Chivumbulutso 10:1-11

10  Kenako, ndinaona mngelo+ wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba, atavala mtambo.+ Kumutu kwake kunali utawaleza, ndipo nkhope yake inali ngati dzuwa.+ Miyendo yake+ inali ngati mizati yamoto.  M’dzanja lake, anali ndi mpukutu waung’ono wofunyulula. Iye anaponda panyanja ndi phazi lake lamanja, koma ndi phazi lake lamanzere anaponda pamtunda.+  Kenako anafuula ndi mawu okweza ngati kubangula kwa mkango.+ Atafuula choncho, mabingu 7+ analankhula, bingu lililonse ndi liwu lakelake.  Tsopano mabingu 7 aja atalankhula, ndinafuna kulemba. Koma ndinamva mawu kumwamba+ akuti: “Tsekera zimene+ mabingu 7 amenewo alankhula, usazilembe.”  Mngelo amene ndinamuona ataimirira panyanja ndi pamtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba.+  Iye analumbira pa Iye wokhala+ ndi moyo kwamuyaya,+ amene analenga kumwamba ndi zokhala kumeneko, ndi dziko lapansi+ ndi zinthu za mmenemo,+ ndi nyanja ndi zinthu za mmenemo. Analumbira kuti: “Sipakhalanso kuchedwa ayi.+  Koma m’masiku oliza lipenga la mngelo wa 7,+ mngeloyo atatsala pang’ono kuliza lipenga lake,+ ndithu chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu chidzathetsedwa, malinga ndi uthenga wabwino umene anaulengeza kwa akapolo ake, aneneri.”+  Kenako, mawu+ amene ndinawamva kuchokera kumwamba aja, analankhulanso ndi ine kuti: “Pita, katenge mpukutu wofunyulula umene uli m’dzanja la mngelo amene waimirira panyanja ndi pamtunda uja.”+  Choncho, ndinapita kwa mngeloyo n’kumuuza kuti andipatse mpukutu waung’onowo. Iye anandiuza kuti: “Tenga mpukutuwu udye.+ Ukupweteketsa m’mimba, koma m’kamwa mwako ukhala wozuna ngati uchi.” 10  Chotero ndinatenga mpukutu waung’onowo m’dzanja la mngeloyo n’kuudya.+ M’kamwa mwanga, unali wozuna ngati uchi,+ koma nditaudya, unandipweteketsa m’mimba. 11  Ndiye iwo anandiuza kuti: “Uyenera kuneneranso zokhudza mitundu ya anthu, mayiko, zinenero, ndi mafumu ambiri.”+

Mawu a M'munsi