Numeri 30:1-16

30  Ndiyeno Mose analankhula ndi atsogoleri+ a mafuko a ana a Isiraeli, kuti: “Tamverani zimene Yehova walamula:  Munthu akalonjeza+ kwa Yehova, kapena akachita lumbiro lodzimana,+ asalephere kukwaniritsa mawu ake.+ Achite malinga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake.+  “Mtsikana amene akanali m’nyumba ya bambo ake akalonjeza zinazake kwa Yehova,+ kapena akachita lonjezo lodzimana,  bambo ake n’kumumva ndithu akulonjeza kapena akuchita lonjezo lodzimanalo,+ koma osanenapo kanthu, malonjezo ake onsewo akhale momwemo. Zikatero, lonjezo lake lililonse lodzimana likhale momwemo.  Koma ngati bambo ake am’kaniza pa tsiku limene amva malonjezo ake onse, malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, akhale opanda ntchito. Yehova adzam’khululukira chifukwa bambo ake anam’kaniza.+  “Koma ngati mkaziyo ali wokwatiwa, ndipo akuchita lonjezo mwa kulumbirira moyo wake,+ kapena kulonjeza ndi pakamwa pake mosaganizira bwino,  mwamuna wake n’kumva koma osanena kanthu kwa iye pa tsiku limene wamva mawu a lonjezolo, malonjezo ake a kudzimana amene walumbirira moyo wake akhale momwemo.+  Mwamunayo akam’kaniza pa tsiku limene wamva kulonjezako,+ ndiye kuti wafafaniza lonjezo la mkaziyo, kapena lonjezo lake limene anachita mosaganizira bwino, limene analumbirira moyo wake ndi pakamwa pake. Yehova adzam’khululukira mkaziyo.+  “Koma mkazi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akachita lonjezo, lonjezo lililonse limene walumbirira moyo wake likhale momwemo. 10  “Komabe, ngati mkazi walonjeza ali m’nyumba ya mwamuna wake, kapena ngati wachita lonjezo lodzimana+ mwa kulumbirira moyo wake, 11  mwamuna wake n’kumva koma osanenapo kanthu, osam’kaniza, malonjezo ake onse akhale momwemo, ndipo lonjezo lililonse lodzimana limene walumbirira moyo wake likhale momwemo. 12  Koma mwamuna wake akafafaniza malonjezowo pa tsiku limene wamva mawu alionse otuluka pakamwa pa mkaziyo, mawu olonjezerawo kapena malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, malonjezo a mkaziyo akhale opanda ntchito.+ Mwamuna wake wawafafaniza, ndipo Yehova adzam’khululukira mkaziyo.+ 13  Mwamuna wake ali ndi mphamvu zokhazikitsa kapena kufafaniza lonjezo lililonse la mkazi wake, kapenanso lumbiro la mkaziyo lodzimana, losautsa moyo wake.+ 14  Koma ngati mwamunayo sananenepo kanthu kwa mkazi wake, masiku n’kumapita, ndiye kuti mwamunayo wakhazikitsa malonjezo onse a mkaziyo, kapena malonjezo onse odzimana amene mkaziyo walumbirira moyo wake.+ Iye wawakhazikitsa chifukwa sananenepo kanthu kwa mkaziyo pa tsiku limene anamumva akulonjeza. 15  Ndipo ngati mwamunayo afafaniza malonjezowo patapita nthawi pambuyo poti wawamva kale, cholakwa chizikhala pa iyeyo m’malo mwa mkazi wake.+ 16  “Awa ndiwo malangizo amene Yehova anapatsa Mose okhudza mwamuna ndi mkazi wake,+ ndiponso bambo ndi mwana wake wachitsikana amene akukhalabe m’nyumba mwake.”+

Mawu a M'munsi