Machitidwe 26:1-32

26  Ndiyeno Agiripa+ anauza Paulo kuti: “Waloledwa kulankhula mbali yako.” Pamenepo Paulo anatambasula dzanja lake+ ndi kuyamba kulankhula modziteteza kuti:+  “Inu Mfumu Agiripa, ndine wosangalala kuti lero ndidziteteza pamaso panu, pa zinthu zonse zimene Ayuda akundineneza.+  Makamaka chifukwa chakuti ndinu katswiri pa miyambo yonse,+ komanso pa zimene Ayuda amakangana. Choncho ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.  “Ndithudi, moyo umene ndakhala+ kuyambira unyamata wanga, pakati pa anthu a mtundu wanga ndiponso mu Yerusalemu, ndi wodziwika bwino kwa Ayuda onse.  Ndi wodziwika bwino kwa Ayuda amene andidziwa ine kuchokera kale. Ndipo atafuna, angandichitire umboni kuti ndinalidi Mfarisi,+ wa m’gulu lampatuko lotsatira kulambira kwathu mokhwimitsa zinthu kwambiri.+  Koma tsopano ndaimirira pano kuti ndiweruzidwe, chifukwa cha chiyembekezo+ pa lonjezo+ limene Mulungu anapereka kwa makolo athu.  Ndipo mafuko athu 12 akuyembekezera kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli, mwa kumuchitira utumiki wopatulika mosalekeza usana ndi usiku.+ Chotero Mfumu, Ayuda akundiimba mlandu chifukwa cha chiyembekezo chimenechi.+  “N’chifukwa chiyani anthu inu mukuona ngati n’zosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?+  Inetu ndinali kuganiza mumtima mwanga kuti ndiyenera kuchita zambiri zotsutsana ndi dzina la Yesu Mnazareti. 10  Ndipo zimenezi ndinazichitadi mu Yerusalemu. Oyera ambiri ndinawatsekera m’ndende,+ nditapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu.+ Pamene anafuna kuwapha, ine ndinali kuvomereza. 11  Nthawi zambiri ndinawapatsa chilango m’masunagoge onse,+ poyesa kuwakakamiza kuti akane chikhulupiriro chawo. Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambiri, ndinafika pa kuwazunza ngakhale m’mizinda yakunja. 12  “Ndili kalikiliki ndi zimenezi, ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko+ mwa mphamvu ndi chilolezo cha ansembe aakulu. 13  Koma ndili mumsewu dzuwa lili pamutu, Inu mfumu, ndinaona kuwala koposa kunyezimira kwa dzuwa kochokera kumwamba kutandizungulira pamodzi ndi amene ndinali nawo pa ulendowo.+ 14  Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza m’Chiheberi kuti, ‘Saulo, Saulo, n’chifukwa chiyani ukundizunza ine? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosera.’*+ 15  Koma ine ndinati, ‘Mbuyanga, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati, ‘Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.+ 16  Komabe, dzuka ndi kuimirira.+ Pakuti ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndi mboni+ ya zinthu zonse, zimene waona ndi zimene ndidzakuonetsa zokhudza ine. 17  Ndidzakuonetsa zimenezi pamene ndidzakulanditsa kwa anthu awa ndi kwa anthu a mitundu ina, kumene ine ndikukutumiza.+ 18  Ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mu mdima+ ndi kuwatembenuzira ku kuwala.+ Kuwachotsa m’manja mwa Satana+ ndi kuwatembenuzira kwa Mulungu, kuti machimo awo akhululukidwe+ ndi kukalandira cholowa+ pamodzi ndi oyeretsedwa,+ mwa chikhulupiriro chawo mwa ine.’ 19  “Chotero, Mfumu Agiripa, ine sindinachite zinthu zosonyeza kusamvera masomphenya a kumwambawo.+ 20  Koma kuyambira kwa okhala ku Damasiko+ ndi ku Yerusalemu,+ komanso m’dziko lonse la Yudeya ndi kwa anthu a mitundu ina,+ ndinafikitsa uthenga wakuti alape ndi kutembenukira kwa Mulungu mwa kuchita ntchito zosonyeza kulapa.+ 21  Chifukwa cha zimenezi, Ayuda anandigwira m’kachisi ndipo anafuna kundipha.+ 22  Komabe, popeza ndinalandira thandizo+ kuchokera kwa Mulungu, ndikupitiriza kuchitira umboni kwa anthu otchuka ndi kwa anthu wamba mpaka lero. Sindikunena kena kalikonse koma zokhazo zimene Zolemba za aneneri+ ndi za Mose+ zinaneneratu kuti zidzachitika. 23  Zolembazo zinaneneratu kuti Khristu adzavutika,+ ndipo monga woyamba kuukitsidwa kwa akufa,+ iye adzafalitsa kuwala+ mwa anthu awa ndi kwa anthu a mitundu ina.”+ 24  Tsopano pamene anali kunena zinthu izi podziteteza, Fesito ananena mokweza mawu kuti: “Ukupenga+ iwe Paulo! Kuphunzira kwambiri kwakuchititsa misala!” 25  Koma Paulo anati: “Wolemekezeka a Fesito, inetu sindinachite misala ayi, koma ndikulankhula mawu a choonadi ndiponso anzeru. 26  Kunena zoona, inu mfumu amene ndikulankhula nanu mwaufulu chotere, mukudziwa bwino zimenezi. Ndili wotsimikiza kuti palibe ngakhale chimodzi mwa zinthu zimenezi, chimene simunachizindikire, pakuti izi sizinachitikire mseri.+ 27  Kodi inuyo, Mfumu Agiripa, mumakhulupirira Zolemba za aneneri? Ndikudziwa kuti mumazikhulupirira.”+ 28  Koma Agiripa anauza Paulo kuti: “M’kanthawi kochepa ungathe kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” 29  Pamenepo Paulo anati: “Kaya m’kanthawi kochepa kapena m’nthawi yaitali, pemphero langa kwa Mulungu ndi lakuti, onse amene andimvetsera lero, osati inu nokha, akhale ngati ine, kupatulapo maunyolo okhawa.” 30  Pamenepo mfumu inaimirira. Chimodzimodzinso bwanamkubwa, Berenike ndi amuna amene anakhala nawo pamodzi. 31  Koma pochoka anayamba kukambirana kuti: “Munthu uyu sakuchita chilichonse choyenera imfa+ kapena kumangidwa.” 32  Ndipo Agiripa anauza Fesito kuti: “Akanakhala kuti sanapemphe kukaonekera kwa Kaisara, munthu ameneyu akanamasulidwa ndithu.”+

Mawu a M'munsi

Zimenezi zinali ndodo zosongola zimene anali kutosera nyama zapagoli kuti ziyende mofulumira.