Machitidwe 5:1-42
5 Tsopano munthu wina, dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsa munda wawo.
2 Koma mobisa iye anapatula zina mwa ndalamazo n’kusunga, mkazi wakenso anadziwa zimenezo. Ndiyeno anabweretsa zotsalazo n’kudzazipereka kwa atumwi.+
3 Koma Petulo anati: “Hananiya, n’chifukwa chiyani Satana+ wakulimbitsa mtima choncho kuti uyese kunamiza+ mzimu woyera+ ndi kubisa zina mwa ndalama za mtengo wa mundawo?
4 Kodi mundawo sunali m’manja mwako usanaugulitse? Ndipo utaugulitsa, kodi ndalamazo sukanatha kuchita nazo mmene ukanafunira? N’chifukwa chiyani mumtima mwako unaganiza zochita zinthu zimenezi? Pamenepa sikuti wanamiza+ anthu ayi, koma Mulungu.”+
5 Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi ndi kumwalira.+ Ndipo onse amene anamva zimenezi anagwidwa ndi mantha aakulu.+
6 Pamenepo anyamata anabwera ndi kumukulunga pansalu.+ Kenako anatuluka naye ndi kukamuika m’manda.
7 Tsopano patapita maola pafupifupi atatu mkazi wake analowa, osadziwa chimene chachitika.
8 Ndiyeno Petulo anamufunsa kuti: “Tandiuza, kodi ndalama zonse zimene awirinu mwapeza mutagulitsa munda wanu ndi izi?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndi zomwezo.”
9 Pamenepo Petulo anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani awirinu munagwirizana kuti muyese+ mzimu wa Yehova? Taona! Anthu amene anapita kukaika mwamuna wako m’manda ali pakhomo. Iwenso akunyamula ndi kutuluka nawe.”
10 Nthawi yomweyo anagwa pansi pamapazi a Petulo n’kumwalira.+ Pamene anyamata aja amalowa anam’peza atafa kale. Choncho anamunyamula ndi kutuluka naye kukamuika m’manda pafupi ndi mwamuna wake.
11 Zitatero mpingo wonse ndi onse amene anamva zimenezi anagwidwa ndi mantha aakulu.
12 Choncho atumwiwo anapitiriza kuchita zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri pakati pa anthu.+ Ndipo okhulupirira onse mogwirizana anali kusonkhana m’khonde la zipilala la Solomo.+
13 Ndithudi, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa enawo amene analimba mtima kuphatikana ndi ophunzirawo,+ koma anthu anali kuwatamanda.+
14 Komanso okhulupirira Ambuye anapitiriza kuwonjezeka, chifukwa amuna ndi akazi ambirimbiri anakhala ophunzira.+
15 Mwakuti anthuwo anabweretsa odwala m’misewu atawagoneka patimabedi ndi pamachira. Anachita izi kuti pamene Petulo akudutsa, chithunzithunzi chake chokhacho chigwere ena mwa iwo.+
16 Ndiponso anthu ambirimbiri ochokera m’mizinda yozungulira Yerusalemu anali kukhamukira kumeneko, atanyamula anthu odwala komanso amene mizimu yonyansa inali kuwazunza. Ndipo onsewo anali kuchiritsidwa.
17 Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, gulu la mpatuko la Asaduki la pa nthawiyo, anachita nsanje.+ Ndipo ananyamuka
18 ndi kugwira atumwiwo n’kuwatsekera m’ndende.+
19 Koma usiku, mngelo wa Yehova+ anatsegula zitseko za ndendeyo+ ndi kuwatulutsa, ndipo anawauza kuti:
20 “Pitani, ndipo mukaimirire m’kachisi ndi kupitiriza kuuza anthu zoyenera kuchita kuti adzapeze moyo umene ukubwerawo.”+
21 Atamva zimenezi, analowa m’kachisi m’mawa kwambiri ndi kuyamba kuphunzitsa.
Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye atafika, anasonkhanitsa pamodzi Khoti Lalikulu la Ayuda ndi bungwe lonse la akulu a ana a Isiraeli.+ Pamenepo anatumiza alonda kundende kuja kuti akatenge atumwiwo ndi kubwera nawo.
22 Koma pamene alonda aja anafika kumeneko sanawapeze m’ndendemo. Choncho anabwerera ndi kukanena zimenezi.
23 Iwo anati: “Ife tapeza ndende ili yokhoma ndi yotetezedwa bwino, alonda ali chilili m’makomo. Koma titatsegula sitinapezemo aliyense.”
24 Tsopano woyang’anira kachisi ndi ansembe aakulu atamva mawu amenewa, anathedwa nzeru ndi zimenezi posadziwa kuti chichitike n’chiyani.+
25 Koma panafika munthu wina amene anawauza kuti: “Tamverani! Amuna munawatsekera m’ndende aja ali m’kachisi, aimirira mmenemo ndipo akuphunzitsa anthu.”+
26 Pamenepo woyang’anira kachisi uja ananyamuka ndi alonda ake n’kukawatenga. Koma sanawatenge mwachiwawa, poopa+ kuti anthu awaponya miyala.
27 Choncho anabwera nawo ndi kuwaimiritsa m’holo ya Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo mkulu wa ansembe ananena
28 kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu+ kuti musadzaphunzitsenso m’dzina limeneli, koma taonani tsopano! Mwadzaza Yerusalemu yense ndi chiphunzitso chanuchi,+ ndipo mwatsimikiza mtima ndithu kuti mubweretse magazi+ a munthu ameneyu pa ife.”
29 Poyankha Petulo ndi atumwi enawo ananena kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.+
30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa+ Yesu, amene inu munamupha mwa kumupachika pamtengo.+
31 Ameneyo Mulungu anamukweza kudzanja lake lamanja+ monga Mtumiki Wamkulu+ ndi Mpulumutsi.+ Anachita zimenezi kuti Aisiraeli alape+ ndi kuti machimo awo akhululukidwe.+
32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zimenezi,+ chimodzimodzinso mzimu woyera,+ umene Mulungu wapereka kwa anthu omumvera monga wolamulira.”
33 Atamva zimenezi, anakwiya kwambiri moti anafuna kungowapha basi.+
34 Koma mwamuna wina anaimirira pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Iyeyu anali Mfarisi wotchedwa Gamaliyeli,+ mphunzitsi wa Chilamulo wolemekezedwa ndi anthu onse. Ndiyeno analamula kuti anthuwo awatulutse kwa kanthawi.+
35 Pamenepo anawauza kuti: “Amuna inu Aisiraeli,+ musamale ndi zimene mukufuna kuwachita anthu awa.
36 Chifukwa m’masiku am’mbuyomu, kunali Teuda amene anadzitchukitsa kwambiri+ ndipo amuna pafupifupi 400 analowa m’gulu lake.+ Koma anaphedwa, ndipo onse amene anali kumutsatira anabalalitsidwa osaonekanso.
37 Kenako kunali Yudasi Mgalileya m’masiku a kalembera.+ Iyeyu anakopa anthu ndipo anamutsatira. Koma munthu ameneyunso anafa, ndipo onse amene anali kumutsatira anabalalikabalalika.
38 Choncho mmene zinthu zilili panopa, ndikukuuzani kuti, Alekeni amuna amenewa musalimbane nawo. Chifukwa ngati zolinga zawo kapena ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali.+
39 Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu,+ simungathe kuwaletsa.+ Mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”+
40 Pamenepo iwo anamvera mawu ake, ndipo anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula+ ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu,+ kenako anawamasula.
41 Choncho atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala+ chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.+
42 Ndipo tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba,+ anapitiriza mwakhama kuphunzitsa+ ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.+