Machitidwe 20:1-38
20 Chipolowe chija chitatha, Paulo anaitanitsa ophunzira. Atawalimbikitsa ndi kutsanzikana nawo,+ ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya.+
2 Iye anayendayenda m’madera akumeneko ndi kulimbikitsa ophunzira ndi mawu ambiri,+ kenako anafika ku Girisi.
3 Atakhala kumeneko miyezi itatu, anaganiza zobwerera ku Makedoniya, chifukwa chakuti Ayuda anamukonzera chiwembu.+ Chiwembuchi anachikonza Paulo atangotsala pang’ono kuyamba ulendo wa pamadzi wopita ku Siriya.
4 Amene anatsagana naye pa ulendowu anali Sopaturo+ mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe, ndi Timoteyo,+ koma ochokera m’chigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+
5 Iwowa anatsogola ndipo anali kutiyembekezera ku Torowa.+
6 Koma tinayamba ulendo wa panyanja ku Filipi masiku a mkate wopanda chofufumitsa atatha.+ Ndipo tinawapeza ku Torowa+ patapita masiku asanu. Kumeneko tinakhalako masiku 7.
7 Pa tsiku loyamba+ la mlungu, titasonkhana pamodzi kuti tidye chakudya, Paulo anayamba kuwakambira nkhani, chifukwa anali kunyamuka m’mawa wake. Ndipo anatenga nthawi yaitali akulankhula mpaka pakati pa usiku.
8 M’chipinda cham’mwamba+ mmene tinasonkhanamo, munali nyale zambiri ndithu.
9 Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko amene anakhala pawindo, anagona tulo tofa nato. Ali m’tulo choncho, anagwa pansi kuchokera panyumba yachitatu yosanja, ndipo anamupeza atafa.
10 Koma Paulo anatsika pansi, ndipo anadziponya pa iye+ ndi kumukumbatira. Kenako ananena kuti: “Khalani chete, pakuti ali moyo tsopano.”+
11 Atatero Paulo anakweranso m’chipinda cham’mwamba chija. Kenako ananyemanyema mkate n’kuyamba kudya, ndipo atakambirana kwa nthawi yaitali mpaka m’mawa, ananyamuka n’kumapita.
12 Koma iwo anatenga mnyamata uja ali wamoyo, ndipo anatonthozedwa kwambiri.
13 Tsopano ife tinatsogola kukakwera ngalawa n’kuyamba ulendo wopita ku Aso, kumene tinali kukatenga Paulo pangalawa. Iye anatilangiza kuti titsogole, chifukwa anafuna kuyenda wapansi.
14 Choncho atatipeza ku Aso, tinamukweza m’ngalawa ndi kupita ku Mitilene.
15 M’mawa wake titachoka kumeneko, tinafika pamalo oyang’anana ndi Kiyo. Koma tsiku lotsatira tinaima kwa kanthawi ku Samo, ndipo m’mawa wake tinafika ku Mileto.
16 Paulo anaganiza zongolambalala Efeso,+ kuti asataye nthawi m’chigawo cha Asia. Anachita zimenezi chifukwa anali kufulumira kuti ngati n’kotheka, akakhale ali ku Yerusalemu+ pa tsiku la chikondwerero cha Pentekosite.
17 Komabe ali ku Mileto anatuma mthenga ku Efeso kuti akaitane akulu+ a mpingo.
18 Akuluwo atafika, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinali kukhalira nanu nthawi zonse kuchokera tsiku loyamba limene ndinaponda m’chigawo cha Asia.+
19 Ndinali kutumikira+ Ambuye monga kapolo, modzichepetsa kwambiri,+ ndi misozi komanso ndi mayesero amene anandigwera chifukwa cha ziwembu+ za Ayuda.
20 Komatu sindinakubisireni chilichonse chopindulitsa, ndipo sindinaleke kukuphunzitsani+ poyera komanso kunyumba+ ndi nyumba.
21 Koma ndachitira umboni mokwanira+ kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape+ ndi kutembenukira kwa Mulungu, komanso kuti akhale ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.
22 Ndipo tsopano, popeza kuti mzimu wandikakamiza,+ ndikupita ku Yerusalemu, ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.
23 Chimodzi chokha chimene ndikudziwa n’chakuti mumzinda ndi mzinda, mzimu woyera+ wandichitira umboni mobwerezabwereza kuti maunyolo ndi masautso akundiyembekezera.+
24 Komabe, moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi.+ Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu,+ komanso kuti ndimalize utumiki+ umene ndinalandira+ kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+
25 “Ndipo tamverani tsopano! Ndikudziwa kuti nonsenu amene ndinakulalikirani za ufumu, nkhope yanga simudzaionanso.
26 Choncho mukhale mboni lero, kuti ine ndine woyera pa mlandu wa magazi+ a anthu onse.
27 Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro+ chonse cha Mulungu.
28 Mukhale tcheru ndi kuyang’anira+ gulu lonse la nkhosa,+ limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira,+ kuti muwete mpingo wa Mulungu,+ umene anaugula ndi magazi+ a Mwana wake weniweni.
29 Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu+ yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi.
30 Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka+ kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.+
31 “Choncho khalani maso, ndipo kumbukirani kuti kwa zaka zitatu,+ usana ndi usiku, sindinaleke kuchenjeza+ aliyense wa inu ndi misozi.
32 Koma tsopano ndikukuperekani kwa Mulungu+ ndi ku mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu. Mawu amenewo angakulimbikitseni+ ndi kukupatsani cholowa pakati pa oyeretsedwa onse.+
33 Sindinasirire mwa nsanje siliva, golide kapena chovala cha munthu.+
34 Inunso mukudziwa bwino kuti manja awa anagwira ntchito kuti ndipeze zosowa zanga+ ndi za amene ali nane.
35 M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi,+ muthandize ofookawo,+ ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka+ kuposa kulandira.’”
36 Atanena zimenezi, anagwada+ nawo pansi onsewo ndi kupemphera.
37 Pamenepo onse analira kwambiri, ndipo anakumbatira+ Paulo ndi kumupsompsona mwachikondi.+
38 Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.+ Kenako anamuperekeza+ kukakwera ngalawa.