Numeri 13:1-33

13  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti:  “Utume amuna kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.+ Pa fuko lililonse utume mwamuna mmodzi, amene ali mtsogoleri+ wa fukolo.”  Chotero Mose anatumiza amunawo kuchokera kuchipululu cha Parana,+ monga mmene Yehova analamulira. Amuna onsewo anali atsogoleri a ana a Isiraeli.  Mayina awo ndi awa: Wa fuko la Rubeni anali Samuwa, mwana wa Zakuri.  Wa fuko la Simiyoni anali Safati, mwana wa Hori.  Wa fuko la Yuda anali Kalebe,+ mwana wa Yefune.  Wa fuko la Isakara anali Igali, mwana wa Yosefe.  Wa fuko la Efuraimu anali Hoshiya,+ mwana wa Nuni.  Wa fuko la Benjamini anali Paliti, mwana wa Rafu. 10  Wa fuko la Zebuloni anali Gadiyeli, mwana wa Sodi. 11  Wa fuko la Yosefe,+ loimira fuko la Manase,+ anali Gadidi mwana wa Susi. 12  Wa fuko la Dani anali Amiyeli, mwana wa Gemali. 13  Wa fuko la Aseri anali Seturi, mwana wa Mikayeli. 14  Wa fuko la Nafitali anali Nabi, mwana wa Vopisi. 15  Wa fuko la Gadi anali Geyuweli, mwana wa Maki. 16  Amenewa ndiwo mayina a amuna amene Mose anawatuma kuti akazonde dzikolo. Mose anatcha Hoshiya mwana wa Nuni kuti Yehoswa.*+ 17  Powatumiza kuti akazonde dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Pitani ku Negebu,+ ndipo mukafike kudera lamapiri.+ 18  Mukaone kuti dzikolo n’lotani.+ Mukaonenso ngati anthu a m’dzikomo ali amphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ali owerengeka kapena ambiri. 19  Mukaone ngati dziko limene akukhalamo lili labwino kapena loipa, ndiponso ngati akukhala m’misasa kapena m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. 20  Komanso mukaone ngati dzikolo lili lachonde kapena lopanda chonde,+ ngati lili ndi mitengo kapena ayi. Mukalimbe mtima+ n’kutengako zipatso za m’dzikomo.” Amenewa anali masiku amene mphesa zoyamba zinali kupsa.+ 21  Choncho amunawo anapita kukazonda dzikolo, kuyambira kuchipululu cha Zini+ mpaka ku Rehobu,+ kufupi ndi Hamati.+ 22  Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni.+ Kumeneko anapezako Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ mbadwa za Anaki.*+ Mzinda wa Heburoni+ unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani+ wa ku Iguputo usanamangidwe. 23  Atafika kuchigwa* cha Esikolo,+ anadula nthambi yokhala ndi tsango limodzi la mphesa,+ ndipo anthu awiri analinyamula paphewa ndi mitengo yonyamulira. Anatengakonso makangaza*+ ndi nkhuyu. 24  Malowo anawatcha chigwa cha Esikolo,+ chifukwa chakuti ana a Isiraeliwo anadulapo tsango la mphesa. 25  Potsirizira pake anabwerako kokazonda dziko kuja patatha masiku 40.+ 26  Iwo anabwera kwa Mose ndi Aroni, ndiponso kwa khamu lonse la ana a Isiraeli m’chipululu cha Parana, ku Kadesi.+ Anafotokozera onsewo za ulendo wawo n’kuwaonetsa zipatso za kudzikolo. 27  Anauza Mose kuti: “Tinakalowa m’dziko limene munatitumako. Ndithudi ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ ndipo zipatso zake ndi izi.+ 28  Ngakhale zili choncho, anthu okhala kumeneko ndi anthu amphamvu zawo, mizinda yawo ndi yotchingidwa ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso yaitali.+ Si zokhazo, mbadwa za Anaki zija tinaziona kumeneko.+ 29  Aamaleki+ amakhala ku Negebu.+ Ahiti, Ayebusi+ ndi Aamori+ amakhala kudera lamapiri. Akanani+ amakhala m’mphepete mwa nyanja, ndi m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano.” 30  Pamenepo Kalebe+ anayesa kukhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, kenako anati: “Tiyeni tipite tsopano lino, tikalanda dzikolo, pakuti tikaligonjetsa ndithu.”+ 31  Koma amuna amene anapita naye limodzi ananena kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.”+ 32  Ndipo iwo anapitiriza kuuza ana a Isiraeliwo zoipa+ za dziko limene anakalizondalo, kuti: “Dziko limene tinakalizondalo limameza anthu ake, ndipo anthu onse amene tinawaona kumeneko ndi ziphona zamatupi akuluakulu.+ 33  Tinaonakonso Anefili,* mbadwa za Anaki,+ moti eni akefe tinangodziona ngati tiziwala kwa iwo. Iwonso ndi mmene anationera.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Yoswa,” kutanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso.”
Kapena kuti “Chiphona.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Mawu akuti “Anefili” amatanthauza “ogwetsa anzawo.”