Numeri 2:1-34
2 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni kuti:
2 “Ana a Isiraeli azikhoma mahema awo, aliyense azikhoma hema wake m’chigawo chawo cha mafuko atatu,+ potsata chizindikiro cha nyumba ya makolo ake. Azikhoma mahema awo mozungulira chihema chokumanako komanso moyang’ana chihemacho.
3 “Chigawo cha mafuko atatu cha Yuda ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kum’mawa kotulukira dzuwa. Mtsogoleri wa ana a Yuda ndi Naasoni,+ mwana wa Aminadabu.
4 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 74,600.+
5 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Isakara.+ Mtsogoleri wa ana a Isakara ndi Netaneli,+ mwana wa Zuwara.
6 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 54,400.+
7 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa ana a Zebuloni ndi Eliyabu,+ mwana wa Heloni.
8 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 57,400.+
9 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Yuda alipo 186,400. Amenewa azikhala oyamba kunyamuka.+
10 “Chigawo cha mafuko atatu cha Rubeni+ ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kum’mwera. Mtsogoleri wa ana a Rubeni ndi Elizuri,+ mwana wa Sedeuri.
11 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 46,500.+
12 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Simiyoni. Mtsogoleri wa ana a Simiyoni ndi Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai.
13 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 59,300.+
14 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Gadi. Mtsogoleri wa ana a Gadi ndi Eliyasafu,+ mwana wa Reueli.
15 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 45,650.+
16 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Rubeni alipo 151,450. Amenewa azikhala achiwiri kunyamuka.+
17 “Posamutsa chihema chokumanako,+ gulu la msasa wa Alevi+ lizikhala pakati pa magulu a misasa ina.
“Dongosolo limene azilitsatira posamuka,+ n’limenenso azitsatira pomanga misasa yawo, aliyense m’malo ake, malinga ndi chigawo chawo cha mafuko atatu.
18 “Chigawo cha mafuko atatu cha Efuraimu+ ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kumadzulo. Mtsogoleri wa ana a Efuraimu ndi Elisama,+ mwana wa Amihudi.
19 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 40,500.+
20 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Manase.+ Mtsogoleri wa ana a Manase ndi Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri.
21 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 32,200.+
22 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Benjamini.+ Mtsogoleri wa ana a Benjamini ndi Abidana,+ mwana wa Gidoni.
23 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 35,400.+
24 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Efuraimu alipo 108,100. Amenewa azikhala achitatu kunyamuka.+
25 “Chigawo cha mafuko atatu cha Dani ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kumpoto. Mtsogoleri wa ana a Dani ndi Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai.
26 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 62,700.+
27 Kumbali yake imodzi azimangako a fuko la Aseri. Mtsogoleri wa ana a Aseri ndi Pagiyeli,+ mwana wa Okirani.
28 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 41,500.+
29 Kumbali yake ina azimangako a fuko la Nafitali.+ Mtsogoleri wa ana a Nafitali ndi Ahira,+ mwana wa Enani.
30 Asilikali ake olembedwa mayina alipo 53,400.+
31 “Asilikali onse olembedwa mayina a msasa wa Dani alipo 157,600. Amenewa azikhala omalizira kunyamuka,+ malinga ndi zigawo za Aisiraeli za mafuko atatuatatu.”
32 Amenewa ndiwo anali olembedwa mayina a ana a Isiraeli, malinga ndi nyumba ya makolo awo. Asilikali onse olembedwa mayina m’misasa yonse, analipo 603,550.+
33 Koma Alevi sanawawerenge+ pamodzi ndi ana a Isiraeli enawo, monga Yehova analamulira Mose.
34 Ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose.+ Dongosolo limene analitsatira pomanga misasa yawo m’zigawo za mafuko atatu,+ n’limenenso anatsatira posamuka,+ aliyense m’banja lake malinga ndi nyumba ya makolo ake.

