Numeri 27:1-23

27  Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri, ndipo Makiri anali mwana wa Manase.+ Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewo mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.+  Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, pamaso pa wansembe Eleazara,+ pamaso pa atsogoleri ndi khamu lonse, pakhomo la chihema chokumanako, n’kunena kuti:  “Bambo athu anafera m’chipululu.+ Koma iwo sanali nawo m’gulu la Kora+ limene linasonkhana kuti litsutsane ndi Yehova. Bambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo,+ ndipo pa nthawiyo analibe mwana aliyense wamwamuna.  Kodi dzina la bambo athu lichotsedwe ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna?+ Chonde, tipatseni cholowa pakati pa abale awo a bambo athu.”+  Pamenepo, Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:  “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo monga cholowa chawo, pakati pa abale a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.+  Ndipo ulankhule kwa ana a Isiraeli kuti: ‘Mwamuna akamwalira wopanda mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi.  Ngati iye analibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene* ake. 10  Ngati analibe azichimwene, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene a bambo ake. 11  Ngati bambo ake analibe azichimwene awo, muzipereka cholowa chake kwa wachibale wake wapafupi wa ku banja lawo,+ ndipo azitenga cholowacho kukhala chake. Ili likhale lamulo kwa ana a Isiraeli mwa chigamulo changa, monga Yehova walamulira Mose.’” 12  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Kwera phiri ili la Abarimu,+ ukaone dziko limene ndidzalipereke kwa ana a Isiraeli.+ 13  Pambuyo poliona dzikolo, udzaikidwa m’manda kuti ukagone ndi makolo ako.+ Ndithudi, iweyo udzaikidwa m’manda mofanana ndi Aroni m’bale wako,+ 14  chifukwa amuna inu munapandukira mawu anga m’chipululu cha Zini, pa nthawi imene khamu lija linakangana nanu.+ Munalephera kundilemekeza+ pa madzi amene anatuluka patsogolo pa khamulo, madzi a Meriba+ ku Kadesi,+ m’chipululu cha Zini.”+ 15  Tsopano Mose anauza Yehova kuti: 16  “Inu Yehova, Mulungu wa miyoyo ya zamoyo+ zamitundu yonse,+ sankhani munthu woti aziyang’anira khamuli.+ 17  Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse,+ kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda m’busa.”+ 18  Chotero Yehova anauza Mose kuti: “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu wolimba mtima,*+ ndipo uike manja ako pa iye.+ 19  Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara, ndi pamaso pa khamu lonse, ndipo umuike kukhala mtsogoleri pamaso pawo.+ 20  Um’patseko ulemerero wako,+ kuti khamu lonse la ana a Isiraeli lizimumvera.+ 21  Yoswayo aziimirira pamaso pa wansembe Eleazara, ndipo Eleazara azifunsira+ chigamulo cha Yehova m’malo mwa Yoswayo pogwiritsa ntchito maere a Urimu.+ Yoswa akalamula, ana onse a Isiraeli ndi khamu lonse azituluka naye, ndipo akalamulanso, onsewo azibwerako limodzi naye.” 22  Mose anachitadi monga mmene Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa n’kumuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara,+ ndi pamaso pa khamu lonselo. 23  Kenako anaika manja ake pa iye n’kumuika kukhala mtsogoleri+ monga Yehova ananenera kudzera kwa Moseyo.+

Mawu a M'munsi

“Azichimwene” akutanthauza abale a munthu aamuna, obadwa kwa mayi ndi bambo mmodzi.
Mawu ake enieni, “munthu amene mwa iye muli mzimu.”