Machitidwe 18:1-28
18 Zimenezi zitatha, Paulo anachoka ku Atene n’kupita ku Korinto.
2 Kumeneko anapeza Myuda wina dzina lake Akula,+ mbadwa ya ku Ponto. Iyeyu pamodzi ndi mkazi wake Purisikila, anali atafika chaposachedwa kuchokera ku Italiya,+ chifukwa Kalaudiyo+ anali atalamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Choncho Paulo anapita kwa iwo.
3 Ndipo popeza kuti ntchito yawo inali imodzi, anakhala kunyumba kwawoko. Iwo ankagwira ntchito pamodzi,+ pakuti onse anali amisiri opanga mahema.
4 Komabe Paulo anali kukamba nkhani m’sunagoge+ sabata lililonse, ndipo anali kukopa Ayuda ndi Agiriki.
5 Tsopano Sila+ ndi Timoteyo+ atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu. Iye anali kuchitira umboni kwa Ayuda ndi kuwatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+
6 Koma iwo atapitiriza kumutsutsa ndi kulankhula monyoza,+ iye anakutumula zovala zake+ ndi kuwauza kuti: “Magazi anu+ akhale pamitu panu. Ine ndilibe mlandu.+ Kuyambira tsopano ndizipita kwa anthu a mitundu ina.”+
7 Zitatero, iye anachoka pamenepo ndi kupita kunyumba ya munthu wina dzina lake Titiyo Yusito. Iyeyu anali wolambira Mulungu, ndipo nyumba yake inali moyandikana ndi sunagoge.
8 Kirisipo,+ mtsogoleri wa sunagoge, anakhala wokhulupirira mwa Ambuye, pamodzi ndi onse a m’banja lake. Ndipo Akorinto ambiri amene anamva uthenga wabwino anayamba kukhulupirira ndi kubatizidwa.
9 Komanso usiku, Ambuye anauza Paulo+ m’masomphenya kuti: “Usaope, pitiriza kulankhula. Usakhale chete,
10 chifukwa ine ndili nawe.+ Palibe munthu amene adzakukhudze ndi kukuvulaza, pakuti ndili ndi anthu ambiri mumzinda uno.”
11 Choncho anakhazikika kumeneko chaka ndi miyezi 6, akuwaphunzitsa mawu a Mulungu.
12 Tsopano pamene Galiyo anali bwanamkubwa+ wa Akaya, Ayuda ananyamuka mogwirizana ndi kuukira Paulo, ndipo anamutengera kumpando woweruzira milandu.+
13 Kumeneko iwo anati: “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu m’njira yosemphana ndi chilamulo.”+
14 Koma pamene Paulo ankati azitsegula pakamwa, Galiyo anauza Ayudawo kuti: “Ayuda inu, chikanakhala cholakwa china, kapena pakanachitika chinachake choipa, ndithu ndikanaleza mtima ndi kukumverani.
15 Koma ngati nkhani yake ili yokhudza mikangano pa mawu, mayina+ ndi chilamulo+ chanu, zimenezo muthane nazo nokha. Ine sindikufuna kuti ndikhale woweruza nkhani zoterezi.”
16 Atatero anawapitikitsa kumpando woweruzira milanduwo.
17 Zitatero, onse anagwira Sositene,+ mtsogoleri wa sunagoge ndi kuyamba kumumenya pafupi ndi mpando woweruzira milanduwo. Koma Galiyo sanasamale zimenezo ngakhale pang’ono.
18 Koma Paulo atakhala kumeneko masiku ndithu, anatsanzikana ndi abalewo ndipo anapitiriza ulendo wake wa pamadzi kulowera ku Siriya. Pa ulendowu anatsagana ndi Purisikila ndi Akula. Paulo anameta tsitsi lake+ ku Kenkereya+ chifukwa cha lonjezo limene anachita.
19 Choncho onse anafika ku Efeso, ndipo anzakewo anawasiya kumeneko. Koma iye yekha analowa m’sunagoge+ ndi kuyamba kukambirana ndi Ayuda.
20 Ngakhale kuti anamupempha mobwerezabwereza kuti akhale nawo kwa nthawi yotalikirapo, iye sanalole.
21 M’malomwake, anatsanzikana+ nawo ndi kuwauza kuti: “Yehova akalola ndidzabweranso kudzakuonani.”+ Choncho ananyamuka ku Efeso ulendo wa panyanja
22 ndipo anafika ku Kaisareya. Kenako anapita* kukapereka moni ku mpingo, ndipo pambuyo pake anapita ku Antiokeya.
23 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, ananyamuka ndi kuyenda malo osiyanasiyana m’chigawo cha Galatiya+ ndi Fulugiya,+ ndipo anali kulimbikitsa+ ophunzira onse.
24 Tsopano Myuda wina dzina lake Apolo,+ mbadwa ya ku Alekizandiriya, amene anali ndi mphatso ya kulankhula, anafika ku Efeso. Iyeyu analinso kuwadziwa bwino Malemba.+
25 Mwamuna ameneyu analangizidwa njira ya Yehova ndi mawu a pakamwa. Ndiyeno popeza kuti anali wodzipereka kwambiri chifukwa chakuti anali ndi mzimu woyera,+ anali kulankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu. Koma anali kudziwa za ubatizo+ wa Yohane wokha basi.
26 Mwamuna ameneyu anayamba kulankhula molimba mtima musunagoge. Tsopano Purisikila ndi Akula+ atamumvetsera, anamutenga ndi kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.
27 Ndiponso, popeza kuti anali wofunitsitsa kupita ku Akaya, abalewo analembera ophunzira kumeneko. Anawalimbikitsa kuti amulandire ndi manja awiri. Choncho iye atafika kumeneko, anathandiza kwambiri+ anthu amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+
28 Pakuti mwamphamvu, iye anawatsimikizira Ayuda poyera kuti anali olakwa, ndipo anasonyeza mwa Malemba+ kuti Yesu ndiyedi Khristu.+
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti anapita ku Yerusalemu.