Numeri 10:1-36

10  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Upange malipenga+ awiri asiliva. Uchite kusula, ndipo uziwagwiritsa ntchito poitanitsa+ msonkhano ndi posamutsa msasa.  Akaliza malipenga onse awiriwo, khamu lonse lizisunga pangano la msonkhano ndi iwe, ndipo lizifika pakhomo la chihema chokumanako.+  Koma akaliza lipenga limodzi lokha, akuluakulu amene ndi atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, nawonso azisunga pangano la msonkhano ndi iwe.+  “Mukaliza lipenga lolira mosinthasintha, a m’misasa yakum’mawa+ azinyamuka ulendo.  Mukaliza kachiwiri lipenga lolira mosinthasintha, a m’misasa yakum’mwera+ azinyamuka ulendo. Gulu lililonse likamanyamuka, aziliza lipenga lolira mosinthasintha.  “Poitanitsa msonkhano wa anthu onse muziliza lipenga,+ koma osati lolira mosinthasintha.  Ana a Aroni, ansembewo, ndiwo aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kugwiritsa ntchito malipengawa m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale.*  “Adani okuvutitsani akakuukirani+ kuti akuthireni nkhondo m’dziko lanu, muziliza malipengawo+ moitanira asilikali kunkhondo. Mukatero, Mulungu wanu Yehova adzakukumbukirani ndithu ndi kukupulumutsani kwa adani anuwo.+ 10  “Pa tsiku lanu losangalala,+ pa nyengo ya zikondwerero zanu,+ ndi pa masiku oyambira miyezi,+ muziliza malipengawo popereka nsembe zanu zopsereza+ ndi zachiyanjano.+ Kuliza malipengawo kudzakhala chikumbutso kwa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”+ 11  Tsopano m’chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni. 12  Nawonso ana a Isiraeli ananyamuka mwa dongosolo lawo lonyamukira.+ Ananyamuka m’chipululu cha Sinai, ndipo mtambowo unakaima m’chipululu cha Parana.+ 13  Iwo anasamuka malinga ndi malangizo amene Yehova anapereka kudzera kwa Mose.+ Kameneka kanali koyamba kuti iwo asamuke. 14  Choncho, a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Yuda ndiwo anayamba kunyamuka m’magulu awo.+ Mtsogoleri wa asilikali awo anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu. 15  Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Isakara anali Netaneli,+ mwana wa Zuwara. 16  Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Zebuloni anali Eliyabu, mwana wa Heloni.+ 17  Chihema chopatulika chitapasulidwa,+ ana a Gerisoni+ ndi ana a Merari,+ onyamula chihema chopatulikacho, ananyamuka. 18  Kenako, a m’chigawo cha mafuko atatu cha Rubeni+ ananyamuka m’magulu awo. Mtsogoleri wa asilikali awo anali Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 19  Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Simiyoni+ anali Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 20  Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Gadi anali Eliyasafu,+ mwana wa Deyueli. 21  Kenako Akohati, onyamula zinthu za m’malo opatulika+ ananyamuka, kuti pokafika akapeze chihema chopatulika chitamangidwa kale. 22  Ndiyeno a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Efuraimu+ ananyamuka m’magulu awo. Mtsogoleri wa asilikali awo anali Elisama,+ mwana wa Amihudi. 23  Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Manase+ anali Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 24  Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Benjamini+ anali Abidana,+ mwana wa Gidoni. 25  Pomaliza, a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Dani+ ananyamuka. Iwo ndiwo anali olonda kumbuyo kwa zigawo zonse za mafukowo.+ Mtsogoleri wa asilikali awo anali Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26  Mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Aseri+ anali Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 27  Ndipo mtsogoleri wa asilikali a fuko la ana a Nafitali+ anali Ahira,+ mwana wa Enani. 28  Ili ndilo dongosolo limene ana a Isiraeli anali kulitsatira posamuka m’magulu awo.+ 29  Ndiyeno Mose anauza Hobabu yemwe anali mwana wa Reueli+ Mmidiyani, mpongozi wake kuti: “Tikusamukira kumalo amene Yehova anati, ‘Ndidzawapereka kwa inu.’+ Tiyeni tipite limodzi, ndipo tidzakuchitirani zabwino ndithu,+ pakuti Yehova analonjeza Aisiraeli zabwino.”+ 30  Koma iye anamuyankha kuti: “Ayi, sindipita nanu kumeneko. Ndikubwerera kudziko lakwathu,+ kwa abale anga.” 31  Komabe Mose anam’pempha kuti: “Chonde musatisiye, pakuti inu mukudziwa bwino kumene tingamange msasa m’chipululu muno, ndipo mungakhale maso athu. 32  Mukapita nafe limodzi,+ popeza Yehova adzatichitira zabwino, ifenso tidzakuchitirani zabwino.” 33  Chotero iwo ananyamuka kuphiri la Yehova,+ n’kuyenda ulendo wa masiku atatu. Likasa la pangano la Yehova+ linali patsogolo pawo ulendo wa masiku atatu wonsewo, kuwafunira malo oti amangepo msasa.+ 34  Akanyamuka pamsasa masana, mtambo wa Yehova+ unali pamwamba pawo. 35  Nthawi zonse likasa likamanyamuka, Mose anali kunena kuti: “Nyamukani, inu Yehova, adani anu abalalike.+ Ndipo amene ali nanu chidani chachikulu athawe patsogolo panu.”+ 36  Nthawi zonse likasalo likaima, iye ankati: “Bwererani inu Yehova, kumiyandamiyanda yosawerengeka ya Aisiraeli.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.