Numeri 19:1-22

19  Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti:  “Nali lamulo limene Yehova wapereka. Iye wati, ‘Lankhulani ndi ana a Isiraeli kuti akupatseni ng’ombe yaikazi yofiira, yathanzi. Ng’ombeyo ikhale yopanda chilema+ yomwe sinamangidwepo m’goli chikhalire.+  Mupereke ng’ombeyo kwa wansembe Eleazara kuti aitsogolere kunja kwa msasa, ndipo kumeneko ikaphedwe pamaso pake.  Kenako, wansembe Eleazara atengeko magazi a ng’ombeyo ndi chala chake, n’kuwawaza maulendo 7 moyang’anizana ndi chihema chokumanako.+  Ndiyeno ng’ombeyo itenthedwe iyeyo akuona. Atenthe chikopa chake, nyama yake, magazi ake, limodzi ndi ndowe zake.+  Wansembeyo atenge mtengo wa mkungudza,+ kamtengo ka hisope+ ndi ulusi wofiira kwambiri,+ aziponye pakati pa moto umene akutenthapo ng’ombeyo.  Akatha, wansembeyo achape zovala zake n’kusamba thupi lake ndi madzi. Pambuyo pake akhoza kulowa mumsasa, koma akhalebe wodetsedwa mpaka madzulo.  “‘Munthu amene atenthe ng’ombeyo achape zovala zake n’kusamba thupi lake ndi madzi,+ koma akhalebe wodetsedwa mpaka madzulo.  “‘Ndiyeno munthu wosadetsedwa awole phulusa+ la ng’ombeyo, akalithire pamalo oyera kunja kwa msasawo. Phulusalo alisunge kuti azilithira m’madzi oyeretsera+ khamu la ana a Isiraeli. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10  Wowola phulusa la ng’ombeyo azichapa zovala zake, koma azikhalabe wodetsedwa mpaka madzulo.+ “‘Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale kwa ana a Isiraeli ndi kwa mlendo wokhala pakati pawo.+ 11  Aliyense wokhudza mtembo wa munthu aliyense,+ nayenso azikhala wodetsedwa masiku 7.+ 12  Munthu woteroyo azidziyeretsa ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu,+ ndipo pa tsiku la 7 azikhala woyera. Koma akapanda kudziyeretsa pa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera pa tsiku la 7. 13  Munthu aliyense wokhudza mtembo, thupi la munthu aliyense amene angamwalire, amene sadzadziyeretsa, adzaipitsa chihema cha Yehova.+ Munthu ameneyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa Isiraeli.+ Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanawazidwe madzi oyeretsera.+ Chidetso chake chikadali pa iye.+ 14  “‘Ngati munthu angafere muhema, nali lamulo lake: Munthu aliyense wolowa muhemamo, ndi aliyense amene ali mmenemo, akhale wodetsedwa masiku 7. 15  Chiwiya+ chilichonse chosavundikira bwino* chikhale chodetsedwa. 16  Aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu amene waphedwa ndi lupanga,+ kapena mtembo uliwonse, kapenanso fupa la munthu,+ ngakhalenso manda a munthu, akhale wodetsedwa masiku 7. 17  Munthu wodetsedwayo am’tapireko phulusa la nsembe yamachimo yotenthedwa ija. Phulusalo aliike m’mbiya n’kuthiramo madzi a kumtsinje. 18  Ndiyeno munthu wosadetsedwa+ atenge kamtengo ka hisope.+ Akaviike m’madziwo n’kuwaza hemalo. Awazenso ziwiya zonse ndi anthu onse amene anali muhemalo. Komanso, awaze munthu amene anakhudza fupa la munthu, kapena kukhudza munthu wophedwa, kapenanso mtembo uliwonse, ngakhalenso manda a munthu. 19  Munthu wosadetsedwayo awaze madziwo munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu, ndi pa tsiku la 7. Ndipo pa tsiku la 7+ limenelo amuyeretse tchimo lake. Kenako amene akuyeretsedwayo achape zovala zake, asambe ndi madzi, ndipo akhale woyera madzulo ake. 20  “‘Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo aphedwe+ kuti asakhalenso pakati pa mpingowo, chifukwa waipitsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera. Choncho ndi wodetsedwa. 21  “‘Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale kwa iwo, kuti munthu wowaza madzi oyeretsera, komanso munthu amene angakhudze madziwo, azichapa zovala zake.+ Akatero, azikhalabe wodetsedwa mpaka madzulo. 22  Chinthu chilichonse chimene munthu wodetsedwayo angakhudze, chikhale chodetsedwa.+ Komanso munthu amene angakhudze chinthucho, akhale wodetsedwa mpaka madzulo.’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni pa mawu akuti “chosavundikira bwino,” ndi akuti “chosamanga chingwe chake.”