Chivumbulutso 5:1-14
5 Kenako, ndinaona mpukutu wolembedwa mkati ndi kunja komwe,+ uli m’dzanja lamanja la Iye wokhala pampando wachifumu.+ Unali womatidwa+ mwamphamvu ndi zidindo 7 zomatira.
2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti: “Ndani ali woyenera kumatula zidindo zimene amatira mpukutuwu ndi kuutsegula?”
3 Koma sipanapezeke ndi mmodzi yemwe, kaya kumwamba, padziko lapansi, kapena pansi pa nthaka, wotha kutsegula mpukutuwo kapena kuyang’anamo ndi kuuwerenga.
4 Choncho ine ndinalira kwambiri chifukwa sipanapezeke wina aliyense woyenera kutsegula mpukutuwo, kapena kuyang’anamo ndi kuuwerenga.+
5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pa nkhondo+ moti iye ndiye woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo ndi kuutsegula.”
6 Kenako ndinaona mwana wa nkhosa+ wooneka ngati wophedwa,+ ataimirira pafupi ndi mpando wachifumu+ uja ndi zamoyo zinayi, ndi pakati pa akulu aja.+ Iye anali ndi nyanga 7, ndi maso 7. Maso amenewo akuimira mizimu 7 ya Mulungu,+ imene yatumizidwa m’dziko lonse lapansi.
7 Iye anapita, ndipo nthawi yomweyo anatenga mpukutu umene unali kudzanja lamanja la Iye wokhala pampando wachifumu.+
8 Atatenga mpukutuwo, zamoyo zinayi ndi akulu 24 aja+ anagwada ndi kuwerama pamaso pa Mwanawankhosa. Aliyense wa iwo anali ndi zeze woimbira+ ndi mbale yagolide yodzaza ndi zofukiza. Zofukizazo+ zikuimira mapemphero+ a oyera.
9 Iwo anali kuimba nyimbo yatsopano,+ yakuti: “Inu ndinu woyenera kutenga mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake zomatira, chifukwa munaphedwa, ndipo ndi magazi anu,+ munagula+ anthu kuti atumikire Mulungu.+ Anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.
10 Ndipo munawasandutsa mafumu+ ndi ansembe+ a Mulungu wathu,+ moti adzakhala mafumu+ olamulira dziko lapansi.”
11 Kenako, ndinaona ndi kumva mawu a angelo ambiri atazungulira mpando wachifumu limodzi ndi zamoyo zija ndi akulu aja. Chiwerengero chawo chinali miyanda kuchulukitsa ndi miyanda*+ ndiponso masauzande kuchulukitsa ndi masauzande.+
12 Iwo anali kunena mofuula kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa+ ndiye woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero, ndi madalitso.”+
13 Ndipo cholengedwa chilichonse chakumwamba, padziko lapansi,+ pansi pa nthaka, panyanja, ndi zinthu zonse za mmenemo, ndinazimva zikunena kuti: “Iye wokhala pampando wachifumu,+ ndi Mwanawankhosa,+ atamandidwe ndiponso alandire ulemu,+ ulemerero,+ ndi mphamvu, kwamuyaya.”
14 Ndiyeno zamoyo zinayi zija zinati: “Ame!” Ndipo akulu aja+ anagwada n’kuwerama ndi kulambira.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “10,000 kuchulukitsa ndi ma 10,000.”