Numeri 18:1-32

18  Tsopano Yehova analankhula ndi Aroni kuti: “Iwe ndi ana ako, ndi nyumba yonse ya bambo ako, mudzasenza zolakwa zanu pa malamulo okhudza malo opatulika.+ Iweyo ndi ana ako mudzasenza zolakwa zanu pa malamulo okhudza unsembe wanu.+  Utengenso abale ako a fuko la Levi, amtundu wa bambo ako, kuti azikhala pafupi ndi inu. Azitumikira+ iweyo limodzi ndi ana ako pachihema cha Umboni.+  Azitumikira inuyo ndi kugwira ntchito zawo za pachihema chonse.+ Koma asamayandikire zipangizo za m’malo oyera, kapena kuyandikira guwa lansembe kuti iwowo kapena inuyo mungafe.+  Azikhala pafupi nanu kuti azichita utumiki wawo wonse wa pachihema chokumanako, ndipo munthu wina aliyense amene si Mlevi asayandikire kwa inu.+  Muzichita utumiki wanu m’malo oyera+ ndi paguwa lansembe,+ kuti mkwiyo+ usadzawabukirenso ana a Isiraeli.  Inetu ndatenga abale anu Alevi, mwa ana a Isiraeli,+ ndipo ndawapereka kwa inu monga mphatso yanu.+ Iwowa akhala operekedwa kwa Yehova kuti atumikire pachihema chokumanako.+  Iweyo ndi ana ako, muzichita utumiki wanu waunsembe mosamala pa chilichonse chokhudza guwa lansembe, ndiponso pa zonse zamkati, kuseri kwa nsalu yotchinga.+ Umenewu ndiwo utumiki wanu.+ Unsembewu ndikukupatsani monga mphatso, ndipo aliyense wosakhala Mlevi akayandikira pafupi aziphedwa.”+  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni, kuti: “Inetu ndakupatsa udindo woyang’anira zopereka zonse zoperekedwa kwa ine.+ Pa zinthu zonse zopatulika zimene ana a Isiraeli azipereka, ndakupatsako gawo iweyo ndi ana ako, likhale gawo lanu mpaka kalekale.+  Gawo limenelo lizikhala lako pazopereka zopatulika koposa, ndizo nsembe zonse zotentha ndi moto. Nsembezo, zimene azibwera nazo kwa ine, ndi izi: Nsembe zawo zambewu,+ nsembe zawo zamachimo,+ nsembe zawo za kupalamula,+ ndi nsembe zawo zina zonse. Gawolo lizikhala chinthu chopatulika koposa kwa iwe ndi ana ako. 10  Uzilidyera m’malo oyera koposa,+ ndipo mwamuna aliyense azidyako.+ Gawo limenelo lizikhala chinthu chopatulika kwa iwe.+ 11  Mphatso zonse za ana a Isiraeli, limodzi ndi nsembe zawo zonse zoweyula*+ zimene azipereka monga zopereka zawo,+ zizikhala zako. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna, limodzi ndi ana ako aakazi.+ Zikhale gawo lanu mpaka kalekale. Aliyense wa m’nyumba yako amene ndi wosadetsedwa azidya nawo.+ 12  “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+ 13  Zipatso zonse zoyamba kupsa m’minda yawo, zimene azizipereka kwa Yehova zizikhala zako.+ Aliyense wa m’nyumba yako amene ndi wosadetsedwa azidya nawo. 14  “Chinthu chilichonse chimene anthu apatulira Mulungu mu Isiraeli chizikhala chako.+ 15  “Chamoyo chilichonse chotsegula mimba ya mayi ake,+ chimene chiziperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu kapena nyama, chizikhala chako. Komabe, uzionetsetsa kuti ukuwombola mwana woyamba kubadwa wa munthu.+ Uziwombolanso+ mwana woyamba kubadwa wa nyama yodetsedwa. 16  Mwanayo uzimuwombola ndi dipo akakwanitsa mwezi umodzi kapena kuposerapo. Uzimuwombola ndi mtengo woikidwiratu, masekeli asiliva asanu, malinga ndi sekeli la kumalo oyera,+ lofanana ndi magera+ 20. 17  Koma usawombole ng’ombe yamphongo yoyamba kubadwa, mwana wa nkhosa wamphongo woyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa.+ Zimenezi ndi zopatulika. Magazi+ ake uziwawaza paguwa lansembe, ndipo mafuta ake uziwafukiza pamoto monga nsembe yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ 18  Uzitenga nyama yake kuti ikhale yako, mofanana ndi nganga ya nsembe yoweyula, komanso mwendo wam’mbuyo wakumanja.+ 19  Zopereka zonse zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova, ndakupatsa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi, ngati gawo lanu mpaka kalekale.+ Limeneli ndi pangano losatha* limene lidzakhala mpaka kalekale pakati pa Yehova ndi iwe ndi mbadwa zako.”+ 20  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni, kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa m’dziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa gawo lililonse pakati pawo.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Isiraeli.+ 21  “Kunena za ana a Levi, iwo ndawapatsa chakhumi+ chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo umene akuchita, utumiki wa pachihema chokumanako. 22  Ana a Isiraeli asadzayandikirenso chihema chokumanako, kuti angadzachimwe n’kufa.+ 23  Aleviwo azichita utumiki wawo pachihema chokumanako, ndipo ndiwo amene azisenza zolakwa za anthuwo.+ Iwo asakhale ndi cholowa+ pakati pa ana a Isiraeli. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale m’mibadwo yanu yonse. 24  Chakhumi chimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova monga chopereka, ndawapatsa Alevi monga cholowa chawo. N’chifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa ana a Isiraeli.’”+ 25  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 26  “Lankhula ndi Alevi, uwauze kuti, ‘Muzilandira kwa ana a Isiraeli chakhumi chimene ndakupatsani monga cholowa+ chanu. Ndipo pachakhumi chimene muzilandiracho, muziperekapo chopereka chanu kwa Yehova, chakhumi cha chakhumicho.+ 27  Chakhumicho ndicho chizikhala chopereka chanu, monga cha tirigu wochokera pamalo popunthira,+ ndi cha vinyo wochuluka wochokera mopondera mphesa, kapena cha mafuta ochuluka ochokera m’chofinyira mafuta. 28  Mwa njira imeneyi, inunso muzipereka chopereka chanu kwa Yehova. Muzipereka kuchokera pazakhumi zonse zimene muzilandira kuchokera kwa ana a Isiraeli. Kuchokera pazakhumizo, muzipereka chopereka chanu kwa Yehova mwa kupatsa wansembe Aroni. 29  Pamphatso zonse zosiyanasiyana zoperekedwa kwa inu, inunso muziperekapo chopereka kwa Yehova. Muzipereka gawo lake labwino koposa,+ monga chinthu chopatulika chimene iwo apereka.’ 30  “Ndipo uwauze kuti, ‘Mukapereka zabwino koposa za zoperekazo,+ zotsalazo zizikhala za Alevinu, monga tirigu wochokera popunthira, vinyo wochokera mopondera mphesa, kapena mafuta ochokera m’chofinyira mafuta. 31  Inuyo ndi a m’nyumba zanu muzidya zimenezo pamalo alionse, chifukwa ndizo malipiro anu pa utumiki umene muzichita m’chihema chokumanako.+ 32  Musachimwe polephera kupereka gawo labwino koposa la zinthuzo, ndipo musaipitse zinthu zopatulika za ana a Isiraeli, kuti mungafe.’”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.
Mawu ake enieni, “pangano la mchere.”