Numeri 20:1-29

20  Tsopano khamu lonse la ana a Isiraeli linafika m’chipululu cha Zini,+ m’mwezi woyamba, ndipo anthuwo anakhala ku Kadesi.+ Kumeneko n’kumene Miriamu+ anafera n’kuikidwa m’manda.  Koma anthuwo anasowa madzi pamalopo, ndipo khamu+ lonselo linasonkhana n’kuukira Mose ndi Aroni.+  Pamenepo anthuwo anayamba kukangana+ ndi Mose, kuti: “Zikanakhala bwino tikanangofera limodzi ndi abale athu amene anafa pamaso pa Yehova aja.+  N’chifukwa chiyani anthu inu mwafikitsa mpingo wa Yehova kuchipululu chino, kuti ife limodzi ndi ziweto zathu tifere kuno?+  N’chifukwa chiyani munatitulutsa m’dziko la Iguputo kutibweretsa kumalo oipa ano?+ Malo anji osamera mbewu iliyonse? Mitengo ya nkhuyu kulibe kuno, ngakhale mitengo ya mpesa, kapena mitengo ya makangaza.+ Ndi madzi akumwa omwe kulibe!”  Pamenepo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa mpingowo n’kupita kukhomo la chihema chokumanako. Kumeneko, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi,+ ndipo ulemerero wa Yehova unayamba kuonekera kwa iwo.+  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti:  “Tenga ndodoyo,+ ndipo iwe ndi m’bale wako Aroni, musonkhanitse khamu lonse la anthuwo. Muuze thanthwe pamaso pawo kuti litulutse madzi. Utulutse madzi m’thanthweli kuti upatse khamulo, kuti limwe limodzi ndi ziweto zawo.”+  Choncho Mose anatenga ndodo ija pamaso pa Yehova,+ monga mmene anamulamulira. 10  Kenako, Mose ndi Aroni anasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi patsogolo pa thanthwelo, ndipo Mose anawauza kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu!+ Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?”+ 11  Mose atatero, anakweza dzanja lake n’kumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake. Pamenepo madzi ambiri anayamba kutuluka, ndipo khamu lonselo linayamba kumwa madziwo limodzi ndi ziweto zawo.+ 12  Pambuyo pake Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Chifukwa simunasonyeze chikhulupiriro mwa ine, polephera kundilemekeza+ pamaso pa ana a Isiraeli, simudzaulowetsa mpingowu m’dziko limene ndidzawapatse.”+ 13  Madzi amenewo anatchedwa madzi a ku Meriba,*+ chifukwa pamalopo ana a Isiraeli anakanganapo ndi Yehova, ndipo iye anakwezeka pakati pawo. 14  Tsiku lina Mose anatumiza amithenga kuchokera ku Kadesi kumene iwo anali, kupita kwa mfumu ya Edomu,+ kukanena kuti: “Abale anu Aisiraeli+ akuti, ‘Inu mukudziwa bwino za mavuto onse amene ationekera ife.+ 15  Paja kale makolo athu anapita ku Iguputo,+ ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri.+ Aiguputowo anatizunza ife ndi makolo athu.+ 16  Potsirizira pake, tinalirira Yehova.+ Iye anamva kulira kwathu, ndipo anatitumizira mngelo+ n’kutitulutsa m’dziko la Iguputo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m’malire a dziko lanu. 17  Chonde mutilole tidzere m’dziko lanu. Sitidzera m’munda wanu uliwonse, kapena m’munda wa mpesa uliwonse. Sitimwa madzi a pachitsime chanu chilichonse. Tizingoyenda+ mumsewu wa mfumu, osapatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ mpaka titadutsa m’dziko lanu.’” 18  Koma mfumu ya Edomu inawayankha kuti: “Musadzere m’dziko langa, chifukwa ndingatuluke ndi lupanga kudzakuthirani nkhondo.” 19  Ana a Isiraeliwo anayankha kuti: “Ife tidzangodutsa mumsewu waukulu, ndipo ngati tidzamwa madzi anu, ife kapena ziweto zathu, ndithu tidzalipira mtengo wake.+ Sitikufuna chilichonse ayi, koma kungodutsa m’dziko lanu basi.”+ 20  Koma iye anakanabe, kuti: “Ayi, musadzere+ m’dziko langa.” Mfumu ya Edomu+ itanena zimenezi, inatuluka ndi chikhamu cha anthu, ndi gulu la asilikali lamphamvu, kuti akawathire nkhondo. 21  Choncho mfumu ya Edomu inakana kulola Aisiraeli kudzera m’dziko lake.+ Motero, Aisiraeli analambalala dziko la Edomu.+ 22  Kenako khamu lonse la ana a Isiraeli linanyamuka ku Kadesi+ kuja n’kukafika kuphiri la Hora.+ 23  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni m’phiri la Hora, m’malire a dziko la Edomu, kuti: 24  “Aroni aikidwe m’manda, agone ndi makolo ake,+ pakuti sadzalowa m’dziko limene ndidzapatse ana a Isiraeli. Izi zili choncho chifukwa amuna inu munapandukira malangizo anga okhudza madzi a ku Meriba.+ 25  Utenge Aroni ndi mwana wake Eleazara n’kukwera nawo phiri la Hora. 26  M’phirimo, ukamuvule Aroni zovala zake zaunsembe,+ n’kuveka mwana wake Eleazara.+ Aroni akamwalira kumeneko n’kugona ndi makolo ake.”+ 27  Choncho Mose anachitadi zimene Yehova anamulamula. Pamaso pa khamu lonselo, iwo anakwera m’phiri la Hora. 28  Kumeneko, Mose anavula Aroni zovala zake zaunsembe n’kuveka mwana wake Eleazara. Pambuyo pake, Aroni anamwalira pamwamba pa phiripo.+ Potsirizira pake, Mose ndi Eleazara anatsika m’phirimo. 29  Tsopano khamu lonse la anthuwo litaona kuti Aroni wamwalira, nyumba yonse ya Isiraeli inalira maliro a Aroni masiku 30.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Meriba” limatanthauza “Kukangana; Kutsutsana; Kulimbana.”