Chivumbulutso 20:1-15
20 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho+ ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.
2 Kenako anagwira chinjoka,+ njoka yakale ija,+ amene ndi Mdyerekezi+ ndiponso Satana,+ ndi kumumanga zaka 1,000.
3 Ndipo anamuponyera m’phompho+ ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.+
4 Kenako ndinaona mipando yachifumu+ ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza.+ Ndiyeno ndinaona miyoyo ya amene anaphedwa ndi nkhwangwa chifukwa cha kuchitira umboni za Yesu, ndi kulankhula za Mulungu. Ndinaonanso anthu amene sanalambire chilombo+ kapena chifaniziro chake,+ ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja pawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu+ limodzi ndi Khristu zaka 1,000.
5 (Akufa+ enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000.)+ Uku ndi kuuka koyamba+ kwa akufa.
6 Wodala+ ndi woyera+ ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri+ ilibe ulamuliro.+ Koma adzakhala ansembe+ a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.+
7 Tsopano zikadzangotha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa m’ndende yake,
8 ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa kunyanja.+
9 Iwo adzayenda n’kufalikira mpaka kumbali zonse za dziko lapansi, kenako adzazungulira msasa wa oyera,+ ndi mzinda wokondedwa.+ Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba ndi kuwapsereza.+
10 Mdyerekezi,+ amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo+ ndi mneneri wonyenga uja.+ Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya.
11 Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo.+ Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa+ pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso.
12 Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka,+ ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo.+ Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+
13 Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa+ amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.+
14 Ndipo imfa+ ndi Manda zinaponyedwa m’nyanja yamoto.+ Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.+
15 Komanso, aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo+ anaponyedwa m’nyanja yamoto.+