Numeri 23:1-30

23  Tsopano Balamu anauza Balaki kuti: “Mundimangire pamalo ano maguwa ansembe+ okwanira 7. Mukatero mundikonzere ng’ombe zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.”  Nthawi yomweyo Balaki anachita monga momwe anamuuzira Balamu. Kenako, Balaki ndi Balamu anapereka nsembe. Anapereka ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+  Ndiyeno Balamu anauza Balaki kuti: “Muime pafupi ndi nsembe yanu yopsereza.+ Mundilole ine ndichoke, kuti mwina Yehova akumana nane n’kundilankhula.+ Akatero, zimene andiuzezo n’zimenenso ndinene kwa inu.” Chotero Balamu anapita pamwamba pa phiri.  Mulungu atam’peza Balamu,+ iye anamuuza Mulunguyo kuti: “Ndamanga maguwa ansembe 7 m’mizere, ndipo ndapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.”+  Pamenepo Yehova anamuika Balamu+ mawu m’kamwa, n’kumuuza kuti: “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze mawu amenewa.”+  Iye atabwerera kwa Balaki, anapeza Balakiyo limodzi ndi akalonga onse a ku Mowabu ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza.  Pamenepo Balamu anayamba kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti:“Balaki mfumu ya Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu,+Kuchokera kumapiri a kum’mawa, kuti:‘Bwera, udzanditembererere Yakobo.Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+   Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere?+Anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka, ndingathe bwanji kuwaitanira tsoka?+   Pakuti pomwe ndili pano ndikutha kuwaona, pamwamba pa matanthwe pano,Ndikuwaona ndithu, pano pamwamba pa mapiri.Akukhala paokhaokha m’mahema awo,+Iwo akudziona kuti ndi osiyana ndi mitundu ina.+ 10  Ndani watha kuwerenga mtundu wa Yakobo,+ wochuluka ngati fumbi,Ndipo ndani watha kuwerenga gawo limodzi mwa magawo anayi a Isiraeli?Moyo wanga ufe imfa ya olungama,+Ndipo mathero anga akhale ngati awo.”+ 11  Balaki atamva zimenezi anafunsa Balamu kuti: “N’chiyani mwandichitachi? Ndinakutengani kuti mudzatemberere adani anga, koma inu mwawadalitsa kwambiri.”+ 12  Koma iye anamuyankha kuti: “Kodi chilichonse chimene Yehova wandiika m’kamwa, si chimene ndinayenera kunena?”+ 13  Ndiyeno Balaki anauza Balamu kuti: “Tabwerani chonde, tiyeni tipite kumalo ena kumene mungathe kuwaona anthuwo. Simukaona onse, koma mukangoona okhawo amene ali chakufupi.+ Mukanditembererere amenewo.”+ 14  Chotero anamutengera ku Zofimu, pamwamba pa phiri la Pisiga.+ Kumeneko anamanga maguwa ansembe 7, n’kupereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 15  Pambuyo pake, Balamu anauza Balaki kuti: “Muime pano, pafupi ndi nsembe yanu yopserezayi koma ine mundilole ndichoke ndikalankhule ndi Mulungu uko.” 16  Kumeneko Yehova analankhuladi ndi Balamu, n’kumuika mawu m’kamwa, ndipo anamuuza kuti:+ “Bwerera kwa Balaki+ ukamuuze zimenezi.” 17  Balamu atabwerera kwa Balaki, anam’peza ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza, akalonga a ku Mowabu ali naye limodzi pamenepo. Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi Yehova wati chiyani?” 18  Pamenepo Balamu anayambanso kulankhula mwa ndakatulo, kuti:+“Nyamuka, Balaki iwe, tamvera.Tchera khutu kwa ine, iwe mwana wa Zipori.+ 19  Mulungu si munthu, woti anganene mabodza,+Si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu.+Kodi ananenapo kanthu koma osachita,Analankhulapo kanthu kodi koma osakwaniritsa?+ 20  Inetu ndalamulidwa kudzadalitsa,Ndipo Iye wadalitsa,+ ine sindisintha zimenezo.+ 21  Iye sanaone mphamvu yamatsenga+ iliyonse ikuchita kanthu pa Yakobo,Ndipo sanaone Isiraeli akuponyeredwa vuto.Mulungu wake Yehova ali naye,+Ndipo mfuu yotamanda mfumu ikumveka pakati pake. 22  Mulungu wawatulutsa ku Iguputo.+Akuwayendetsa mwa liwiro la ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+ 23  Palibe amene walodza Yakobo,+Ngakhale kuchesa Isiraeli.+Za Yakobo ndi Isiraeli, adzati,‘Mwaonatu zimene Mulungu wachita!’+ 24  Taonani, mtundu udzadzuka ngati mkango,Udzanyamuka monga mkango.+Sugona pansi mpaka ugwire nyama,Ndipo udzamwa magazi a ophedwawo.”+ 25  Tsopano Balaki anauza Balamu kuti: “Ngati mwalephera kuwatemberera ngakhale pang’ono pokha, ndiye musawadalitsenso m’pang’ono pomwe.” 26  Pamenepo Balamu anafunsa Balaki kuti: “Kodi sindinanene kwa inu kuti, ‘Ndichita zokhazo zimene Yehova andiuze’?”+ 27  Koma Balaki anauza Balamu kuti: “Chonde tabwerani. Tiyeni tipite kumalo enanso. Mwina kumeneko Mulungu woona angalole kuti munditembererere anthuwa.”+ 28  Balaki atatero, anatengera Balamu pamwamba pa phiri la Peori, loyang’ana ku Yesimoni.+ 29  Kumeneko Balamu+ anauza Balaki kuti: “Mundimangire pamalo ano maguwa ansembe 7, ndipo mundikonzere ng’ombe zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.”+ 30  Chotero Balaki anachita monga momwe Balamu ananenera. Anapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+

Mawu a M'munsi

Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.