Numeri 4:1-49

4  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti:  “Muwerenge ana onse a Kohati+ mwa ana a Levi, malinga ndi mabanja a nyumba za makolo awo.  Muwerenge kuyambira azaka 30+ mpaka 50,+ onse olowa m’gulu la ogwira ntchito+ m’chihema chokumanako.  “Nawu utumiki wa ana a Kohati m’chihema chokumanako,+ utumiki wopatulika koposa:  Pamene msasa ukusamuka, Aroni ndi ana ake azilowa m’chihema. Mmenemo, azichotsa nsalu yotchinga+ n’kuphimba nayo likasa+ la umboni.  Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu,*+ n’kuyalanso nsalu yabuluu pamwamba pake. Kenako azibwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+  “Iwo aziyala nsalu yabuluu patebulo+ la mkate wachionetsero, n’kuikapo mbale,+ zikho, mbale zolowa,+ ndi mitsuko ya nsembe yachakumwa. Mkate wachionetsero womwe ndi nsembe ya nthawi zonse+ uzikhalabe pomwepo.  Akatero, aziziphimba ndi nsalu yowomba ndi ulusi wofiira kwambiri,+ ndiponso aziphimba tebulolo ndi zikopa za akatumbu.+ Kenako azibwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+  Ndiyeno azitenga nsalu yabuluu n’kuphimbira choikapo nyale,+ pamodzi ndi nyale zake,+ zopanira zake zozimitsira nyale,+ zoikamo phulusa la zingwe za nyale,+ ndi ziwiya zake zonse+ zosungiramo mafuta ogwiritsa ntchito nthawi zonse. 10  Choikapo nyalecho, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, azichiika m’zikopa za akatumbu+ n’kupisako mtengo wonyamulira. 11  Kenako, aziphimba guwa lansembe+ lagolide ndi nsalu yabuluu. Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu,+ n’kubwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+ 12  Akatero, azitenga ziwiya zonse+ zimene amachitira utumiki wawo nthawi zonse m’malo oyera, n’kuzikuta ndi nsalu yabuluu. Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu,+ n’kuikako mtengo wake wonyamulira. 13  “Ndipo azichotsa phulusa losakanizika ndi mafuta la paguwa lansembe+ n’kuyalapo nsalu ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. 14  Akatero, aziikaponso ziwiya zonse zimene amachitira utumiki paguwapo nthawi zonse. Aziikapo zoikamo phulusa la zingwe za nyale, mafoloko aakulu, mafosholo, mbale zolowa, ndi ziwiya zonse za paguwa lansembe.+ Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, n’kubwezeretsa mitengo yake yonyamulira.+ 15  “Aroni ndi ana ake akamaliza kuphimba zinthu za m’malo oyera+ ndi ziwiya zonse+ za m’malo oyerawo posamutsa msasa, ana a Kohati azilowamo n’kudzazinyamula.+ Iwo asamakhudze+ zinthu za m’malo oyerazo chifukwa angafe. Zinthu zimenezi ndizo katundu wa m’chihema chokumanako amene ana a Kohati azinyamula.+ 16  “Eleazara mwana wa wansembe Aroni, aziyang’anira+ mafuta+ a nyale, zofukiza zonunkhira,+ nsembe yanthawi zonse yambewu,+ ndi mafuta odzozera.+ Aziyang’aniranso chihema chonse chopatulika ndi zonse za mmenemo, ndiwo malo oyerawo ndi ziwiya zake.” 17  Yehova analankhulanso ndi Mose ndi Aroni, kuti: 18  “Musalole kuti fuko la mabanja a Akohati+ liwonongeke pakati pa Alevi. 19  Kuti iwo asaphedwe poyandikira zinthu zopatulika koposa,+ koma akhalebe ndi moyo, Aroni ndi ana ake azilowa m’chihemacho. Mmenemo azigawira aliyense wa iwo ntchito ndi katundu woti anyamule. 20  Ana a Kohatiwo asadzayese kulowamo kuti akaone ngakhale pang’ono pokha zinthu zopatulikazo kuti angafe.”+ 21  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 22  “Uwerenge ana onse a Gerisoni.+ Uwawerenge potsata nyumba za makolo awo malinga ndi mabanja awo. 23  Uwerenge kuyambira azaka 30 mpaka 50,+ onse olowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako. 24  Tsopano utumiki umene mabanja a Agerisoni azichita ndiponso katundu amene azinyamula ndi uwu:+ 25  Azinyamula nsalu za chihema chopatulika+ ndi chihema chokumanako,+ ndiponso chophimba chake,+ chophimba cha chikopa cha katumbu+ chomwe chili pamwamba pake, ndi nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema chokumanako. 26  Azinyamulanso nsalu za mpanda+ wa bwalo ndi nsalu yotchinga+ khomo la mpanda umene umazungulira chihema chopatulika ndi guwa lansembe. Ndiponso azinyamula zingwe zolimbitsira mpandawo, ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wawo, pamodzi ndi zinthu zina zonse zogwirira ntchito zawo za nthawi zonse. Umenewu ndiwo utumiki wawo. 27  Ana a Gerisoni+ azichita utumiki wawo wonse molangizidwa ndi Aroni ndi ana ake.+ Aziwauza ntchito zimene azigwira ndi katundu amene azinyamula. Onse muziwagawira katundu amene azinyamula monga gawo lawo. 28  Uwu ndiwo utumiki umene mabanja a ana a Gerisoni+ azichita m’chihema chokumanako. Itamara+ mwana wa wansembe Aroni, ndiye aziyang’anira utumiki wawo. 29  “Ana a Merari+ uwawerenge malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo. 30  Uwerenge kuyambira azaka 30 mpaka 50, onse olowa m’gulu la ogwira ntchito pachihema chokumanako.+ 31  Tsopano uyu ndi katundu amene azinyamula,+ monga gawo la utumiki wawo m’chihema chokumanako: Mafelemu+ a chihema chopatulika, mipiringidzo yake,+ mizati yake,+ ndiponso zitsulo zokhazikapo mizati ndi mafelemu.+ 32  Azinyamulanso nsanamira+ zozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo nsanamirazo,+ zikhomo+ ndi zingwe zolimbitsira mpandawo limodzi ndi zipangizo zonse zimene amachitira utumiki wawo. Aliyense muzimugawira katundu woti azinyamula monga gawo lake.+ 33  Uwu ndiwo utumiki wa mabanja a ana a Merari,+ monga gawo la utumiki wawo m’chihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni, ndiye aziyang’anira utumiki wawo.”+ 34  Tsopano Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a anthuwo,+ anawerenga ana a Kohati+ malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo. 35  Anawerenga kuyambira azaka 30+ mpaka 50,+ onse amene analowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako.+ 36  Onse owerengedwa, malinga ndi mabanja awo, anakwana 2,750.+ 37  Awa ndiwo anawerengedwa+ mwa mabanja a ana a Kohati, onse otumikira m’chihema chokumanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera mawu a Yehova kwa Mose. 38  Onse owerengedwa mwa ana a Gerisoni,+ malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, 39  kuyambira azaka 30 mpaka 50, onse amene analowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako,+ 40  amene anawerengedwa malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, onse pamodzi anakwana 2,630.+ 41  Amenewa ndiwo anawerengedwa mwa mabanja a ana a Gerisoni, onse otumikira m’chihema chokumanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera mawu a Yehova.+ 42  Onse owerengedwa mwa mabanja a ana a Merari, malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, 43  kuyambira azaka 30 mpaka 50, onse olowa m’gulu la ogwira ntchito m’chihema chokumanako,+ 44  amene anawerengedwa malinga ndi mabanja awo, onse pamodzi anakwana 3,200.+ 45  Amenewa ndiwo anawerengedwa mwa mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera mawu a Yehova kwa Mose.+ 46  Alevi onse owerengedwa, amene Mose ndi Aroni limodzi ndi atsogoleri a Isiraeli anawawerenga, malinga ndi mabanja awo potsata nyumba za makolo awo, 47  kuyambira azaka 30 mpaka 50,+ onse ogwira ntchito yolemetsa ndi utumiki wonyamula katundu m’chihema chokumanako,+ 48  onse owerengedwawo anakwana 8,580.+ 49  Pomvera mawu a Yehova, Mose anawawerenga, aliyense malinga ndi utumiki wake ndi katundu wake wonyamula. Anawerengedwa monga mmene Yehova analamulira Mose.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:5.