Chivumbulutso 15:1-8

15  Ndipo ndinaona chizindikiro china+ kumwamba, chachikulu ndi chodabwitsa. Ndicho angelo 7+ okhala ndi miliri 7.+ Imeneyi ndiyo yomaliza, chifukwa ndiyo ikumalizitsa+ mkwiyo+ wa Mulungu.  Kenako ndinaona chooneka ngati nyanja yagalasi+ yosakanikirana ndi moto. Ndipo amene anagonjetsa+ chilombo chija, chifaniziro chake,+ ndi nambala+ ya dzina lake, ndinawaona ataimirira pambali pa nyanja yagalasiyo,+ ali ndi azeze+ a Mulungu.  Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+  Kodi ndani sadzakuopani,+ inu Yehova?+ Ndani sadzalemekeza dzina lanu?+ Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika.+ Mitundu yonse ya anthu idzabwera kudzalambira pamaso panu,+ chifukwa malamulo anu olungama aonekera.”+  Zimenezi zitatha, ndinaona malo opatulika a m’chihema+ cha umboni+ atatsegulidwa kumwamba.+  Ndipo angelo 7+ okhala ndi miliri 7+ aja anatuluka kumalo opatulikawo, atavala zovala zoyera+ ndi zowala, atavalanso zoteteza pachifuwa zagolide.  Ndiye chimodzi cha zamoyo zinayi+ zija chinapatsa angelo 7 amenewo mbale zagolide 7, zodzaza ndi mkwiyo wa Mulungu,+ amene adzakhala ndi moyo kwamuyaya.+  Ndipo malo opatulikawo anadzaza utsi chifukwa cha ulemerero wa Mulungu,+ ndiponso chifukwa cha mphamvu zake. Palibe amene anatha kulowa m’malo opatulikawo, mpaka miliri 7+ ya angelo 7 aja itatha.

Mawu a M'munsi