Machitidwe 2:1-47

2  Tsopano pa tsiku la chikondwerero cha Pentekosite,+ onse anali atasonkhana pamalo amodzi.  Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza m’nyumba yonse imene iwo anakhalamo.+  Pamenepo anaona malawi amoto ooneka ngati malilime,+ ndipo anagawanika ndi kukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi.  Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana,+ monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.  Pa nthawiyo mu Yerusalemu munali kukhala Ayuda ena,+ anthu oopa Mulungu,+ ochokera mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo.  Choncho mkokomo umenewu utamveka, panasonkhana khamu la anthu ambiri. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense wa iwo anawamva akulankhula m’chinenero chake.  Ndithudi, izi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsa mothedwa nzeru kuti: “Taonani anthuni, kodi onse akulankhulawa si Agalileya?+  Nanga zikutheka bwanji kuti aliyense wa ife azimva chinenero chimene anabadwa nacho?  Pakati pathu pali Apati, Amedi,+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya,+ ku Kapadokiya,+ ku Ponto+ ndi kuchigawo cha Asia.+ 10  Pali anthu ochokera ku Fulugiya,+ ku Pamfuliya,+ ku Iguputo ndi kumadera a Libiya amene ali kufupi ndi Kurene. Palinso alendo ochokera ku Roma, amene ndi Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda,+ 11  komanso Akerete+ ndi Aluya.+ Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu m’zinenero zathu.” 12  Inde, onse anadabwa kwambiri ndi kuthedwa nzeru, n’kumafunsana kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” 13  Koma ena anali kuwaseka n’kumanena kuti: “Aledzera vinyo watsopano amenewa.”+ 14  Koma Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja.+ Iye analankhula nawo mokweza mawu kuti: “Anthu inu a m’Yudeya ndi inu nonse okhala m’Yerusalemu,+ dziwani ndi kutchera khutu ku zimene ndikufuna kukuuzani pano. 15  Sikuti anthu awa aledzera+ ngati mmene inu mukuganizira ayi, chifukwa nthawi panopa ndi 9 koloko m’mawa.* 16  Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: 17  ‘“Ndipo m’masiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga+ pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+ 18  Ndidzatsanuliranso mbali ya mzimu wanga ngakhale pa akapolo anga aamuna ndi aakazi m’masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.+ 19  Ndidzachita zodabwitsa kuthambo ndi zizindikiro padziko lapansi. Ndidzachititsa kuti pakhale magazi, moto ndi mtambo wautsi.+ 20  Dzuwa+ lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndi laulemerero la Yehova* lisanafike.+ 21  Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”’+ 22  “Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu Mnazareti,+ ndi munthu amene Mulungu anamuonetsera poyera kwa inu. Anatero mwa ntchito zamphamvu,+ mwa zodabwitsa komanso mwa zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ monga mmene inunso mukudziwira. 23  Munthu ameneyu, monga woperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu ndi kudziwiratu kwake zam’tsogolo,+ ndi amene inu munamukhomerera pamtengo ndi kumupha kudzera mwa anthu osamvera malamulo.+ 24  Koma Mulungu anamuukitsa+ kwa akufa mwa kumasula zopweteka za imfa,+ chifukwa zinali zosatheka kuti imfa ipitirize kumugwira mwamphamvu.+ 25  Ponena za iyeyu, pajatu Davide anati, ‘Ndinali kuona Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka ngakhale pang’ono.+ 26  Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unakondwera ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso, ine ndidzakhala ndi chiyembekezo,+ 27  chifukwa simudzasiya moyo wanga m’Manda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.+ 28  Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo chifukwa cha nkhope yanu ndidzakhala ndi chimwemwe chosefukira.’+ 29  “Amuna inu, abale anga, ndilankhula ndithu mwaufulu za kholo lathu Davide. Iye anamwalira+ ndi kuikidwa m’manda, ndipo manda ake tili nawo mpaka lero. 30  Iye anali mneneri, ndipo anali kudziwa kuti Mulungu anam’lonjeza mwa lumbiro, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi mwa zipatso za m’chiuno mwake.+ 31  Choncho pokhala mneneri, iye anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka kwa Khristu. Ananeneratu kuti iye sanasiyidwe m’Manda, komanso kuti thupi lake silinavunde.+ 32  Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za choonadi chimenecho.+ 33  Iye anakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watitsanulira mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu. 34  Ndipotu Davide sanakwere kumwamba,+ koma iye mwini anati, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja+ 35  kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”’+ 36  Choncho nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu, kuti Yesu ameneyu, amene inu munam’pachika,+ Mulungu anamuika kukhala Ambuye+ ndi Khristu.” 37  Tsopano iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima,+ ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Amuna inu, abale athu, tichite chiyani pamenepa?”+ 38  Petulo anawayankha kuti: “Lapani,+ ndipo aliyense wa inu abatizidwe+ m’dzina+ la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe.+ Mukatero mudzalandira mphatso yaulere+ ya mzimu woyera. 39  Pakuti lonjezoli+ laperekedwa kwa inu, kwa ana anu ndi kwa onse akutali,+ onse amene Yehova Mulungu wathu angawasankhe.”+ 40  Ndipo ndi mawu enanso ambiri, Petulo anachitira umboni mokwanira. Komanso sanaleke kuwadandaulira kuti: “Dzipulumutseni ku m’badwo wopotoka maganizo uno.”+ 41  Choncho amene analandira mawu akewo ndi mtima wonse anabatizidwa,+ moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezeka ndi anthu pafupifupi 3,000.+ 42  Chotero iwo anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa. Iwo anali kugawana zinthu,+ kudya chakudya+ komanso kupemphera.+ 43  Pamenepo anthu onse anayamba kuchita mantha, ndipo atumwiwo anayamba kuchita zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri.+ 44  Onse amene anakhala okhulupirira anasonkhana pamodzi ndipo zinthu zonse zimene anali nazo zinali za onse.+ 45  Anali kugulitsa malo awo ndi zina zimene anali nazo,+ n’kugawa kwa onse zimene apeza, aliyense malinga ndi kusowa kwake.+ 46  Tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi mogwirizana.+ Analinso kuyenderana m’nyumba zawo ndi kudyera limodzi chakudya mosangalala+ ndiponso ndi mtima wofunitsitsa kugawana zinthu. 47  Anali kutamanda Mulungu ndipo anthu onse anali kuwakonda.+ Komanso tsiku ndi tsiku, Yehova anapitiriza kuwawonjezera+ anthu amene anali kuwapulumutsa.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 5.