Machitidwe 15:1-41
15 Ndiyeno amuna ena ochokera ku Yudeya+ anapita kumeneko ndi kuyamba kuphunzitsa abale kuti: “Mukapanda kudulidwa+ malinga ndi mwambo wa Mose,+ simungapulumuke.”
2 Koma Paulo ndi Baranaba sanamvane nawo ndipo anatsutsana nawo kwambiri. Choncho iwo anasankha Paulo ndi Baranaba, pamodzi ndi ena mwa iwo, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,+ kuti akawauze za kutsutsanako.
3 Tsopano mpingo utawaperekeza,+ amuna amenewa anapitiriza ulendo wawo kudzera ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko anali kufotokoza mwatsatanetsatane za kutembenuka kwa anthu a mitundu ina,+ ndipo iwo anasangalatsa kwambiri abale onse.+
4 Atafika ku Yerusalemu analandiridwa ndi manja awiri+ ndi mpingo, atumwi, komanso akulu. Kumeneko anafotokoza zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.+
5 Koma okhulupirira ena, amene kale anali m’gulu lampatuko la Afarisi anaimirira m’mipando yawo n’kunena kuti: “M’pofunika kuwadula+ ndi kuwalamula kuti azisunga chilamulo cha Mose.”+
6 Ndiyeno atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti akambirane nkhani imeneyi.+
7 Tsopano atatsutsana kwambiri,+ Petulo anaimirira, ndi kuwauza kuti: “Amuna inu, abale anga, mukudziwa bwino kuti m’masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu, kuti kudzera pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino ndi kukhulupirira.+
8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa zamumtima,+ anachitira umboni mwa kuwapatsa mzimu woyera,+ monga anachitiranso kwa ife.
9 Ndipo iye sanasiyanitse m’pang’ono pomwe pakati pa ife ndi iwo.+ Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.+
10 Nanga tsopano n’chifukwa chiyani inu mukumuyesa Mulungu mwa kukanikizira goli pakhosi la ophunzira, goli+ limene makolo athu ngakhalenso ife sitinathe kulisenza?+
11 Koma tsopano timakhulupirira kuti ife tidzapulumuka mwa kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye Yesu, mofanananso ndi anthu amenewa.”+
12 Pamenepo gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera Baranaba ndi Paulo pamene anali kufotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo pakati pa anthu a mitundu ina.+
13 Ataleka kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Amuna inu, abale anga, ndimvetsereni.+
14 Sumeoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.+
15 Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’Zolemba za aneneri. Mawuwo amati,
16 ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera ndi kumanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo ndi kuiimikanso.+
17 Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalirawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova amene akuchita zinthu zimenezi,+
18 zimene anatsimikiza kalekale kuti adzazichita.’+
19 Choncho chigamulo changa n’chakuti, anthu amene akuchokera m’mitundu ina ndi kutembenukira kwa Mulungu, tisawavutitse.+
20 Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ dama,*+ zopotola,+ ndi magazi.+
21 Pakuti kuyambira kalekale, anthu akhala akulalikira mumzinda ndi mzinda mawu ochokera m’mabuku a Mose, chifukwa mabuku amenewa amawerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.”+
22 Pamenepo atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwirizana zosankha amuna pakati pawo, kuti awatumize ku Antiokeya limodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Choncho anasankha Yudasi wotchedwa Barasaba,+ ndi Sila, amuna otsogolera pakati pa abale.
23 Chotero ndi manja awo analemba kuti:
“Ife abale anu atumwi pamodzi ndi akulu, tikulembera inu abale athu ochokera mwa anthu a mitundu ina, okhala ku Antiokeya,+ ku Siriya ndi ku Kilikiya:+ Landirani moni!
24 Tamva kuti ena ochokera pakati pathu akhala akulankhula mawu okusautsani,+ pofuna kupotoza maganizo anu, ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo aliwonse.+
25 Pa chifukwa chimenechi, tonse tagwirizana chimodzi,+ ndipo tavomerezana kuti tisankhe amuna oti tiwatumize kwa inu limodzi ndi okondedwa athu, Baranaba ndi Paulo.+
26 Amenewa ndi amuna omwe apereka miyoyo yawo chifukwa cha dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+
27 Chotero tikutumiza Yudasi ndi Sila,+ kuti iwonso adzakufotokozereni zinthu zomwezi mwa mawu apakamwa.+
28 Pakuti mzimu woyera+ pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera,+ kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi
29 kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola,+ ndi dama.+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri,+ zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”
30 Amuna amenewa atanyamuka, analowera ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa khamu lonse la anthu ndi kuwapatsa kalatayo.+
31 Ataiwerenga, anakondwera chifukwa cha mawu olimbikitsawo.+
32 Ndiponso popeza kuti Yudasi ndi Sila anali aneneri,+ analimbikitsa abalewo ndi mawu ambiri ndipo anawapatsa mphamvu.+
33 Atakhala kumeneko kanthawi, abalewo anawalola kubwerera mumtendere+ kwa amene anawatuma.
34 * ——
35 Koma Paulo ndi Baranaba anatsalira ku Antiokeya.+ Ndipo iwo pamodzi ndi enanso ambiri anali kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova.+
36 Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tsopano, tiyeni tibwerere kumizinda yonse kumene tinafalitsa mawu a Yehova kuti tikachezere abale ndi kuwaona kuti ali bwanji.”+
37 Chotero Baranaba anafunitsitsa kutenga Yohane, wotchedwa Maliko.+
38 Koma Paulo anaona kuti n’kosayenera kumutenga kuti apite nawo. Anaona kuti n’kosayenera chifukwa ulendo wapita Yohane anawasiya ku Pamfuliya+ ndipo sanapite nawo ku ntchitoyi.
39 Pamenepo panabuka mkangano woopsa mpaka anapatukana. Baranaba+ anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wa pamadzi kulowera ku Kupuro.+
40 Koma Paulo anasankha Sila,+ ndipo abale atamuikiza m’manja mwa Yehova kuti amusonyeze kukoma mtima kwakukulu, ananyamuka.+
41 Iye anadzera ku Siriya ndi ku Kilikiya, ndipo anali kulimbitsa mipingo.+