Numeri 14:1-45

14  Pamenepo khamu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anachezera kulira+ usiku wonse.  Ana onse a Isiraeli anayamba kudandaula za Mose ndi Aroni.+ Ndipo khamu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera m’chipululu muno.  N’chifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+  Iwo anafika ngakhale pouzana kuti: “Tiyeni tisankhe mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo!”+  Mose ndi Aroni atamva zimenezi, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ pamaso pa khamu lonse la ana a Isiraeli.  Ndipo Yoswa mwana wa Nuni,+ ndi Kalebe mwana wa Yefune,+ amene anakazonda nawo dzikolo, anang’amba zovala zawo.+  Iwo anauza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti: “Dziko limene tinakalowamo n’kulizonda, n’labwino kwambiri.+  Yehova akatikomera mtima,+ ndithu adzatilowetsa m’dzikolo n’kulipereka kwa ife, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+  Chongofunika n’chakuti musam’pandukire Yehova.+ Komanso anthu a m’dzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo,+ koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope ayi.”+ 10  Koma khamu lonselo linayamba kunena zoti liwaponye miyala.+ Kenako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa ana a Isiraeli onse pamwamba pa chihema chokumanako.+ 11  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza kufikira liti?+ Kodi adzayamba liti kundikhulupirira pambuyo pa zizindikiro zonse zimene ndachita pakati pawo?+ 12  Ndiwagwetsera mliri ndi kuwafafaniza, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwowa.”+ 13  Koma Mose anamuyankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene munalanditsako anthuwa mwa mphamvu zanu, adzamva ndithu zimenezi.+ 14  Iwo akamva adzauza anthu a m’dziko lino, amene amva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu anu,+ ndi kuti mumaonekera kwa iwo pamasom’pamaso.+ Inu ndinu Yehova, ndipo mtambo wanu uli pamwamba pawo. Masana mumawatsogolera mumtambo woima njo ngati chipilala, pamene usiku mumawatsogolera m’lawi lamoto.+ 15  Mukapha anthuwa kamodzi n’kamodzi ngati mukupha munthu mmodzi,+ ndithu mitundu imene yamva za ukulu wanu idzati, 16  ‘Chifukwa Yehova analephera kufikitsa anthuwo kudziko limene anawalumbirira, anangowaphera m’chipululu.’+ 17  Chonde Yehova, tsopano sonyezani ukulu wa mphamvu zanu,+ monga munanenera kuti, 18  ‘Yehova ndi wosakwiya msanga,+ ndipo ndi wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Amakhululukira wolakwa ndi wophwanya malamulo,+ koma iye salekerera konse wolakwa osam’langa.+ Amalanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za makolo awo.’+ 19  Chonde, khululukani kulakwa kwa anthuwa mwa kukoma mtima kwanu kosatha, ngati mmene mwakhala mukuwakhululukira kuchokera ku Iguputo mpaka pano.”+ 20  Ndiyeno Yehova anati: “Chabwino, ndakhululuka chifukwa cha mawu ako.+ 21  Komanso, pali ine Mulungu wamoyo, dziko lonse lapansi lidzadzaza ndi ulemerero wa Yehova.+ 22  Koma anthu onse amene aona ulemerero wanga,+ ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, ndi zimene ndachita m’chipululu, amene akupitirizabe kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, amenenso sanamvere mawu anga,+ 23  sadzaliona m’pang’ono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+ 24  Koma mtumiki wanga Kalebe,+ chifukwa wasonyeza kuti ali ndi mzimu wosiyana ndi wa ena, ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse,+ ndithudi ndidzam’lowetsa m’dziko limene anakalizonda, ndipo mbadwa zake zidzakhalamo ngati dziko lawo.+ 25  Popeza kuti Aamaleki ndi Akanani+ akukhala kuchigwa, mawa mutembenuke, munyamuke ulendo wolowera kuchipululu podzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.”+ 26  Yehova anapitiriza kulankhula kwa Mose ndi Aroni, kuti: 27  “Kodi khamu la anthu oipa amenewa lidandaula motsutsana nane kufikira liti?+ Ndamva kudandaula konseko kumene ana a Isiraeli akuchita motsutsana nane.+ 28  Uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, mudzandifunse ngati sindidzachita kwa inu monga mwa zimene mwakhala mukulankhula, zimene ndadzimvera ndekha m’makutu mwangamu.+ 29  Mitembo yanu idzagona m’chipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30  Inu simudzalowa m’dziko limene ndinachita kukweza dzanja langa+ polumbira kuti ndidzakhala nanu mmenemo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.+ 31  “‘“Komanso, ana anu amene munati adzatengedwa ndi adani,+ nawonso ndidzawalowetsa m’dzikolo ndithu. Moti dziko limene inuyo mwalikana, iwo adzalidziwa bwino.+ 32  Koma inuyo mitembo yanu idzagona m’chipululu muno.+ 33  Ana anu adzakhala abusa m’chipululu+ kwa zaka 40, ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika*+ kwanu, mpaka womalizira kufa wa inu atagona m’manda m’chipululu.+ 34  Mwa kuchuluka kwa masiku amene munazonda dzikolo, masiku 40,+ mudzalangidwanso kwa zaka 40+ chifukwa cha zolakwa zanu, tsiku limodzi kuwerengera chaka chimodzi, tsiku limodzi chaka chimodzi,+ kuti mudziwe kuipa kondipandukira.+ 35  “‘“Ine Yehova ndalankhula, mudzandifunse ngati sindidzawafafaniza m’chipululu mommuno anthu oipa onsewa,+ amene agwirizana kuti atsutsane ndi ine. Onse adzathera m’chipululu mommuno.+ 36  Komanso amuna amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo, amene atabwerako anapangitsa anthu onse kudandaula motsutsana ndi Mose, mwa kunena zoipa zokhudza dzikolo,+ 37  amuna amene anadzanena zoipa zokhazokha zokhudza dzikolo, adzafa ndi mliri wa Yehova.+ 38  Koma mwa amuna amene anakazonda dzikolo, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, adzakhalabe ndi moyo ndithu.”’”+ 39  Mose atalankhula mawuwo kwa ana onse a Isiraeli, anthu onsewo anayamba kulira kwambiri.+ 40  Komanso, iwo anadzuka m’mawa kwambiri kuti apite kudera lamapiri lija, ndipo anati: “Tiyeni! Ife tipita kumalo amene Yehova ananena, chifukwa tachimwa.”+ 41  Koma Mose anati: “N’chifukwa chiyani mukuphwanya lamulo la Yehova?+ Zimenezo sizikuthandizani. 42  Musapite kumeneko chifukwa Yehova sali nanu. Adani anuwo akakugonjetsani.+ 43  Kumeneko mukakumana ndi Aamaleki ndi Akanani,+ ndithu akakuphani ndi lupanga. Chifukwa mwasiya kutsatira Yehova, Yehovayo sapita nanu kumeneko.”+ 44  Komabe, anthuwo ananyamuka mwa iwo okha ulendo wopita kudera lamapiri kuja,+ koma likasa la pangano la Yehova silinachoke pakati pa msasa. Mose nayenso sanachoke.+ 45  Koma Aamaleki+ ndi Akanani omwe anali kukhala kudera lamapirilo anatsika n’kuyamba kuwapha ndi kuwabalalitsa mpaka ku Horima.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “dama.”