Numeri 5:1-31

5  Popitiriza kulankhula ndi Mose, Yehova anati:  “Lamula ana a Isiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche,+ ndi aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu.+  Kaya akhale mwamuna kapena mkazi, uziwatulutsa kunja kwa msasa+ kuti asadetse+ misasa ya anthu amene ine ndikukhala pakati pawo.”+  Ana a Isiraeli anali kuchitadi zimenezo. Anali kutulutsadi anthuwo kunja kwa msasa, monga mmene Yehova anauzira Mose.  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Lankhula kwa ana a Isiraeli kuti, ‘Mwamuna kapena mkazi akachita machimo alionse amene anthu amachita, kuchimwira Yehova, iyenso azikhala ndi mlandu.+  Munthuyo aziulula+ tchimo lake limene wachita. Azipereka malipiro onse a mlandu wake, komanso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu a malipirowo.+ Azipereka malipirowo kwa munthu amene wam’lakwira.  Koma ngati wolakwiridwayo wamwalira wopanda wachibale wake weniweni, amene angalandire malipiro a mlanduwo, malipirowo aperekedwe kwa Yehova kuti akhale a wansembe. Wochimwayo aziperekanso nkhosa yamphongo yoti wansembeyo am’phimbire machimo ake.+  “‘Zopereka zonse+ za zinthu zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli azipereka kwa wansembe, zizikhala zake.+ 10  Zinthu zopatulika zimene munthu aliyense azipereka, zizikhala za wansembe. Chilichonse chimene munthu angapereke kwa wansembe, chimenecho chizikhala chake.’” 11  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Mkazi wa munthu angazembere mwamuna wake n’kumuchimwira+ 13  mwakuti mwamuna wina wagona* naye,+ koma zimenezi n’kukhala zobisika kwa mwamuna wake.+ Ngakhale kuti mkaziyo wadziipitsa ndithu, zingachitike kuti palibe munthu amene angapereke umboni wotsimikizira kuti mkaziyo walakwadi ndipo iye sanagwidwe. 14  Koma mwamuna wake akhoza kukhala ndi nsanje+ mumtima mwake, n’kumaganiza kuti mkaziyo sanayende bwino, pamene mkaziyo wadziipitsadi. Kapena mwamuna akhoza kukhala ndi nsanje mumtima mwake n’kumaganiza kuti mkazi wake sanayende bwino, pamene mkaziyo sanadziipitse. 15  Mulimonsemo, mwamunayo azitenga mkaziyo n’kupita naye kwa wansembe.+ Azipita ndi nsembe ya mkaziyo ya ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo asamauthire mafuta kapena lubani,*+ chifukwa ndi nsembe yambewu yansanje, nsembe yambewu yachikumbutso, yokumbutsa cholakwa. 16  “‘Wansembeyo azitenga mkaziyo n’kumuimiritsa pamaso pa Yehova.+ 17  Wansembeyo azitenga madzi opatulika m’chiwiya chadothi. Azitengakonso fumbi lapansi m’chihema chopatulika, n’kulithira m’madziwo. 18  Ndiyeno wansembeyo aziimiritsa mkaziyo pamaso pa Yehova n’kumumasula chovala cha kumutu kwake. Kenako, azitenga nsembe yambewu yachikumbutso, yomwe ndi nsembe yambewu yansanje,+ n’kuiika m’manja mwa mkaziyo. Wansembeyo azitenga m’dzanja lake madzi owawa obweretsa temberero.+ 19  “‘Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo, pomuuza kuti: “Ngati mwamuna aliyense sanagone nawe, ndipo ngati sunam’zembere mwamuna wako pamene uli m’manja mwake,+ n’kuchita chodetsa chilichonse, madzi owawa obweretsa tembererowa asakuvulaze. 20  Koma ngati unazembera mwamuna wako pamene uli m’manja mwake,+ mwa kudziipitsa, mwakuti mwamuna wina wagona nawe,*+ . . . ” 21  Tsopano wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo ndi lumbiro la temberero.+ Iye aziti kwa mkaziyo: “Yehova akuike kukhala chitsanzo cha temberero ndi lumbiroli pakati pa anthu amtundu wako. Yehova achite zimenezo mwa kufotetsa ntchafu*+ yako, ndi kutupitsa mimba yako. 22  Madzi a tembererowa alowe m’matumbo mwako kuti akatupitse mimba yako ndi kufotetsa ntchafu yako.” Ndipo mkaziyo aziyankha kuti: “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”* 23  “‘Wansembeyo azilemba matemberero amenewa m’buku+ ndi kuwafafaniza+ m’madzi owawa aja. 24  Azimwetsa mkaziyo madzi owawa a tembererowo,+ ndipo madziwo akalowa m’thupi mwake, mkaziyo azimva ululu. 25  Ndiyeno wansembeyo azitenga nsembe yambewu+ yansanje imene ili m’manja mwa mkaziyo, ndi kuiweyulira uku ndi uku pamaso pa Yehova. Akatero, aziibweretsa pafupi ndi guwa lansembe. 26  Wansembeyo azitapako nsembe yambewuyo monga chikumbutso,+ n’kuifukiza paguwa lansembe. Pambuyo pake, azipatsa mkaziyo madziwo kuti amwe. 27  Akam’mwetsa madziwo, ngati iye anadzidetsa mwa kugona ndi mwamuna wina,+ madzi a tembererowo akalowa m’thupi mwake, azikhala chinthu chowawa. Pamenepo mimba yake izitupa, ndipo ntchafu yake izifota. Mkaziyo azikhala chitsanzo cha wotembereredwa pakati pa anthu amtundu wake.+ 28  Koma ngati mkaziyo ali woyera chifukwa sanadziipitse, chilangocho chisam’gwere,+ ndipo azitha kutenga pakati. 29  “‘Limeneli ndilo lamulo la nkhani ya nsanje,+ pamene mkazi wazembera mwamuna wake,+ n’kudziipitsa pamene ali m’manja mwake,+ 30  kapena pamene mwamuna wakhala ndi nsanje mumtima mwake, ndipo akuganiza kuti mkazi wake sanayende bwino. Zikatero, mwamunayo aziimiritsa mkazi wake pamaso pa Yehova, ndipo wansembe azichita zonse zofunika pa mkaziyo malinga ndi lamulo limeneli. 31  Mwamunayo adzakhala wopanda cholakwa, koma mkaziyo adzalandira chilango cha kulakwa kwake.’”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “tulutsa umuna.”
“Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi muyezo wokwana pafupifupi kilogalamu imodzi.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Nu 5:13.
Mawu akuti “ntchafu,” mwina akuimira maliseche.
Kapena kuti “Ame! Ame!” m’Chiheberi.