  Pamenepo mzinda waukulu+ unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu,+ kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu.+ 20  Komanso, chilumba chilichonse chinathawa. Ngakhale mapiri sanapezeke.+ 21  Ndipo matalala aakulu,+ lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungu+ chifukwa cha mliri wa matalalawo,+ pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aramagedo.” M’Chiheberi, mawuwa akutanthauza, “Phiri la Megido.”