Chivumbulutso 22:1-21

22  Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo,+ oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa.+  Mtsinjewo unali kudutsa pakati pa msewu waukulu wa mumzindawo. Kumbali iyi ya mtsinjewo ndi kumbali inayo, kunali mitengo+ ya moyo yobala zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inali kubala zipatso mwezi uliwonse.+ Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu.+  Sikudzakhalanso temberero.+ Koma mpando wachifumu wa Mulungu+ ndi wa Mwanawankhosa+ udzakhala mumzindamo, ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulika+ kwa iye.  Iwo adzaona nkhope yake,+ ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo.+  Komanso, usiku sudzakhalakonso.+ Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwa Yehova Mulungu adzawaunikira.+ Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya.+  Kenako anandiuza kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona.+ Yehova, Mulungu wopereka mauthenga ouziridwa+ a aneneri,+ anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa.+  Ndipo taonani! Ndikubwera mofulumira.+ Wodala ndi aliyense wosunga mawu a ulosi a mumpukutu uwu.”+  Ine Yohane, ndine amene ndinali kumva ndi kuona zinthu zimenezi. Ndipo nditamva ndi kuona, ndinagwada n’kuwerama kuti ndilambire+ pamapazi a mngelo amene anali kundionetsa zinthu zimenezi.  Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ndiwo aneneri,+ ndi wa anthu amene akusunga mawu a mumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.”+ 10  Anandiuzanso kuti: “Usatsekere mawu a ulosi a mumpukutu uwu, pakuti nthawi yoikidwiratu yayandikira.+ 11  Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama,+ ndipo wochita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo.+ Koma wolungama+ achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa.+ 12  “‘Taonani! Ndikubwera mofulumira,+ ndipo mphoto+ ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake.+ 13  Ine ndine Alefa ndi Omega,+ woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto.+ 14  Odala ndiwo amene achapa mikanjo+ yawo, kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo,+ ndiponso kuti akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake.+ 15  Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu,+ amene amachita zamizimu,+ adama,+ opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.’+ 16  “‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu+ ndi mbadwa+ ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’”+ 17  Mzimu+ ndi mkwatibwi+ akunenabe kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!”+ Aliyense wakumva ludzu abwere.+ Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.+ 18  “Ine ndikuchitira umboni kwa aliyense wakumva mawu a ulosi wa mumpukutuwu, kuti: Wina akawonjezera+ pa zimenezi, Mulungu adzamuwonjezera miliri+ yolembedwa mumpukutuwu. 19  Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu a mumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zolembedwa mumpukutuwu, kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso za m’mitengo ya moyo,+ ndipo sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo.+ 20  “Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’”+ “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.” 21  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale ndi oyerawo.+

Mawu a M'munsi