Chivumbulutso 7:1-17

7  Zimenezi zitatha, ndinaona angelo+ anayi ataimirira m’makona anayi a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo zinayi+ za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja, kapena pamtengo uliwonse.+  Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,+ ali ndi chidindo cha Mulungu+ wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu, kwa angelo anayiwo, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja.  Anafuula kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titadinda chidindo+ pamphumi+ za akapolo a Mulungu wathu.”  Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera m’fuko lililonse+ la ana a Isiraeli,+ anadindidwa chidindo:  Mu fuko la Yuda,+ anadindamo anthu 12,000.Mu fuko la Rubeni,+ 12,000.Mu fuko la Gadi,+ 12,000.  Mu fuko la Aseri,+ 12,000.Mu fuko la Nafitali,+ 12,000.Mu fuko la Manase,+ 12,000.  Mu fuko la Simiyoni,+ 12,000.Mu fuko la Levi,+ 12,000.Mu fuko la Isakara,+ 12,000.  Mu fuko la Zebuloni,+ 12,000.Mu fuko la Yosefe,+ 12,000.Ndipo mu fuko la Benjamini,+ anadindamo anthu 12,000.+  Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu,+ limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse,+ fuko lililonse, mtundu uliwonse,+ ndi chinenero chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu+ ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza+ m’manja mwawo. 10  Iwo anapitirizabe kufuula ndi mawu okweza, kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu,+ amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+ 11  Pamenepo angelo+ onse anaimirira mozungulira mpando wachifumu, limodzi ndi akulu,+ ndi zamoyo zinayi zija.+ Ndipo onse anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu.+ 12  Iwo anali kunena kuti: “Ame! Mulungu wathu wanzeru, wamphamvu+ ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemerero ndi ulemu, ndipo ayamikiridwe kwamuyaya. Ame.”+ 13  Ndiyeno mmodzi wa akulu+ aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani, ndipo achokera kuti?” 14  Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anati: “Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu,+ ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa+ m’magazi+ a Mwanawankhosa. 15  N’chifukwa chake ali pamaso+ pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika+ usana ndi usiku m’kachisi wake, ndipo wokhala pampando wachifumuyo+ adzatambasulira hema+ wake pamwamba pawo kuti awateteze. 16  Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17  chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali pa mpando wachifumu, adzawaweta+ ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi+ a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.”+

Mawu a M'munsi