Machitidwe 3:1-26

3  Tsopano Petulo ndi Yohane anali kukalowa m’kachisi pa ola la kupemphera, 3 koloko masana.*+  Ndiyeno tsiku ndi tsiku anthu anali kunyamula mwamuna wina amene anabadwa ali wolumala.+ Iwo anali kukhazika wolumalayo pafupi ndi khomo la kachisi lotchedwa Chipata Chokongola,+ kuti azipempha mphatso zachifundo kwa olowa m’kachisimo.+  Munthuyu ataona Petulo ndi Yohane ali pafupi kulowa m’kachisimo anayamba kupempha kuti amupatse mphatso zachifundo.+  Koma Petulo, pamodzi ndi Yohane, anamuyang’anitsitsa+ n’kunena kuti: “Tiyang’ane.”  Iye anawayang’anitsitsa, akuyembekeza kuti amupatsa kanthu.  Koma Petulo anati: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho:+ M’dzina la Yesu Khristu Mnazareti,+ yenda!”+  Atatero anamugwira dzanja lake lamanja+ ndi kumuimiritsa. Nthawi yomweyo kunsi kwa mapazi ake komanso mafupa ake a akakolo zinalimba.+  Pamenepo anadumpha n’kuimirira,+ ndi kuyamba kuyenda. Ndipo analowa nawo limodzi m’kachisimo,+ akuyenda, kudumphadumpha ndi kutamanda Mulungu.  Anthu onse+ anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. 10  Kenako anayamba kumuzindikira kuti ndi mwamuna amene anali kukhala pa Chipata Chokongola+ cha kachisi n’kumapempha mphatso zachifundo. Ndipo iwo anadabwa ndi kuzizwa kwambiri+ ndi zimene zinam’chitikirazo. 11  Tsopano munthu uja atakangamira Petulo ndi Yohane osawasiya, anthu onse pamodzi anakhamukira kwa iwo pamalo otchedwa khonde la zipilala la Solomo,+ ali odabwa kwambiri. 12  Petulo ataona zimenezi, anauza anthuwo kuti: “Aisiraeli inu, n’chifukwa chiyani mukudabwa nazo zimenezi? N’chifukwa chiyani mukutiyang’anitsitsa ngati kuti tamuyendetsa mwa mphamvu zathu, kapena chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Mulungu?+ 13  Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza+ Mtumiki+ wake Yesu, amene inu munamupereka+ ndi kumukana pamaso pa Pilato, Pilatoyo akufuna kumumasula.+ 14  Inde, inu munakana woyera ndi wolungamayo,+ ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wina, munthu wopha anthu.+ 15  Chotero munapha Mtumiki Wamkulu wa moyo,+ koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, ndipo ife ndife mboni za choonadi chimenechi.+ 16  Choncho mwa chikhulupiriro chathu m’dzina lake, dzina lakelo lalimbitsa mwamunayu amene mukumuona ndi kumudziwa. Ndipo chikhulupiriro chimene ife tili nacho chifukwa cha iye chamuchiritsiratu, monga mmene nonsenu mukuonera. 17  Ndipo tsopano abale, ndikudziwa kuti munachita zinthu mosadziwa,+ ngati mmenenso olamulira+ anu anachitira. 18  Koma mwanjira imeneyi Mulungu wakwaniritsa zimene analengezeratu kudzera mwa aneneri onse, kuti Khristu wake adzavutika.+ 19  “Chotero lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa+ zibwere kuchokera kwa Yehova. 20  Komanso kuti atumize Yesu, amene ndiye Khristu woikidwa chifukwa cha inu. 21  Ameneyu kumwamba kuyenera kumusunga+ mpaka nthawi za kubwezeretsa+ zinthu zonse, kumene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera+ akale. 22  Ndipotu Mose ananena kuti, ‘Yehova Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu.+ Mudzamumvere pa zinthu zonse zimene adzakuuzeni.+ 23  Ndithudi, munthu aliyense amene sadzamvera Mneneri ameneyo Mulungu adzamuwononga ndi kumuchotsa pakati pa anthu ake.’+ 24  Ndipo aneneri onse, kuyambira pa Samueli mpaka aneneri onse amene anabwera m’mbuyo mwake, onse amene analosera, ananena mosapita m’mbali za masiku amenewa.+ 25  Inu ndinu ana+ a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale. Iye anauza Abulahamu kuti, ‘Kudzera mwa mbewu yako mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa.’+ 26  Mulungu atasankha Mtumiki wake, choyamba anamutumiza kwa inu,+ kuti adzakudalitseni mwa kubweza aliyense wa inu kuti musiye ntchito zanu zoipa.”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ola la 9” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.