Machitidwe 12:1-25

12  Nthawi imeneyo m’pamene Mfumu Herode* anayamba kuzunza+ ena a mumpingo.  Yakobo m’bale wake wa Yohane+ anamupha ndi lupanga.+  Ataona kuti zimenezi zasangalatsa Ayuda,+ anamanganso Petulo. (Amenewa anali masiku a mikate yopanda chofufumitsa.)+  Atamugwira, anamutsekera m’ndende+ ndipo anamupereka m’manja mwa magulu anayi a asilikali, kuti azisinthana pomulondera. Gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Cholinga cha Herode chinali chakuti adzamuonetse kwa anthu pambuyo pa pasika.+  Chotero Petulo anakhala akusungidwa m’ndendemo, koma mpingo unali kumupempherera+ mosalekeza kwa Mulungu ndi mtima wonse.  Tsopano Herode atakonzeka kuti abweretse Petulo kwa anthu, usiku umenewo Petuloyo anali chigonere ali womangidwa ndi maunyolo awiri pakati pa asilikali awiri. Pakhomo panalinso alonda olondera ndende.  Mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimirira+ chapafupi, ndipo kuwala kunaunika m’chipinda cha ndendecho. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo mwa kumugunda m’nthiti,+ n’kunena kuti: “Dzuka msanga!” Pamenepo maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+  Ndiyeno mngeloyo+ anamuuza kuti: “Konzeka ndipo uvale nsapato zako.” Iye anachita zimenezo. Kenako anamuuza kuti: “Vala malaya ako akunja+ ndipo uzinditsatira.”  Pamenepo anatuluka ndi kumamutsatira, koma iye sanadziwe kuti zimene zinali kuchitika ndi mngelozo zinali zenizeni. Ankangoganiza kuti akuona masomphenya.+ 10  Atapitirira gulu loyamba la asilikali a pachipata ndi lachiwiri, anafika pachipata chachitsulo cholowera mumzinda, ndipo chinawatsegukira chokha.+ Pamene anatuluka anayendera limodzi msewu umodzi wokha, ndipo nthawi yomweyo mngelo uja anamuchokera. 11  Koma Petulo nzeru zitamubwerera, anati: “Ndadziwa tsopano kuti Yehova ndiye watumiza mngelo wake+ kudzandilanditsa+ m’manja mwa Herode, komanso kudzandilanditsa ku zonse zimene anthu achiyuda anali kuyembekezera.” 12  Ataganizira zimene zinachitikazo, iye anapita kunyumba ya Mariya, mayi wake wa Yohane wotchedwanso Maliko.+ Kumeneko anthu ambiri anali atasonkhana pamodzi ndipo anali kupemphera. 13  Pamene anagogoda pachitseko cha pachipata, mtsikana wantchito dzina lake Roda anapita kuti akaone amene akugogoda. 14  Koma atazindikira mawu a Petulo, sanatsegule chipatacho chifukwa cha chimwemwe. M’malomwake, anathamangira mkati ndi kukanena kuti Petulo waima pachipata. 15  Iwo anamunena kuti: “Wachita misala eti!” Koma iye analimbikira kunena motsimikiza kuti akunena zoona. Iwo tsopano anayamba kunena kuti: “Ndi mngelo wake ameneyo.”+ 16  Koma Petulo anapitiriza kugogoda. Iwo atatsegula, anamuona ndipo anadabwa kwambiri. 17  Koma iye anawakwezera dzanja+ kuti akhale chete, ndipo anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Yehova anamutulutsira m’ndende. Kenako iye anati: “Zinthu zimenezi mukazifotokoze kwa Yakobo+ ndi kwa abale.” Atatero anatuluka n’kupita kumalo ena. 18  Tsopano kutacha,+ panali chipwirikiti pakati pa asilikali aja posadziwa chimene chachitikira Petulo. 19  Herode+ anafunafuna Petulo pena paliponse, ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alondawo ndi mafunso ndi kulamula kuti awatenge, akawapatse chilango.+ Pamenepo Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya, kumene anakhalako kanthawi ndithu. 20  Tsopano Herode anali wokwiya ndi anthu a ku Turo ndi ku Sidoni, ndipo anafuna kuwathira nkhondo. Choncho onse anabwera kwa iye mogwirizana. Ndipo iwo atanyengerera Balasito, amene anali woyang’anira chipinda chogona cha mfumu, anayamba kupempha mtendere. Iwo anachita zimenezi chifukwa dziko lawo linali kudalira chakudya+ chochokera m’dziko la mfumuyo. 21  Koma pa tsiku loikidwiratu, Herode anavala zovala zake zachifumu ndi kukhala pampando wake woweruzira milandu, ndi kuyamba kulankhula nawo. 22  Anthu osonkhanawo atamva mawu ake anayamba kufuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu ayi!”+ 23  Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha,+ chifukwa sanapereke ulemerero kwa Mulungu.+ Ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira. 24  Koma mawu+ a Yehova anapitiriza kukula ndi kufalikira.+ 25  Tsopano Baranaba+ ndi Saulo atamaliza utumiki wopereka thandizo+ ku Yerusalemu, anabwerera ndi kutenga Yohane,+ wotchedwanso Maliko.

Mawu a M'munsi

Ameneyu anali Herode Agiripa Woyamba.