Numeri 24:1-25

24  Balamu ataona kuti Yehova akungowadalitsa Aisiraeli, sanapitenso kukawafunira tsoka lina lililonse+ mmene anachitira nthawi zina zija.+ M’malomwake, anatembenuka n’kuyang’ana kuchipululu.  Pamene Balamu anakweza maso ake n’kuona Aisiraeli ali m’misasa mwa mafuko awo,+ mzimu wa Mulungu unafika pa iye.+  Pamenepo anayamba kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti: “Mawu a Balamu mwana wa Beori,Mawu a mwamuna wamphamvu, maso ake ali chitsegukire,+   Mawu a iye wakumva zonena za Mulungu,+Iye amene waona masomphenya a Wamphamvuyonse,+Pamene anali kugwa pansi, maso ake ali chipenyere.+ Mawu ake akuti:   Akongolerenji malo ako okhala Yakobo! Mahema ako n’ngokongola ndithu Isiraeli!+   Andanda kukafika kutali ngati zigwa,*+Ngati minda m’mphepete mwa mtsinje.+Ngati mitengo ya aloye imene Yehova anabzala,Ngati mikungudza m’mbali mwa madzi.+   Madzi odzaza mitsuko yake iwiri akutayikirabe pansi,Ndipo mbewu yake ili m’mbali mwa madzi ambiri.+Mfumu yakenso+ idzakwezeka kuposa Agagi,+Ndi ufumu wake udzakwezedwa.+   Mulungu akum’tulutsa mu Iguputo.Amathamanga mwaliwiro ngati ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+Adzameza anthu a mitundu ina, om’pondereza iye,+Adzakungudza mafupa awo,+ n’kudzawaswa ndi mivi yake.+   Iye anagwada pansi. Anagona pansi ngati mkango.Ngati mkango, ndani angayese kum’dzutsa?+Odalitsa iwe n’ngodalitsika,+Ndipo otemberera iwe n’ngotembereredwa.”+ 10  Pamenepo Balaki anapsera mtima Balamu n’kuwomba m’manja.+ Kenako anauza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere+ adani anga, koma iwe wawadalitsa kwambiri katatu konseka! 11  Choka! Nyamuka uzipita. Ine ndimati ndikupatse ulemerero,+ koma taona! Yehova wakumanitsa ulemererowo.” 12  Balamu poyankha anafunsa Balaki kuti: “Kodi sindinanene kwa amithenga anu amene munawatuma kwa ine, kuti, 13  ‘Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chochokera mumtima mwanga, kaya chabwino kapena choipa, chosemphana ndi zimene Yehova walamula? Sindinanene kodi, kuti chilichonse chimene Yehova ati alankhule, ndilankhula chomwecho’?+ 14  Chabwino, ndikupita kwa anthu a mtundu wanga. Koma tamverani, ndikuuzeni+ zimene anthuwa adzachite kwa anthu anu kumapeto kwa masiku otsiriza.”+ 15  Kenako anayambanso kulankhula mwa ndakatulo,+ kuti:“Mawu a Balamu mwana wa Beori,Mawu a mwamuna wamphamvu, maso ake ali chitsegukire,+ 16  Mawu a munthu womva zonena za Mulungu,+Iye wozindikira nzeru za Wam’mwambamwamba . . .Iye anaona masomphenya a Wamphamvuyonse+Pamene anali kugwa pansi, maso ake ali chipenyere.+ Mawu ake ndi akuti: 17  Ndidzamuona,+ koma si nthawi ino;Ndidzam’penya, koma si panopo.Ndithu nyenyezi+ idzatuluka mwa Yakobo,Ndodo yachifumu idzatulukadi mu Isiraeli.+Ndipo iye adzaphwanya chipumi cha Mowabu+Ndi chigaza cha ana onse ankhondo. 18  Edomu adzalandidwa,+Ndithu Seiri+ adzalandidwa ndi adani ake,+Pamene Isiraeli akuonetsa kulimba mtima kwake. 19  Wina adzatuluka mwa Yakobo kukagonjetsa,+Adzawononga wopulumuka aliyense mumzindamo.”+ 20  Tsopano Balamu ataona Amaleki, anapitiriza mawu ake a ndakatulo, kuti:+“Amaleki anali woyamba wa anthu a mitundu ina,+Koma chiwonongeko chake chidzakhaladi mapeto ake.”+ 21  Iye ataona Akeni,+ anapitirizanso mawu ake a ndakatulo, kuti:“Mokhala mwanu ndi mokhazikika, malo okhala inu ali pathanthwe. 22  Koma adzafika wodzanyeketsa Kayini*+ ndi moto.Kodi udzakhalabe mpaka liti Asuri asanakugwire n’kupita nawe kudziko lina?”+ 23  Iye anapitiriza kulankhula mawu ake a ndakatulo, kuti:“Kalanga ine! Adzapulumuke tsokalo ndani, Mulungu akadzaliponya?+ 24  Padzafika zombo zochokera kugombe la Kitimu,+Ndipo iwo adzasautsa Asuri+ ndithu,Adzasautsadi Ebere.Koma iyenso adzawonongeka pamapeto pake.” 25  Tsopano Balamu ananyamuka kumabwerera kwawo.+ Nayenso Balaki ananyamuka kulowera njira yake.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Onani mawu a m’munsi pa Nu 23:22.
“Kayini” akuimira fuko la “Akeni.”