Numeri 33:1-56

33  Tsopano nawa malo amene ana a Isiraeli anaima pa ulendo wawo, atatuluka mu Iguputo+ m’magulu awo+ motsogoleredwa ndi Mose ndi Aroni.+  Molamulidwa ndi Yehova, Mose anali kulemba malo onyamukira ulendo uliwonse. Maulendowo, kuchokera kumalo ena kukafika kumalo ena, anali awa: +  Ananyamuka ku Ramese+ m’mwezi woyamba,+ pa tsiku la 15. Pasika anali atachitika dzulo lake,+ pamene ana a Isiraeli ananyamuka molimba mtima* pamaso pa Aiguputo onse.+  Pa nthawiyi n’kuti Aiguputo ali pa ntchito yoika m’manda ana onse oyamba kubadwa,+ amene Yehova anawapha pakati pawo. Yehovayo anali atapereka ziweruzo pamilungu yawo.+  Chotero ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ n’kukamanga msasa ku Sukoti.+  Atanyamuka ku Sukoti anakamanga msasa ku Etamu,+ pafupi ndi chipululu.  Atanyamuka ku Etamu anabwerera m’mbuyo kulowera ku Pihahiroti.+ Pihahiroti anali moyang’anana ndi Baala-zefoni.+ Ndipo anakamanga msasa pafupi ndi Migidoli.+  Pambuyo pake ananyamuka ku Pihahiroti, n’kukadutsa panyanja+ kuwolokera kuchipululu.+ Anayendabe ulendo wa masiku atatu m’chipululu cha Etamu,+ n’kukamanga msasa ku Mara.+  Kenako ananyamuka ku Mara n’kukafika ku Elimu.+ Ku Elimuko anapezako akasupe 12 a madzi, ndi mitengo 70 ya kanjedza, ndipo anamanga msasa kumeneko. 10  Atanyamuka ku Elimu anakamanga msasa ku Nyanja Yofiira. 11  Atanyamuka ku Nyanja Yofiira anakamanga msasa m’chipululu cha Sini.+ 12  Kenako ananyamuka m’chipululu cha Sini, n’kukamanga msasa ku Dofika. 13  Atanyamuka ku Dofika anakamanga msasa ku Alusi. 14  Atanyamuka ku Alusi anakamanga msasa ku Refidimu.+ Kumeneko kunalibe madzi oti anthu amwe. 15  Atanyamuka ku Refidimu anakamanga msasa m’chipululu cha Sinai.+ 16  Pambuyo pake ananyamuka m’chipululu cha Sinai, n’kukamanga msasa ku Kibiroti-hatava.+ 17  Atanyamuka ku Kibiroti-hatava, anakamanga msasa ku Hazeroti.+ 18  Pambuyo pake ananyamuka ku Hazeroti, n’kukamanga msasa ku Ritima. 19  Atanyamuka ku Ritima anakamanga msasa ku Rimoni-perezi. 20  Atanyamuka ku Rimoni-perezi anakamanga msasa ku Libina. 21  Pambuyo pake ananyamukanso ku Libina, n’kukamanga msasa ku Risa. 22  Kenako ananyamuka ku Risa n’kukamanga msasa ku Kehelata. 23  Atanyamuka ku Kehelata anakamanga msasa kuphiri la Saferi. 24  Pambuyo pake ananyamukanso kuphiri la Saferi, n’kukamanga msasa+ ku Harada. 25  Atanyamuka ku Harada anakamanga msasa ku Makeloti. 26  Atanyamuka+ ku Makeloti anakamanga msasa ku Tahati. 27  Atanyamuka ku Tahati anakamanga msasa ku Tera. 28  Kenako ananyamukanso ku Tera n’kukamanga msasa ku Mitika. 29  Atanyamuka ku Mitika anakamanga msasa ku Hasimona. 30  Atanyamuka ku Hasimona anakamanga msasa ku Mosera. 31  Kenako ananyamukanso ku Mosera n’kukamanga msasa ku Bene-yaakana.+ 32  Atanyamuka ku Bene-yaakana anakamanga msasa ku Hori-hagidigadi. 33  Atanyamuka ku Hori-hagidigadi anakamanga msasa ku Yotibata.+ 34  Pambuyo pake ananyamukanso ku Yotibata n’kukamanga msasa ku Abirona. 35  Kenako ananyamuka ku Abirona n’kukamanga msasa ku Ezioni-geberi.+ 36  Atanyamuka ku Ezioni-geberi anakamanga msasa m’chipululu cha Zini,+ ku Kadesi. 37  Pambuyo pake ananyamuka ku Kadesi, n’kukamanga msasa kuphiri la Hora,+ kumalire ndi dziko la Edomu. 38  Wansembe Aroni anakwera m’phiri la Hora monga mmene Yehova anamulamulira, ndipo anamwalira ali m’phirimo. Anamwalira m’chaka cha 40 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi wachisanu, pa tsiku loyamba la mweziwo.+ 39  Aroni anamwalira m’phiri la Hora ali ndi zaka 123. 40  Tsopano mfumu ina yachikanani, mfumu ya Aradi,+ imene inali kukhala ku Negebu+ m’dziko la kanani, inamva kuti ana a Isiraeli akubwera. 41  Patapita nthawi, Aisiraeliwo ananyamuka kuphiri la Hora,+ n’kukamanga msasa ku Tsalimona. 42  Pambuyo pake ananyamuka ku Tsalimona, n’kukamanga msasa ku Punoni. 43  Kenako ananyamukanso ku Punoni n’kukamanga msasa ku Oboti.+ 44  Atanyamuka ku Oboti anakamanga msasa ku Iye-abarimu,* kumalire ndi Mowabu.+ 45  Atanyamuka ku Iyimu anakamanga msasa ku Diboni-gadi.+ 46  Atanyamuka ku Diboni-gadi, anakamanga msasa ku Alimoni-dibilataimu. 47  Kenako ananyamukanso ku Alimoni-dibilataimu,+ n’kukamanga msasa kumapiri a Abarimu,+ pafupi ndi Nebo.+ 48  Potsirizira pake ananyamuka kumapiri a Abarimu n’kukamanga msasa ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+ 49  Anakhalabe mumsasa wawo pafupi ndi Yorodano, kuyambira ku Beti-yesimoti+ mpaka ku Abele-sitimu,+ m’chipululu cha Mowabu. 50  Ndipo Yehova analankhula ndi Mose ku Yeriko, pafupi ndi Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+ Anamuuza kuti: 51  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Tsopano muwoloka Yorodano kuti mulowe m’dziko la Kanani.+ 52  Mukapitikitse anthu onse a m’dzikolo, ndipo mukawononge zifaniziro zawo zonse zamiyala,+ ndi mafano awo onse achitsulo.+ Mukawonongenso malo awo onse opatulika olambirira.+ 53  Mukalande dzikolo n’kukhalamo, chifukwa ndidzalipereka ndithu kwa inu kuti likhale lanu.+ 54  Mukagawire dzikolo kwa mabanja anu monga cholowa chanu mwa kuchita maere.+ Banja la anthu ambiri mukaliwonjezere cholowa chawo, ndipo banja la anthu ochepa mukalichepetsere cholowa chawo.+ Malo alionse amene maere akagwere banja, akapatsidwe kwa banjalo.+ Mukagawane malowo potsata mafuko a makolo anu.+ 55  “‘Koma ngati simukawapitikitsa anthu onsewo,+ ndithu amene mukasiyewo adzakhala ngati zitsotso m’maso mwanu, ndiponso ngati minga yokulasani m’nthiti mwanu. Ndithu adzakusautsani m’dziko limene mudzakhalamo.+ 56  Zikadzatero, zimene ndinafuna kuchita kwa anthuwo ndidzachita kwa inu.’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “dzanja lokwezeka.”
Dzina lakuti “Iye-abarimu” lalembedwa mwachidule kuti “Iyimu” m’vesi 45.