Numeri 1:1-54

1  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose m’chipululu cha Sinai,+ m’chihema chokumanako.+ Analankhula naye pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri m’chaka chachiwiri, atatuluka m’dziko la Iguputo.+ Iye anati:  “Uwerenge+ khamu lonse la ana a Isiraeli malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, n’kulemba mayina awo. Uwerenge amuna onse, mmodzi ndi mmodzi.  Uwerenge kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ aliyense woyenerera kupita kunkhondo pakati pa Aisiraeli.+ Iweyo ndi Aroni muwalembe m’kaundula malinga ndi magulu awo a asilikali.  “Mukhale ndi amuna ena okuthandizani, mwamuna mmodzi pafuko lililonse. Aliyense akhale woti ndi mtsogoleri wa nyumba ya makolo ake.+  Nawa mayina a amuna amene akuthandizeni: Kuchokera ku fuko la Rubeni,+ Elizuri+ mwana wa Sedeuri,  kuchokera ku fuko la Simiyoni,+ Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai,  kuchokera ku fuko la Yuda,+ Naasoni+ mwana wa Aminadabu,  kuchokera ku fuko la Isakara,+ Netaneli+ mwana wa Zuwara,  kuchokera ku fuko la Zebuloni,+ Eliyabu+ mwana wa Heloni. 10  Mwa ana a Yosefe+ kuchokera ku fuko la Efuraimu,+ Elisama mwana wa Amihudi, kuchokera ku fuko la Manase,+ Gamaliyeli mwana wa Pedazuri, 11  kuchokera ku fuko la Benjamini,+ Abidana+ mwana wa Gidoni, 12  kuchokera ku fuko la Dani,+ Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai, 13  kuchokera ku fuko la Aseri,+ Pagiyeli+ mwana wa Okirani, 14  kuchokera ku fuko la Gadi,+ Eliyasafu+ mwana wa Deyueli,+ 15  kuchokera ku fuko la Nafitali,+ Ahira+ mwana wa Enani. 16  Amenewa ndiwo osankhidwa a khamu la anthuwo, atsogoleri a mafuko+ a makolo awo. Aliyense wa iwo ndi mtsogoleri wa anthu masauzande mu Isiraeli.”+ 17  Choncho Mose ndi Aroni anatengadi amuna amene anatchulidwa mayinawo. 18  Atatero, anasonkhanitsa anthu onse pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri. Anawasonkhanitsa n’cholinga chakuti awalembe m’kaundula+ kuti adziwe mibadwo yawo malinga ndi mabanja awo, ndiponso nyumba za makolo awo. Anawalemba mayina kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ mmodzi ndi mmodzi. 19  Chotero Mose anawerenga anthuwo+ m’chipululu cha Sinai, monga mmene Yehova anamulamulira. 20  Mbadwa za Rubeni, mwana woyamba wa Isiraeli,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba amuna onse kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 21  Onse olembedwa mayina a fuko la Rubeni anakwana 46,500.+ 22  Mbadwa za Simiyoni,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba amuna onse kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 23  Onse olembedwa mayina a fuko la Simiyoni analipo 59,300.+ 24  Mbadwa za Gadi,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 25  Onse olembedwa mayina a fuko la Gadi+ analipo 45,650.+ 26  Mbadwa za Yuda,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 27  Onse olembedwa mayina a fuko la Yuda analipo 74,600.+ 28  Mbadwa za Isakara,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 29  Onse olembedwa mayina a fuko la Isakara analipo 54,400.+ 30  Mbadwa za Zebuloni,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 31  Onse olembedwa mayina a fuko la Zebuloni analipo 57,400.+ 32  Mbadwa za Yosefe za fuko la Efuraimu+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 33  Onse olembedwa mayina a fuko la Efuraimu+ analipo 40,500.+ 34  Mbadwa za Manase+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 35  Onse olembedwa mayina a fuko la Manase analipo 32,200.+ 36  Mbadwa za Benjamini,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 37  Onse olembedwa mayina a fuko la Benjamini analipo 35,400.+ 38  Mbadwa za Dani,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 39  Onse olembedwa mayina a fuko la Dani analipo 62,700.+ 40  Mbadwa za Aseri,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 41  Onse olembedwa mayina a fuko la Aseri analipo 41,500.+ 42  Mbadwa za Nafitali,+ anazilemba mayina malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo. 43  Onse olembedwa mayina a fuko la Nafitali analipo 53,400.+ 44  Amenewa ndi amene analembedwa mayina, amene Mose ndi Aroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri 12, amuna achiisiraeli. Aliyense wa amunawa anaimira nyumba za makolo ake. 45  Choncho ana a Isiraeli onse olembedwa mayina malinga ndi nyumba za makolo awo, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo pakati pa Aisiraeli, 46  onse amene analembedwa mayina anakwana 603,550.+ 47  Koma Alevi+ malinga ndi fuko la makolo awo sanawawerengere pamodzi ndi enawo.+ 48  Sanawawerenge chifukwa Yehova anali atauza Mose kuti: 49  “A fuko la Levi okha usawalembe mayina, ndipo usawawerengere pamodzi ndi ana a Isiraeli enawo.+ 50  Iweyo uike Aleviwo kukhala oyang’anira chihema cha Umboni+ ndi ziwiya zake zonse, ndi chilichonse cha mmenemo.+ Iwowo ndi amene azinyamula chihema chopatulikacho ndi ziwiya zake zonse.+ Ndi amenenso azitumikira+ pachihemapo, ndipo azimanga misasa yawo mochizungulira.+ 51  Pa nthawi yosamutsa chihema chopatulika, Aleviwo azichipasula,+ ndipo mukafika pomanga msasa, iwo ndiwo azimanga chihemacho. Aliyense amene si Mlevi akayandikira chihemacho aziphedwa.+ 52  “Ana a Isiraeli azimanga mahema awo, aliyense malinga ndi msasa wawo, munthu aliyense malinga ndi gulu lake la mafuko atatu,+ malinga ndi magulu awo a asilikali. 53  Alevi azimanga mahema awo mozungulira chihema cha Umboni kuti mkwiyo+ wa Mulungu usawayakire ana a Isiraeli. Aleviwo azitumikira pachihema cha Umbonicho.”+ 54  Ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose. Anachitadi momwemo.+

Mawu a M'munsi