Numeri 15:1-41

15  Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti:  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Mukakafika m’dziko limene ndikukupatsani, kumalo amene muzikakhala,+  popereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova,+ kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe yochitira lonjezo lapadera, kapena nsembe yongopereka mwaufulu,+ kapena yopereka pa nthawi ya zikondwerero zanu,+ kuti mufukize fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova+ la nyama ya ng’ombe kapena ya nkhosa,  wopereka nsembeyo, azikaperekanso kwa Yehova nsembe yambewu ya ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini.*  Ndipo muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa.+ Azikakhala wokwanira gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini. Vinyoyo muzikam’pereka limodzi ndi nsembe yopsereza, kapena ndi nsembe ya mwana wa nkhosa wamphongo.  Komanso popereka nsembe ya nkhosa yamphongo, muzikaipereka limodzi ndi nsembe yambewu yokwanira magawo awiri a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini.  Ndiponso muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini, monga fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.  “‘Koma ngati mukupereka ng’ombe yamphongo monga nsembe yopsereza,+ kapena monga nsembe yochitira lonjezo lapadera,+ kapenanso monga nsembe zachiyanjano kwa Yehova,+  woperekayo azikapereka ng’ombe yamphongoyo limodzi ndi nsembe yambewu.+ Nsembe yambewuyo izikakhala yokwanira magawo atatu a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo azikauthira mafuta okwanira hafu ya muyezo wa hini. 10  Ndiponso muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa.+ Vinyoyo azikakhala wokwanira hafu ya muyezo wa hini. Akakhale nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 11  Izi n’zimene muyenera kuchita popereka ng’ombe yamphongo iliyonse, nkhosa yamphongo iliyonse, mwana wa nkhosa wamphongo, kapena mbuzi. 12  Muyenera kuchita zimenezi panyama iliyonse yoti mupereke nsembe, ngakhale zitachuluka motani. 13  Mbadwa iliyonse izichita zimenezi popereka nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ 14  “‘Ngati mlendo wokhala pakati panu, kapena mlendo amene wakhala nanu kwa mibadwomibadwo, afunikira kupereka nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova, monga mmene inuyo muzichitira, iyenso azichita momwemo.+ 15  Inu amene mwapanga mpingo limodzi ndi alendo amene akukhala pakati panu, mukhale ndi malamulo amodzi.+ Amenewa ndiwo malamulo amene inuyo muziwatsatira mpaka kalekale m’mibadwo yanu. Mlendo azikhala chimodzimodzi ndi inu pamaso pa Yehova.+ 16  Pakhale malamulo ndi zigamulo zofanana kwa inu ndi kwa alendo amene akukhala nanu.’”+ 17  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 18  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Mukakalowa m’dziko limene ndikukutengeraniko,+ 19  muzikapereka chopereka kwa Yehova pachakudya chilichonse cha m’dzikolo,+ chimene muzikadya. 20  Muzikapereka mikate yozungulira yoboola pakati ya ufa wamisere monga chopereka cha zipatso zoyambirira kucha.+ Muzikaipereka ngati mmene mumaperekera chopereka chochokera popunthira mbewu. 21  Muzipereka kwa Yehova ufa wamisere wa zipatso zanu zoyambirira ku mibadwo yanu yonse. 22  “‘Koma ngati mwachita cholakwa cholephera kusunga malamulo onsewa+ amene Yehova walankhula kudzera mwa Mose, 23  zonse zimene Yehova wakulamulirani kudzera mwa Mose, kuchokera pa tsiku limene Yehova analamula mpaka ku mibadwo yanu yonse, 24  ngati khamulo lachita cholakwacho mosazindikira, pamenepo khamu lonselo lipereke ng’ombe yaing’ono yamphongo monga nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Apereke nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa monga mwa dongosolo la nthawi zonse.+ Aperekenso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ 25  Pamenepo wansembe azipereka nsembe yophimba machimo+ a khamu lonse la ana a Isiraeli. Akatero, anthuwo azikhululukidwa cholakwacho chifukwa anachita mosazindikira,+ komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova, ndiponso nsembe yamachimo kwa Yehova pa cholakwa chawocho. 26  Khamu lonse la ana a Isiraeli lizikhululukidwa+ limodzi ndi alendo amene akukhala pakati pawo, chifukwa anthu onsewo anachimwa mosazindikira. 27  “‘Ngati munthu angachimwe mosazindikira,+ apereke mbuzi yaikazi yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ 28  Wansembe apereke nsembe yophimba tchimo la munthuyo, amene walakwira Yehova mosazindikira, kuti akhululukidwe.+ 29  Munthu akachita tchimo mosazindikira, pazikhala lamulo limodzi, kwa mbadwa ya ana a Isiraeli ndi kwa mlendo wokhala pakati pawo.+ 30  “‘Koma munthu amene wachita cholakwa mwadala,+ kaya akhale mbadwa kapena mlendo, kumene kuli kunyoza Yehova,+ munthuyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake.+ 31  Munthu ameneyo wanyoza mawu a Yehova,+ ndipo waphwanya malamulo ake.+ Aziphedwa ndithu mosalephera.+ Mlandu wa cholakwa chake uzikhala ndi iye mwini.’”+ 32  M’chipululumo, tsiku lina ana a Isiraeli anapeza munthu wina akutola nkhuni pa tsiku la sabata.+ 33  Amene anam’peza akutola nkhuniwo anam’tengera kwa Mose ndi Aroni ndi kwa khamu lonselo. 34  Iwo anam’sunga kaye+ chifukwa panalibe lamulo lachindunji lonena chilango chimene akanapereka. 35  Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: “Munthuyo aphedwe basi!+ Khamu lonselo likam’ponye miyala kunja kwa msasa.”+ 36  Choncho khamu lonselo linam’tengera kunja kwa msasa kumene linakam’ponya miyala mpaka kufa, monga mmene Yehova analamulira Mose. 37  Kenako Yehova anauza Mose kuti: 38  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti azisokerera mphonje m’mphepete mwa zovala zawo, ku mibadwo yawo yonse. Azisokereranso chingwe cha buluu pamwamba pa mphonje za zovalazo.+ 39  ‘Chingwecho chikhale ngati mphonje kwa inu, kuti mukachiyang’ana muzikumbukira malamulo onse+ a Yehova ndi kuwasunga. Muleke kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu,+ chifukwa potsatira zilakolako zimenezo, mukuchita chiwerewere.+ 40  Ndakupatsani lamulo limeneli kuti muzikumbukira ndi kusunga malamulo anga onse, ndi kukhaladi oyera kwa Mulungu wanu.+ 41  Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo, kuti ndionetse kuti ndine Mulungu wanu.+ Ndine Yehova Mulungu wanu.’”+

Mawu a M'munsi

Gawo limodzi la magawo 10 a muyezo wotchedwa “efa” ndi lofanana ndi malita awiri.
“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.