Machitidwe 17:1-34

17  Iwo tsopano anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda.  Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa m’sunagogemo, ndipo kwa masabata atatu anakambirana nawo mfundo za m’Malemba.+  Iye anali kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti kunali koyenera kuti Khristu avutike+ ndi kuuka kwa akufa.+ Anali kunena kuti: “Yesu amene ndikumulalikira kwa inu, ndiye Khristu.”+  Zotsatira zake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira+ ndipo anagwirizana ndi Paulo ndi Sila.+ Ndipo khamu lalikulu la Agiriki opembedza Mulungu, ndi amayi ambiri olemekezeka anachitanso chimodzimodzi.  Koma Ayuda anachita nsanje,+ ndipo anatengana ndi anthu ena oipa, anthu osowa chochita amene anali kungokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa ndi kuyambitsa chipolowe mumzindamo.+ Kenako anakhamukira kunyumba ya Yasoni,+ kukafuna atumwiwo kuti awatulutsire ku gulu lachipolowelo.  Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: “Anthu awa amene abweretsa mavuto+ padziko lapansi kumene kuli anthu, tsopano akupezekanso kuno,  ndipo Yasoni anawalandira bwino. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo+ a Kaisara. Akunena kuti eti kulinso mfumu ina+ dzina lake Yesu.”  Ndi mawu amenewa, iwo anautsa mkwiyo wa khamu la anthu lija ndi olamulira a mzindawo.  Pamenepo olamulira a mzindawo analipiritsa Yasoni ndi enawo ndalama, kenako anawamasula. 10  Kutangoda,+ abale anatulutsa Paulo ndi Sila ndi kuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko, analowa m’sunagoge wa Ayuda. 11  Koma anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. Iwowa analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku anali kufufuza+ Malemba+ mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.+ 12  Chotero ambiri a iwo anakhala okhulupirira, chimodzimodzinso akazi ndi amuna ambiri otchuka+ achigiriki. 13  Koma Ayuda ochokera ku Tesalonika atamva kuti Paulo akufalitsanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko kukayambitsa chipolowe+ ndi kuchititsa anthuwo kukwiyira+ atumwiwo. 14  Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo kuti apite kunyanja.+ Koma Sila ndi Timoteyo anatsalira kumeneko. 15  Ndipo anthu amene anaperekeza Paulo anakamufikitsa ku Atene. Koma anabwerera atatumidwa kuti akauze Sila ndi Timoteyo+ kuti amutsatire msanga. 16  Pamene Paulo anali kuwayembekezera ku Atene, mtima unamuwawa kwambiri+ poona kuti mumzindawo mwadzaza mafano. 17  Choncho ali m’sunagoge anayamba kukambirana ndi Ayuda+ ndi anthu ena opembedza Mulungu. Ndipo tsiku ndi tsiku analinso kukambirana ndi anthu amene anali kuwapeza pamsika.+ 18  Koma ena anzeru za dziko, Aepikureya ndi Asitoiki+ anayamba kutsutsana naye. Ndipo ena anali kunena kuti: “Kodi nayenso wobwetuka uyu akufuna kunena chiyani?”+ Enanso anali kunena kuti: “Akuoneka kuti ndi wofalitsa za milungu yachilendo.” Ananena zimenezi chifukwa chakuti Paulo anali kulengeza uthenga wabwino wa Yesu ndi za kuuka kwa akufa.+ 19  Choncho anamugwira n’kupita naye kubwalo la Areopagi, ndi kunena kuti: “Kodi tingadziweko za chiphunzitso chatsopanochi+ chimene iwe ukuphunzitsa? 20  Chifukwatu zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo m’makutu mwathu. Choncho tikufuna tidziwe tanthauzo la zimenezi.”+ 21  Ndipotu nzika zonse za mu Atene ndi alendo ogonera kumeneko, anali kuthera nthawi yawo yonse yopuma akufotokoza kapena kumvetsera nkhani yatsopano. 22  Tsopano Paulo anaimirira pakati pa bwalo la Areopagi+ ndi kunena kuti: “Amuna inu a mu Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambiri milungu+ kuposa mmene ena amachitira. 23  Mwachitsanzo, pamene ndinali kudutsa ndi kuyang’anitsitsa zinthu zimene mumalambira, ndapezanso guwa lansembe lolembedwa kuti ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Chotero ine ndikulalikira kwa inu za Mulungu wosadziwika amene mukumulambirayo. 24  Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.+ Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 25  Komanso satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu,+ chifukwa ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo,+ mpweya,+ ndi zinthu zonse. 26  Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi+ anapanga mtundu wonse wa anthu,+ kuti akhale padziko lonse lapansi.+ Iye anakhazikitsa nthawi zoikidwiratu+ komanso anaika malire achikhalire a malo oti anthu azikhala.+ 27  Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu,+ amufufuzefufuze ndi kumupezadi,+ ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28  Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo,+ monga mmene andakatulo+ ena pakati panu anenera kuti, ‘Pakuti ndife mbadwa zake.’ 29  “Popeza kuti ndife mbadwa za Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo+ ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu.+ 30  Zoona, Mulungu analekerera nthawi ya kusadziwa koteroko,+ koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape.+ 31  Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa+ kwa akufa.” 32  Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka monyodola,+ pamene ena anati: “Chabwino, udzatiuzenso zimenezi nthawi ina.” 33  Choncho Paulo anachoka pakati pawo. 34  Koma anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatira a Yesu. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, woweruza m’bwalo la Areopagi,+ mayi wina dzina lake Damarisi ndi ena ambiri.

Mawu a M'munsi