Machitidwe 25:1-27
25 Patatha masiku atatu Fesito atayamba kulamulira+ m’chigawocho, anapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kaisareya.+
2 Kumeneko ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda anamuuza zambiri+ zoneneza Paulo. Ndiyeno anayamba kumuchonderera,
3 ndi kumupempha kuti awakomere mtima mwa kuitanitsa munthuyu kuti abwere ku Yerusalemu, kuti iwo amudikirire+ panjira ndi kumupha.
4 Koma Fesito anawayankha kuti Paulo akuyenera kusungidwa ku Kaisareya, ndi kuti posachedwa nayenso anyamuka kupita komweko.
5 Ndiyeno anati: “Amene ali ndi maudindo pakati panu, tipitire limodzi kuti ngati pali cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu akamuimbe mlandu.”+
6 Choncho iye atakhala nawo kumeneko kwa masiku osapitirira 8 kapena 10, anapita ku Kaisareya. Ndipo tsiku lotsatira anakhala pampando woweruzira milandu+ ndi kuitanitsa Paulo kuti abwere naye.
7 Paulo atafika, Ayuda amene anabwera kuchokera ku Yerusalemu, anaima momuzungulira n’kumamuneneza milandu yoopsa yambiri,+ imene sanathe kupereka umboni wake.
8 Koma Paulo podziteteza anati: “Ine sindinachimwire Chilamulo cha Ayuda, kapena kachisi,+ kapena Kaisara.”+
9 Koma pofuna kuti Ayudawo amukonde,+ Fesito anayankha Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?”+
10 Paulo anayankha kuti: “Ine ndaimirira kutsogolo kwa mpando woweruzira milandu wa Kaisara,+ kumene ndiyenera kuweruzidwa. Ayuda+ sindinawalakwire chilichonse, monga mmene inunso mukuonera.
11 Ngati ndilidi wolakwa,+ ndipo ndachita chinthu choyenera imfa, sindikukana kufa.+ Koma ngati pa zimene awa akundinenezazi palibe chinthu chotero, palibe munthu amene angandipereke kwa iwo kuti awakondweretse. Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!”+
12 Ndiyeno Fesito atalankhula ndi bungwe la aphungu, anayankha kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekera kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.”
13 Tsopano patapita masiku angapo, Mfumu Agiripa* ndi Berenike anafika ku Kaisareya pa ulendo wa boma wokapereka ulemu kwa Fesito.
14 Pamene anali kumeneko masiku angapo, Fesito anafotokozera mfumuyo nkhani yokhudza Paulo. Iye ananena kuti:
“Pali munthu wina amene Felike anamusiya m’ndende,
15 ndipo pamene ndinali ku Yerusalemu, ansembe aakulu komanso akulu a Ayuda anabwera kudzamuneneza.+ Anali kupempha kuti apatsidwe chiweruzo chakuti aphedwe.
16 Koma ine ndinawayankha kuti, Aroma sachita zinthu mwa njira imeneyo. Iwo sapereka munthu m’manja mwa omuneneza pongofuna kuwakondweretsa, munthu wonenezedwayo+ asanapatsidwe mwayi woonana pamasom’pamaso ndi omunenezawo kuti alankhule mawu odziteteza pa mlanduwo.
17 Choncho onse atafika kuno, sindinachedwe, koma tsiku lotsatira ndinakhala pampando woweruzira milandu ndi kuitanitsa munthuyo kuti abwere naye.
18 Omunenezawo ataimirira, sanatchule mlandu uliwonse+ wa zoipa zimene ndinali kuganiza zokhudza munthu ameneyu.
19 Iwo anali kungotsutsana naye nkhani zokhudzana ndi kulambira+ kwawo mulungu, ndi za munthu wina wake wotchedwa Yesu amene anafa koma Paulo akupitiriza kunena motsimikiza kuti ali moyo.+
20 Choncho pothedwa nzeru ndi mkangano wa nkhani zimenezi, ndinamufunsa ngati akufuna kupita ku Yerusalemu kuti nkhanizi zikaweruzidwire kumeneko.+
21 Koma pamene Paulo anapempha+ kuti timusunge kuti akamve chigamulo cha Wolemekezeka, ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”
22 Pamenepo Agiripa anauza Fesito kuti: “Inenso ndikufuna ndimve ndekha munthu ameneyu+ akulankhula.” Iye anati: “Mawa mudzamumvetsera.”
23 M’mawa wake, Agiripa ndi Berenike anabwera ndi ulemu waukulu wachifumu.+ Analowa m’chipinda chosonkhanira pamodzi ndi akuluakulu a asilikali komanso akuluakulu a mumzindawo, ndipo Fesito atalamula, anamubweretsa Paulo.
24 Ndiyeno Fesito ananena kuti: “Mfumu Agiripa ndi anthu nonse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu. Ayuda onse anandipempha ine ku Yerusalemu komanso kuno, mofuula kuti iyeyu sayeneranso kukhala ndi moyo.+
25 Koma ine ndinaona kuti sanachite chilichonse choyenera imfa.+ Choncho iyeyu atapempha kuti akaonekere kwa Wolemekezeka,+ ndinaganiza zomutumiza.
26 Koma ndilibe chenicheni chimene ndingalembere Mbuyanga chokhudza munthuyu. Choncho ndamubweretsa pamaso panu, makamaka pamaso pa inu, Mfumu Agiripa, kuti mukamufunsa za nkhaniyi,+ ndipeze cholemba.
27 Chifukwa kwa ine, ndikuona kuti si chanzeru kutumiza mkaidi koma osanena milandu imene akumuneneza.”
Mawu a M'munsi
^ Ameneyu anali Herode Agiripa Wachiwiri.