Machitidwe 21:1-40

21  Tsopano titadzikakamiza kulekana nawo n’kuyamba ulendo wathu wa panyanja, tinayenda molunjika mpaka kufika ku Ko. Koma tsiku lotsatira tinafika ku Rode, ndipo titachoka kumeneko tinakafika ku Patara.  Kumeneko tinapeza ngalawa imene inali kuwolokera ku Foinike, ndipo tinakwera ndi kunyamuka.  Chilumba cha Kupuro+ chitayamba kuonekera, tinachisiya kumanzere ndi kupitiriza ulendo wathu kulowera ku Siriya.+ Tinaima ku Turo, chifukwa kumeneko ngalawa inafunika kutsitsa katundu.+  Titafufuza tinapeza ophunzira ndi kukhala nawo kumeneko masiku 7. Koma mouziridwa ndi mzimu,+ iwo anauza Paulo mobwerezabwereza kuti asakaponde mu Yerusalemu.  Choncho titatsiriza masikuwo, tinanyamuka kuti tipitirize ulendo wathu. Ndipo abale onse, pamodzi ndi amayi ndi ana, anatiperekeza mpaka kunja kwa mzindawo. Kumeneko tinagwada+ pagombe ndi kupemphera  n’kutsanzikana.+ Kenako ife tinakwera ngalawa ndipo iwo anabwerera kunyumba zawo.  Choncho tinanyamuka ku Turo pangalawa ndipo tinafika ku Tolemayi. Kumeneko tinalonjerana ndi abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi.  M’mawa mwake tinanyamuka ndi kukafika ku Kaisareya.+ Kumeneko tinakalowa m’nyumba ya mlaliki* Filipo. Iyeyu anali mmodzi wa amuna 7 a mbiri yabwino aja,+ ndipo tinakhala naye.  Mwamuna ameneyu anali ndi ana aakazi anayi, anamwali, amene anali kunenera.+ 10  Koma titakhala masiku ndithu, mneneri wina dzina lake Agabo+ anafika kumeneko kuchokera ku Yudeya. 11  Iye anafika kwa ife ndi kutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja ndi kunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga+ chonchi ku Yerusalemu ndi kumupereka+ m’manja mwa anthu a mitundu ina.’” 12  Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu akumeneko, tinayamba kuchonderera Paulo kuti asapite+ ku Yerusalemu. 13  Koma Paulo anayankha kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira+ ndi kunditayitsa mtima?+ Dziwani kuti ine ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa+ ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14  Titalephera kumusintha maganizo, tinangovomereza ndi kunena kuti: “Chifuniro+ cha Yehova chichitike.” 15  Masiku amenewa atapita, tinakonzekera ulendo ndipo tinanyamuka kulowera ku Yerusalemu.+ 16  Koma ophunzira ena a ku Kaisareya+ ananyamuka nafe, kuti atiperekeze kunyumba ya munthu wina kuti tikafikire kumeneko. Munthu ameneyu dzina lake linali Mnaso wa ku Kupuro, ndipo anali mmodzi wa ophunzira oyambirira. 17  Titafika ku Yerusalemu,+ abale anatilandira mokondwa.+ 18  Koma tsiku lotsatira, Paulo anapita nafe kwa Yakobo,+ ndipo akulu onse anali komweko. 19  Paulo anawalonjera ndi kuyamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane+ zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.+ 20  Iwo atamva zimenezi anayamba kutamanda Mulungu, ndipo anamuuza kuti: “M’bale, kodi ukuona kuchuluka kwa okhulupirira amene ali pakati pa Ayuda? Ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo.+ 21  Komatu iwo amva mphekesera zakuti iwe wakhala ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti apandukire Chilamulo cha Mose.+ Akuti ukuwauza kuti asamachite mdulidwe+ wa ana awo kapena kutsatira miyambo imene takhala tikuitsatira kuyambira kale. 22  Tsopano tichite chiyani pamenepa? Sitikukayikira kuti iwo adzamva ndithu kuti iwe wafika. 23  Choncho uchite zimene tikuuze pano: Tili ndi amuna anayi amene anachita lumbiro. 24  Utenge amuna amenewa+ ndipo ukachite mwambo wa kudziyeretsa pamodzi ndi iwo. Uwalipirire zonse zofunika,+ kuti amete tsitsi lawo.+ Ukatero, aliyense adzadziwa kuti mphekesera zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa chabe. Adzaona kuti ukuchita zinthu motsatira dongosolo, komanso kuti umasunga Chilamulo.+ 25  Koma kwa okhulupirira ochokera mwa anthu a mitundu inawo, tinawatumizira chigamulo chathu chakuti apewe zoperekedwa nsembe kwa mafano+ komanso magazi,+ zopotola,+ ndi dama.”+ 26  Choncho Paulo anatenga amunawo tsiku lotsatira ndi kukachita mwambo wa kudziyeretsa pamodzi ndi iwo.+ Kenako analowa m’kachisi, kukanena pamene masiku awo a mwambo wa kudziyeretsa adzathere,+ ndi pamene aliyense wa iwo adzamuperekere nsembe.+ 27  Ali pafupi kutsiriza masiku 7,+ Ayuda ochokera ku Asia anaona Paulo ali m’kachisi. Chotero anayambitsa chisokonezo+ m’khamu lonse la anthu ndipo anamugwira. 28  Iwo anali kufuula kuti: “Inu Aisiraeli, tithandizeni! Munthu amene akuphunzitsa zotsutsana ndi anthu a mtundu wathu kulikonse ndi ameneyu.+ Iyeyu akuphunzitsa zotsutsana ndi Chilamulo komanso malo ano. Kuwonjezera pamenepo, inu mukudziwa kuti anatenga Agiriki n’kudzawalowetsa m’kachisi ndipo waipitsa malo oyera ano.”+ 29  Iwo ananena zimenezi chifukwa tsiku lina anaona Terofimo+ wa ku Efeso ali naye limodzi mumzindawo. Atawaona anaganiza kuti Paulo analowetsa Terofimo m’kachisi. 30  Chotero munali chisokonezo mumzinda wonsewo, ndipo anthu anali balalabalala+ kuthamangira kukachisiko. Kenako anagwira Paulo ndi kumukokera kunja kwa kachisi.+ Nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31  Ndipo pamene anali kufuna kumupha, uthenga unafika kwa mtsogoleri wa gulu la asilikali kuti mu Yerusalemu monse muli chisokonezo.+ 32  Mwamsanga, iye anatenga asilikali ndi akapitawo awo ndi kuthamangira kumeneko.+ Anthuwo ataona mkulu wa asilikali+ uja pamodzi ndi asilikali akewo, analeka kumenya Paulo. 33  Pamenepo mkulu wa asilikali uja anafika pafupi ndi kumugwira ndipo analamula kuti amumange ndi maunyolo awiri.+ Ndiyeno anafunsa za iye kuti anali ndani ndiponso zimene anachita. 34  Koma ena m’khamulo anayamba kufuula zinthu zina, enanso zina.+ Choncho, atalephera kutolapo mfundo yeniyeni chifukwa cha phokoso, analamula kuti apite naye kumpanda wa asilikali.+ 35  Ndiyeno atafika pamasitepe, asilikaliwo anachita kumunyamula chifukwa chakuti khamulo linali kuchita chiwawa. 36  Khamu la anthu linali kuwatsatira, likufuula kuti: “Aphedwe ameneyo!”+ 37  Koma atatsala pang’ono kulowa naye kumpanda wa asilikali, Paulo anauza mkulu wa asilikali kuti: “Mungandilole kodi kulankhula nanu pang’ono?” Iye anati: “Kodi umalankhula Chigiriki? 38  Kodi si iwe Mwiguputo uja amene masiku apitawo unayambitsa chipolowe choukira boma+ ndi kutsogolera zigawenga 4,000 kupita nazo m’chipululu?” 39  Pamenepo Paulo ananena kuti: “Inetu ndine Myuda+ wa ku Tariso,+ ku Kilikiya, nzika ya mzinda wotchuka. Chonde ndikukupemphani, kuti mundilole ndilankhule kwa anthuwa.” 40  Atamulola, Paulo anaimirira pamasitepe ndi kukwezera anthuwo dzanja.+ Onse atakhala phee, analankhula nawo m’Chiheberi,+ kuti:

Mawu a M'munsi

“Mlaliki” palembali akutanthauza “mmishonale.”