Numeri 32:1-42

32  Tsopano ana a Rubeni+ ndi ana a Gadi+ anakhala ndi ziweto zambiri, zankhaninkhani. Iwo anayamba kusirira dziko la Yazeri+ ndi la Giliyadi, ndipo deralo linalidi malo abwino a ziweto.  Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo anafika kwa Mose, wansembe Eleazara, ndi atsogoleri a khamulo, n’kuwauza kuti:  “Midzi ya Ataroti,+ Diboni,+ Yazeri, Nimira,+ Hesiboni,+ Eleyale,+ Sebamu, Nebo,+ ndi Beoni,+  ndilo dziko limene Yehova anagonjetsera+ khamu la Isiraeli. Dziko limeneli n’labwino kwa ziweto, ndipo atumiki anufe ziweto tili nazo.”+  Anapitiriza kunena kuti: “Ngati mungatikomere mtima atumiki anufe, mutipatse dzikolo ngati cholowa chathu. Tisawoloke nawo Yorodano.”+  Koma Mose poyankha, anafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo kuti: “Mukuti abale anu apite kunkhondo inuyo mutsale kuno?+  N’chifukwa chiyani mukufuna kuwatayitsa mtima ana a Isiraeli, kuti asawolokere kudziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa?  N’zimenenso makolo anu anachita+ ku Kadesi-barinea,+ pamene ndinawatuma kuti akazonde dziko.  Iwo atafika kuchigwa* cha Esikolo+ n’kuliona dzikolo, anatayitsa mtima ana a Isiraeli, kuti asakalowe m’dziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa.+ 10  Pa tsiku limenelo Yehova anakwiya koopsa, ndipo analumbira+ kuti, 11  ‘Amuna amene anatuluka mu Iguputo kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ sadzaiona nthaka imene ndinalumbirira Abulahamu, Isaki ndi Yakobo,+ chifukwa sanandimvere ndi mtima wonse. 12  Koma Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, adzaiona nthakayo chifukwa akhala akumvera Yehova ndi mtima wonse.’ 13  Yehova anawakwiyira koopsa Aisiraeli ndipo anawachititsa kuzungulira m’chipululu zaka 40,+ mpaka m’badwo wonse wochita zoipa pamaso pa Yehova utatha.+ 14  Inunso mukukhala kam’badwo ka anthu ochita zoipa mofanana ndi makolo anu, kuti muwonjezere mkwiyo woyaka moto wa Yehova+ pa Isiraeli. 15  Mukaleka kumumvera,+ ndithu iye adzachititsanso anthu onsewa kukhalabe m’chipululu muno,+ ndipo mudzawazunzitsa kwambiri.”+ 16  Kenako iwo anafikanso kwa iye n’kunena kuti: “Mutilole timange makola amiyala a ziweto zathu kunoko, ndi mizinda ya ana athu aang’ono. 17  Ifeyo tinyamula zida zathu n’kufola mwa dongosolo lomenyera nkhondo+ ndipo titsogolera ana a Isiraeli kunkhondo mpaka tikawafikitse kumalo awo. Koma ana athu aang’ono tiwasiye m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kuti tiwateteze kwa anthu a dziko lino. 18  Sitidzabwerera kunyumba zathu mpaka aliyense wa ana a Isiraeli atapeza malo ake monga cholowa chake.+ 19  Ife sitidzalandira nawo cholowa tsidya ilo la Yorodano kupita kutsogoloko, chifukwa cholowa chathu chili tsidya lino la Yorodano, kum’mawa kuno.”+ 20  Pamenepo Mose anawauza kuti: “Muchitedi zimenezo. Mutenge zida n’kukonzekera kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova.+ 21  Aliyense wokonzekera nkhondo awoloke Yorodano pamaso pa Yehova, kufikira iye atapitikitsa adani ake pamaso pake,+ 22  mpaka dzikolo litagonjetsedwa pamaso pa Yehova.+ Pambuyo pake mudzabwerere.+ Ngati muchitadi zimenezi, mudzakhala opanda mlandu kwa Yehova ndi kwa Isiraeli. Ndipo dzikoli lidzakhaladi lanu, monga cholowa chanu pamaso pa Yehova.+ 23  Koma mukapanda kuchita zimenezo, ndithu mudzachimwira Yehova.+ Ndipo mukatero, dziwani kuti tchimo lanu lidzakutsatani.+ 24  Mizinda ya ana anu aang’ono, ndi makola amiyala a ziweto zanu, mangani. Koma zonse zimene mwalonjeza muchitedi.”+ 25  Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anamuyankha Mose kuti: “Atumiki anufe tichita zonse zimene mwalamula mbuyathu.+ 26  Ana athu aang’ono ndi akazi athu atsala kuno m’mizinda ya Giliyadi, limodzi ndi ziweto zathu zonse.+ 27  Koma atumiki anufe tiwoloka, aliyense atakonzekera kukamenya nkhondo+ pamaso pa Yehova, monga mwanenera mbuyathu.” 28  Chotero Mose anapereka lamulo lonena za iwowo kwa wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli. 29  Iye anawauza kuti: “Ana a Gadi ndi ana a Rubeni akawoloka nanu Yorodano, aliyense wokonzekera kukamenya nkhondo+ pamaso pa Yehova, ndipo ngati dzikolo lidzagonjetsedwa pamaso panu, pamenepo mudzawapatse dziko la Giliyadi monga cholowa chawo.+ 30  Koma akapanda kukonzekera nkhondo ndi kuwoloka nanu, basi azikakhala pakati panu m’dziko la Kanani.”+ 31  Ana a Gadi ndi ana a Rubeni atamva mawuwo anati: “Tidzachita zimene Yehova walankhula kwa atumiki anufe.+ 32  Tidzawoloka ndi zida kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova kudziko la Kanani.+ Ndipo tidzalandira cholowa chathu tsidya lino la Yorodano.”+ 33  Pamenepo Mose anagawira malo ana a Gadi+ ndi ana a Rubeni.+ Anagawiranso malo hafu ya fuko la Manase+ mwana wa Yosefe. Anawagawira malo a ufumu wa Sihoni+ mfumu ya Aamori, ndi a ufumu wa Ogi+ mfumu ya Basana, dera lonse la mizinda ndi midzi yozungulira. 34  Tsopano ana a Gadi anayamba kumanga mizinda ya Diboni,+ Ataroti,+ Aroweli,+ 35  Atiroti-sofani, Yazeri,+ Yogebeha,+ 36  Beti-nimira,+ ndi Beti-harana.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri,+ komanso inali ndi makola a ziweto amiyala.+ 37  Ana a Rubeni anamanga mizinda ya Hesiboni,+ Eleyale,+ Kiriyataimu,+ 38  Nebo,+ Baala-meoni,+ ndi Sibima. Mayina a mizindayi anawasintha, n’kuipatsa mayina ena atsopano. 39  Kenako ana a Makiri+ mwana wa Manase, ananyamuka ulendo wopita kumzinda wa Giliyadi. Analanda mzindawo ndi kupitikitsa Aamori amene anali kukhalamo. 40  Choncho Mose anapereka mzinda wa Giliyadi kwa Makiri mwana wa Manase, ndipo iye anayamba kukhala mmenemo.+ 41  Yairi mwana wa Manase ananyamuka ulendo wokalanda midzi yawo ing’onoing’ono. Midzi imeneyi anaitcha kuti Havoti-yairi.+ 42  Noba nayenso ananyamuka ulendo wokalanda mzinda wa Kenati+ ndi midzi yake yozungulira. Mzindawo anaupatsa dzina lake, loti Noba.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.