Numeri 8:1-26

8  Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti:  “Lankhula ndi Aroni, unene kuti, ‘Ukayatsa nyale 7 zija, ziziunika malo apatsogolo pa choikapo nyalecho.’”+  Ndipo Aroni anayamba kuchitadi zimenezo. Anayatsa nyalezo kuti ziwalitse malo apatsogolo pa choikapo nyalecho,+ monga mmene Yehova analamulira Mose.  Choikapo nyalecho chinali chooneka motere kapangidwe kake: Chinali chosula, chagolide. Chinasulidwa kuchokera kutsinde lake mpaka kumaluwa ake.+ Anachisula malinga ndi chitsanzo chimene Yehova anaonetsa+ Mose m’masomphenya.  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Tenga Alevi pakati pa ana a Isiraeli, ndipo uwayeretse.+  Kuwayeretsa kwake uchite motere: Uwawaze madzi oyeretsera machimo,+ ndipo iwo amete thupi lonse.+ Komanso achape zovala zawo+ kuti akhale oyera.+  Kenako iwo atenge ng’ombe yaing’ono yamphongo,+ pamodzi ndi nsembe yake yambewu+ ya ufa wosalala wothira mafuta. Iweyo utenge ng’ombe inanso yaing’ono yamphongo ya nsembe yamachimo.+  Ukatero, ubweretse Aleviwo kuchihema chokumanako, ndipo usonkhanitse khamu lonse la ana a Isiraeli.+ 10  Ndiyeno upereke Aleviwo pamaso pa Yehova, ndipo ana a Isiraeliwo aike+ manja awo pa Aleviwo.+ 11  Pamenepo, Aroni auze Aleviwo kuti ayende uku ndi uku pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula*+ ya ana a Isiraeli. Iwo azigwira ntchito yotumikira Yehova.+ 12  “Aleviwo aike manja awo pamitu ya ng’ombe zamphongozo.+ Pambuyo pake, upereke kwa Yehova ng’ombe imodzi monga nsembe yamachimo, ndipo inayo uipereke monga nsembe yopsereza yophimbira machimo+ a Alevi. 13  Uimiritse Aleviwo pamaso pa Aroni ndi ana ake, ndi kuwauza kuti ayende uku ndi uku monga nsembe yoweyula kwa Yehova. 14  Upatule Aleviwo pakati pa ana a Isiraeli kuti akhale anga.+ 15  Pambuyo pake, Aleviwo azitumikira pachihema chokumanako.+ Chotero uwayeretse, ndi kuwauza kuti ayende uku ndi uku monga nsembe yoweyula.+ 16  Amenewa ndi operekedwa. Aperekedwa kwa ine kuchokera pakati pa ana a Isiraeli.+ Ine ndikuwatenga iwowa m’malo mwa onse otsegula mimba ya mayi awo, oyamba kubadwa onse pakati pa ana a Isiraeli.+ 17  Mwana woyamba kubadwa aliyense pakati pa ana a Isiraeli ndi wanga, kaya akhale wa munthu kapena wa nyama.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana woyamba kubadwa aliyense m’dziko la Iguputo+ ndinawapatula kuti akhale anga.+ 18  Choncho m’malo mwa ana oyamba kubadwa onse a Isiraeli, ndikutenga Alevi kuti akhale anga.+ 19  Ndipo ndidzapereka Alevi kwa Aroni ndi ana ake monga operekedwa kuchokera mwa ana a Isiraeli.+ Aleviwo adzatumikira m’malo mwa ana a Isiraeli pachihema chokumanako,+ ndipo aziphimba machimo a ana a Isiraeli.+ Chifukwa cha utumiki wawowo, mliri sudzawagwera ana a Isiraeli pakuti sadzayandikira malo oyerawo.” 20  Choncho Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Isiraeli, anachita zonse zofunikira kwa Alevi. Ana a Isiraeliwo anachitira Aleviwo malinga ndi zonse zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi. 21  Aleviwo anadziyeretsa+ n’kuchapa zovala zawo. Pambuyo pake, Aroni anawauza kuti ayende uku ndi uku monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.+ Kenako Aroniyo anawaphimbira machimo awo kuti awayeretse.+ 22  Ndiyeno Aleviwo analowa n’kukayamba utumiki wawo m’chihema chokumanako, pamaso pa Aroni ndi ana ake.+ Anthu anachitira Aleviwo malinga ndi zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi. 23  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 24  “Lamulo lokhudza Alevi ndi ili: Kuyambira wazaka 25 kupita m’tsogolo azilowa m’gulu la otumikira m’chihema chokumanako. 25  Koma akakwanitsa zaka 50 atuluke m’gululo, ndipo asadzatumikirenso. 26  Iye azingothandizira abale ake m’chihema chokumanako pochita utumiki wawo, koma asatumikire. Umu ndi mmene uzichitira ndi Alevi malinga ndi ntchito zawo.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.