Numeri 17:1-13

17  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti:  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo utenge ndodo+ ya fuko lililonse kwa mtsogoleri+ wa fukolo. Zikhalepo ndodo 12. Pandodo iliyonse ulembepo dzina la mtsogoleri wa fukolo.  Pandodo ya fuko la Levi ulembepo dzina la Aroni. Pakuti mtsogoleri aliyense ali ndi ndodo ya fuko lawo.  Ndodozo uziike m’chihema chokumanako, patsogolo pa Umboni,+ pamene ndimakumana nawe nthawi zonse.+  Chimene chichitike n’chakuti, munthu amene ndimusankheyo,+ ndodo yake idzaphuka, ndipo ndidzathetseratu kudandaula+ kwa ana a Isiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine, pamene akudandaula motsutsana nawe.”+  Choncho, Mose analankhula ndi ana a Isiraeli. Aliyense wa atsogoleri awo anapereka ndodo+ yake, malinga ndi fuko lawo. Zinalipo ndodo 12, ndipo imodzi ya ndodozo+ inali ya Aroni.  Ndiyeno Mose anakaika ndodozo pamaso pa Yehova m’chihema cha Umboni.+  Tsiku lotsatira, Mose atalowa m’chihema cha Umbonicho, anangoona kuti ndodo ya Aroni ya nyumba ya Levi inali itaphuka. Ndodoyo inali itaphuka ndipo inali kumasula maluwa ndi kubala zipatso za amondi zakupsa.  Tsopano Mose anachotsa ndodo zonse pamaso pa Yehova n’kupita nazo kwa ana a Isiraeli onse. Amuna aja anayang’ana ndodozo, ndipo aliyense anatengapo yake. 10  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Bwezera ndodo+ ya Aroni patsogolo pa Umboni. Uisunge kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana a chipandukowa,+ n’cholinga chakuti aleke kudandaula motsutsana ndi ine, kuti angafe.” 11  Nthawi yomweyo, Mose anachita monga momwe Yehova anamulamulira. Anachitadi momwemo. 12  Tsopano ana a Isiraeli anayamba kuuza Mose kuti: “Tsopano ife tifa ndithu! Ndithudi titha ife! Tonse titha basi.+ 13  Aliyense amene ayandikire+ chihema cha Yehova, afa!+ Koma zoona ife tithe mwa njira imeneyi?”+

Mawu a M'munsi