Numeri 36:1-13

36  Atsogoleri a mabanja a ana a Giliyadi mwana wa Makiri,+ mwana wa Manase, ochokera kumabanja a ana a Yosefe, anafika ndi kulankhula ndi Mose ndi akalonga omwe anali atsogoleri a ana a Isiraeli.  Iwo anati: “Paja Yehova anakulamulani inu mbuyathu, kuti mugawire dzikoli ana a Isiraeli monga cholowa chawo, mwa kuchita maere.+ Yehova anakulamulaninso kuti cholowa cha m’bale wathu Tselofekadi muchipereke kwa ana ake aakazi.+  Tsopano ana aakaziwa akadzakwatiwa ndi amuna a mafuko ena a ana a Isiraeli, ndiye kuti cholowa chawo chidzachotsedwa ku cholowa cha makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense adzakwatiweko. Zikadzatero ndiye kuti cholowa chathu cha malo chidzachepa.+  Chaka cha Ufulu+ cha ana a Isiraeli chikadzafika, cholowa cha akaziwa chidzachotsedwa ku cholowa cha fuko la makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense wa iwo adzakwatiweko ndipo chidzakhala cha fukolo mpaka kalekale.”  Pamenepo Mose anauza ana a Isiraeli zimene Yehova anamuuza, kuti: “Fuko la ana a Yosefe likunena zoona.  Zimene Yehova walamula zokhudza ana aakazi a Tselofekadi+ n’zakuti, ‘Iwo angakwatiwe ndi aliyense amene wawakomera m’maso. Koma akwatiwe ndi amuna a fuko la makolo awo okha.+  Cholowa cha ana a Isiraeli chisachoke ku fuko lina kupita ku fuko lina. Aliyense wa ana a Isiraeli ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake.  Choncho, mwana wamkazi aliyense amene walandira nawo cholowa pakati pa mafuko a ana a Isiraeli, azikwatiwa ndi mwamuna wa m’banja la fuko la bambo ake,+ kuti aliyense wa ana a Isiraeli azilandira cholowa chochokera kwa makolo ake.  Cholowa chilichonse chisachoke ku fuko lina kupita ku fuko lina. Fuko lililonse la ana a Isiraeli lizisunga cholowa chake.’” 10  Ana aakazi a Tselofekadi amenewo anachitadi zimene Yehova analamula Mose.+ 11  Chotero, Mala, Tiriza, Hogila, Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Tselofekadi,+ anakwatiwa ndi ana a abale* a bambo awo. 12  Anakwatiwa ku mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, kuti cholowa chawo chisachoke ku fuko la banja la bambo awo. 13  Amenewa ndiwo malamulo+ ndi zigamulo za Yehova, zimene anapereka kwa ana a Isiraeli kudzera kwa Mose ku Yeriko, m’chipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.+

Mawu a M'munsi

“Abale a bambo awo” akutanthauza akulu awo kapena ang’ono awo a bambo awo.