Numeri 16:1-50

16  Tsopano Kora+ mwana wa Izara,+ mwana wa Kohati,+ mwana wa Levi,+ anagwirizana ndi adzukulu a Rubeni,+ omwe ndi Datani+ ndi Abiramu+ ana a Eliyabu,+ komanso Oni mwana wa Pelete, kuti aukire.  Iwo anaukira Mose. Oukirawo anali limodzi ndi amuna achiisiraeli okwanira 250. Iwowa anali atsogoleri a anthuwo, owaimira kumisonkhano, amuna otchuka.  Choncho iwo anasonkhana n’kuyamba kutsutsana+ ndi Mose ndi Aroni, kuti: “Tatopa nanu tsopano! Khamu lonseli ndi loyera,+ ndipo Yehova ali pakati pawo.+ Nanga n’chifukwa chiyani inu mukudzikweza pa mpingo wa Yehova?”+  Mose atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.  Ndiyeno Mose analankhula ndi Kora ndiponso khamu lonselo, kuti: “Mawa m’mawa, Yehova aonetsa amene ali wake+ ndiponso amene ali woyera.+ Aonetsa amene ayenera kuima pamaso pake,+ ndipo amene ati am’sankheyo+ adzaima pamaso pake.  Mudzachite izi: Iwe Kora ndi khamu lonselo,+ mudzatenge zofukizira.+  M’zofukizirazo mudzaikemo moto ndiponso zofukiza ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova mawa. Munthu amene Yehova ati adzamusankhe,+ ameneyo ndiye woyera. Inenso ndatopa nanu, inu ana a Levi!”+  Ndipo Mose anapitiriza kulankhula ndi Kora, kuti: “Tamverani, inu ana a Levi.  Kodi amuna inu mukuyesa n’chinthu chaching’ono kuti Mulungu wa Isiraeli anakupatulani+ pakati pa Aisiraeli, n’kukutengani kukhala akeake, kuti muzitumikira Yehova pachihema chake ndi kutumikira khamulo?+ 10  Kodi ndi chinthu chaching’ono kuti Mulungu anakuyandikizani kwa iye, limodzi ndi abale anu onse, ana a Levi? Kodi tsopano anthu inu mukufunanso udindo waunsembe?+ 11  Zimene mukuchitazi, iweyo limodzi ndi khamu lako lonseli, mukuukira Yehova.+ Kunena za Aroni, kodi iye ndani kuti amuna inu mum’dandaule?”+ 12  Pambuyo pake, Mose anatuma mthenga kukaitana Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu. Koma iwo anayankha kuti: “Ife sitibwerako kumeneko!+ 13  Kodi ukuyesa n’chinthu chaching’ono kuti unatichotsa kudziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphere m’chipululu muno,+ kutinso ukhale ngati mfumu yomatilamula?+ 14  Si izi nanga, sunatifikitse kudziko lililonse loyenda mkaka ndi uchi,+ kumene ungatigawire malo ndiponso minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuti amunawo uwakolowole maso? Tatitu kumeneko sitibwerako!” 15  Mose atamva zimenezi anakwiya kwambiri, ndipo anauza Yehova kuti: “Nsembe zawo zambewu musaziyang’ane.+ Ine sindinawalande ngakhale bulu mmodzi wamphongo, kapena kuchitira choipa aliyense wa iwo.”+ 16  Kenako Mose anauza Kora+ kuti: “Mawa, iweyo ndi khamu lako lonse mukaonekere pamaso pa Yehova.+ Mukaonekere, iweyo limodzi ndi khamulo, ndi Aroni. 17  Aliyense akatenge chofukizira chake. Mukaikemo nsembe yofukiza, ndipo aliyense adzabweretse chofukizira chake pamaso pa Yehova. Zofukizirazo zidzakhalepo zokwanira 250, komanso iweyo ndi Aroni aliyense adzakhale ndi chake.” 18  Choncho aliyense wa iwo anatenga chofukizira chake n’kuikamo moto ndi nsembe yofukiza. Atatero, anakaimirira pakhomo la chihema chokumanako limodzi ndi Mose ndi Aroni. 19  Kora atasonkhanitsa khamu+ lonse lotsutsana nawo pakhomo la chihema chokumanako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa khamu lonselo.+ 20  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndiponso Aroni, kuti: 21  “Chokani+ pakati pa khamu ili, kuti ndiwafafanize+ kamodzi n’kamodzi.” 22  Anthuwo atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, n’kunena kuti: “Chonde Mulungu, inu Mulungu amene amapereka moyo kwa zamoyo zonse,+ kodi kuchimwa kwa munthu mmodzi yekha n’kumene mungapsere mtima khamu lonseli?”+ 23  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 24  “Uza khamulo kuti, ‘Chokani kumahema a Kora, Datani ndi Abiramu!’”+ 25  Kenako Mose ananyamuka n’kupita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akulu+ a Isiraeli anapita naye limodzi. 26  Atafika anauza khamulo kuti: “Chonde, chokani kumahema a anthu oipawa, ndipo musakhudze chinthu chawo chilichonse,+ kuti musaphedwe nawo limodzi chifukwa cha kuchimwa kwawo.” 27  Nthawi yomweyo anthuwo anachoka kumbali zonse za mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Zitatero, Datani ndi Abiramu anatuluka n’kuima pamakomo a mahema awo,+ limodzi ndi akazi awo, ana awo. 28  Ndiyeno Mose anati: “Mudziwira izi kuti Yehova ndiye anandituma kuti ndichite zonsezi,+ ndiponso kuti si za mumtima mwanga ayi:+ 29  Ngati anthuwa angafe mmene anthu onse amafera, ndipo ngati angalangidwe ndi chilango cha anthu,+ pamenepo, ndiye kuti sindinatumidwe ndi Yehova.+ 30  Koma ngati angafe ndi chinthu chachilendo chimene Yehova achite,+ kuti nthaka iyasame n’kuwameza iwo+ ndi zonse ali nazo, moti iwo n’kutsikira ku Manda*+ ali amoyo, pamenepo mudziwa ndithu kuti amunawa anyoza+ Yehova.” 31  Mose atangomaliza kulankhula mawu amenewa, nthaka imene iwo anapondapo inayamba kung’ambika.+ 32  Nthakayo inatsegula pakamwa pake n’kuwameza iwowo ndi mabanja awo, limodzi ndi anthu ena onse amene anali kumbali ya Kora, komanso katundu wawo yense.+ 33  Chotero iwo analowa m’nthaka, limodzi ndi onse amene anali kumbali yawo. Iwo anatsikira ku Manda ali amoyo. Nthakayo inawafotsera,+ moti iwo anafafanizika pakati pa mpingo wonse.+ 34  Pamenepo, Aisiraeli onse amene anali pamalopo anayamba kuthawa atamva kufuula kwawo, ndipo anati: “Tikuopa kuti nthaka ingatimeze nafenso!”+ 35  Ndiyeno panabuka moto wochokera kwa Yehova,+ umene unapsereza amuna 250 omwe anali kupereka nsembe zofukiza+ aja. 36  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 37  “Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse zofukizira+ pamotowo, ‘Ndipo umwaze makalawo. Zofukizirazo n’zopatulika, 38  zofukizira za amuna amene anafa+ chifukwa cha kuchimwa. Azisule kuti zikhale timalata topyapyala n’kukutira nato guwa lansembe,+ popeza anafika nazo pamaso pa Yehova, ndipo zakhala zopatulika. Timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli.’”+ 39  Chotero, wansembe Eleazara anatenga zofukizira+ zamkuwa zimene anabwera nazo anthu amene anapsa ndi moto aja, ndipo anazisula n’kuzipanga timalata tokutira guwa lansembe. 40  Eleazara anachita izi kuti timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli, kuti munthu aliyense amene si mbadwa+ ya Aroni asayandikire kwa Yehova+ kukafukiza nsembe. Anateronso kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi gulu lake+ anachita. Eleazara anachita zonse monga mmene Yehova anamuuzira kudzera kwa Mose. 41  Koma tsiku lotsatira, khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose ndi Aroni,+ kuti: “Mwapha anthu a Yehova inu.” 42  Khamulo litasonkhana pamodzi kuti liukire Mose ndi Aroni, linacheukira kuchihema chokumanako. Anthuwo anangoona kuti mtambo waphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova wayamba kuonekera.+ 43  Tsopano Mose ndi Aroni anakaima patsogolo pa chihema chokumanako.+ 44  Pamenepo Yehova analankhula ndi Mose, kuti: 45  “Amuna inu, chokani pakati pa khamuli kuti ndilifafanize kamodzi n’kamodzi.”+ Atamva zimenezi, iwo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 46  Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Tenga chofukizira uikemo moto wochokera paguwa lansembe.+ Uikemo nsembe yofukiza n’kupita kwa khamulo mofulumira kuti ukawaphimbire machimo awo.+ Chita zimenezi chifukwa Yehova wakwiya kwambiri.+ Mliritu wayamba kale!” 47  Nthawi yomweyo Aroni anatenga chofukiziracho monga anamuuzira Mose, n’kuthamanga kukalowa pakati pa mpingowo. Koma mliri unali utayamba kale pakati pawo. Choncho Aroni anaika nsembe ija pamoto n’kuyamba kuwaphimbira machimo anthuwo. 48  Aroni anaimabe chilili pakati pa akufa ndi amoyo.+ Kenako mliriwo unaleka.+ 49  Amene anaphedwa ndi mliriwo anakwana 14,700, kupatula amene anaphedwa chifukwa cha Kora aja. 50  Pamapeto pake, pamene Aroni anabwerera kwa Mose pakhomo la chihema chokumanako, mliriwo unali utaleka.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.