Machitidwe 10:1-48

10  Tsopano ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Koneliyo, kapitawo wa gulu la asilikali+ lotchedwa Ataliyana.+  Iyeyu anali wopembedza+ ndi woopa+ Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse. Anali kupatsa anthu mphatso zambiri zachifundo+ ndipo anali kupemphera kwa Mulungu nthawi zonse.+  Tsiku lina cha m’ma 3 koloko masana,*+ anaona mngelo+ wa Mulungu m’masomphenya.+ Mngeloyo anabwera kwa iye n’kunena kuti: “Koneliyo!”  Pamenepo Koneliyo anayang’anitsitsa mngelo uja, ndipo mantha atamugwira anati: “N’chiyani Mbuyanga?” Mngeloyo anamuuza kuti: “Mapemphero ako+ ndi mphatso zako zachifundo zakwera kwa Mulungu monga chikumbutso.+  Chotero tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina dzina lake Simoni, wotchedwanso Petulo.  Munthu ameneyu ndi mlendo kunyumba kwa Simoni wina wofufuta zikopa, amene nyumba yakeyo ili m’mbali mwa nyanja.”+  Mngelo amene anali kulankhula nayeyo atangochoka, iye anaitana antchito ake a panyumbapo awiri ndi msilikali. Msilikaliyo anali wopembedza, ndipo anali mmodzi wa amene anali kumutumikira nthawi zonse.+  Koneliyo anawafotokozera zonse ndi kuwatuma ku Yopa.+  Tsiku lotsatira, ulendo wawo uli mkati komanso akuyandikira mzindawo, Petulo anakwera padenga*+ kukapemphera cha m’ma 12 koloko masana.*+ 10  Koma anamva njala kwambiri ndipo anafuna kudya. Pamene chakudya chinali kukonzedwa, anayamba kuona masomphenya.+ 11  M’masomphenyawo anaona kumwamba kutatseguka,+ ndipo chinthu china chake chinali kutsika. Chinthucho chinali chooneka ngati chinsalu chachikulu chimene achigwira m’makona onse anayi n’kumachitsitsira padziko lapansi. 12  Pachinthu chimenecho panali mitundu yonse ya nyama za miyendo inayi, ndi zokwawa zapadziko lapansi, ndiponso mbalame zam’mlengalenga.+ 13  Pamenepo mawu anamveka kwa iye kuti: “Nyamuka Petulo, ipha udye!”+ 14  Koma Petulo anati: “Iyayi Ambuye, sindinadyepo choipitsidwa ndi chonyansa chilichonse chikhalire.”+ 15  Ndipo mawu aja anamvekanso kwa iye kachiwiri kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.”+ 16  Mawu amenewo anamvekanso kachitatu, ndipo nthawi yomweyo chinthu chooneka ngati chinsalu chija chinatengedwa kupita kumwamba.+ 17  Petulo atathedwa nzeru chifukwa chosamvetsa tanthauzo la masomphenya amene anaonawo, amuna otumidwa ndi Koneliyo aja anali atafunsira kuti nyumba ya Simoni ili kuti ndipo anali ataima pachipata.+ 18  Iwo analankhula mofuula ndi kufunsa ngati kumeneko anali ndi mlendo dzina lake Simoni wotchedwanso Petulo. 19  Petulo ali mkati moganizira za masomphenyawo, mzimu+ unati: “Tamvera! Pali amuna atatu amene akukufuna. 20  Chotero nyamuka, tsika upite nawo limodzi, usakayikire ayi, chifukwa ndawatuma ndine.”+ 21  Choncho Petulo anatsika kukakumana ndi anthuwo ndipo anati: “Amene mukumufunayo ndine. Mukufuna chiyani kuno?” 22  Iwo anati: “Tachokera kwa Koneliyo, kapitawo wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu,+ amene mtundu wonse wa Ayuda umamuyamikira.+ Mngelo woyera anamupatsa malangizo a Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.” 23  Ndiyeno anawalowetsa m’nyumba ndi kuwachereza. M’mawa mwake ananyamuka ndi kupita nawo, ndipo abale ena a mu Yopa anatsagana naye. 24  Tsiku linalo anafika ku Kaisareya. Kumeneko Koneliyo anali kuwayembekezera, ndipo anasonkhanitsa achibale ndi mabwenzi ake apamtima. 25  Pamene Petulo anali kulowa, Koneliyo anakumana naye ndipo anagwada pamaso pake n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. 26  Koma Petulo anamuimiritsa, ndi kunena kuti: “Imirira, inenso ndine munthu chabe.”+ 27  Pamene anali kukambirana naye, analowa mkati ndipo anapeza anthu ambiri atasonkhana mmenemo. 28  Ndiyeno Petulo anawauza kuti: “Inunso mukudziwa bwino kuti n’kosaloleka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa fuko lina kapena kumuyandikira.+ Koma tsopano Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti woipitsidwa kapena wonyansa.+ 29  N’chifukwa chake ndabwera mosanyinyirika mutanditumizira anthu aja. Choncho ndikufuna ndidziwe chimene mwandiitanira.” 30  Pamenepo Koneliyo anati: “Masiku anayi apitawo kuchokera pa ola lino, ndinali kupemphera m’nyumba mwanga cha m’ma 3 koloko masana.+ Mwadzidzidzi munthu wovala zowala+ anaimirira pamaso panga. 31  Munthuyo anandiuza kuti, ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira mphatso zako zachifundo.+ 32  Chotero tumiza anthu ku Yopa, kuti akaitane Simoni wotchedwanso Petulo.+ Munthu ameneyo ndi mlendo m’nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, amene amakhala m’mbali mwa nyanja.’+ 33  Chotero ndinawatumiza mwamsanga kwa inu, ndipo mwachita bwino kubwera kuno. N’chifukwa chake pa nthawi ino tonse tili pano pamaso pa Mulungu, kuti timve zonse zimene Yehova wakulamulani kuti mutiuze.”+ 34  Pamenepo Petulo anayamba kulankhula kuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho.+ 35  Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.+ 36  Mulungu anatumiza mawu+ kwa ana a Isiraeli ndi kulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa mtendere+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ameneyu ndiye Ambuye wa ena onse.+ 37  Inu mukudziwa nkhani imene inali m’kamwam’kamwa mu Yudeya monse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane anali kulalikira.+ 38  Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, kuti Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye,+ anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.+ 39  Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse zimene anachita m’dziko la Ayuda ndi mu Yerusalemu momwe. Koma iwo anamupha mwa kumupachika pamtengo.+ 40  Ameneyu Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu ndi kumulola kuonekera,+ 41  osati kwa anthu onse, koma kwa mboni zoikidwiratu ndi Mulungu,+ zomwe ndi ife amene tinadya ndi kumwa naye limodzi+ atauka kwa akufa. 42  Ndiponso, anatilamula kuti tilalikire+ kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira wakuti iyeyu ndi Amene Mulungu anamuika kukhala woweruza anthu amoyo ndi akufa.+ 43  Aneneri onse amachitira umboni za iyeyu,+ kuti aliyense womukhulupirira, machimo ake amakhululukidwa m’dzina lake.”+ 44  Pamene Petulo anali kulankhula zinthu izi, mzimu woyera unagwa pa onse amene anali kumvera mawu amenewo.+ 45  Ndipo okhulupirika amene anabwera ndi Petulo, amene anali odulidwa anadabwa, chifukwa mphatso yaulere ya mzimu woyera inalinso kuthiridwa pa anthu a mitundu ina.+ 46  Pakuti anawamva akulankhula m’malilime ndi kulemekeza Mulungu.+ Ndiyeno Petulo anati: 47  “Anthu awa alandira mzimu woyera monga mmenenso ife tinalandirira. Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe ndi madzi?”+ 48  Atatero anawalamula kuti abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu.+ Pamenepo iwo anamupempha kuti akhalebe nawo masiku angapo.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Ena amati “patsindwi.”
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.