Machitidwe 28:1-31

28  Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita.+  Ndipo anthu olankhula chinenero chachilendo kumeneko anatisonyeza kukoma mtima kwapadera.+ Iwo anasonkha moto ndi kutilandira bwino tonse chifukwa kunali kugwa mvula ndiponso kuzizira.+  Koma pamene Paulo anatola kamtolo ka nkhuni ndi kukaika pamoto, panatuluka njoka ya mphiri chifukwa cha kutentha ndipo inaluma ndi kukanirira kudzanja la Paulo.  Anthu achinenero chachilendowo ataona njoka yapoizoni ikulendewera kudzanja lake, anayamba kuuzana kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu, chifukwa ngakhale wapulumuka panyanja, chilungamo sichinamulole kuti akhalebe ndi moyo.”  Koma iye anakutumulira njoka yapoizoniyo pamoto, ndipo sinamuvulaze.+  Iwo anali kuyembekezera kuti atupa kapena agwa mwadzidzidzi n’kufa. Koma atayembekezera nthawi yaitali n’kuona kuti palibe choopsa chimene chikumuchitikira, anasintha maganizo awo ndi kuyamba kumunena kuti ndi mulungu.+  Tsopano pafupi ndi malo amenewa, panali minda ya munthu woyang’anira chilumbacho, dzina lake Papuliyo. Iyeyu anatilandira ndi kutichereza bwino kwambiri masiku atatu.  Koma kunapezeka kuti bambo ake a Papuliyo anali chigonere akuvutika ndi malungo* komanso kamwazi. Choncho Paulo analowa mmene bambowo anali ndi kupemphera, ndipo anasanjika manja ake+ pa iwo ndi kuwachiritsa.+  Izi zitachitika, anthu ena onse pachilumbacho amene anali kudwala, nawonso anabwera kwa iye ndipo anawachiritsa.+ 10  Iwo anatilemekeza mwa kutipatsa mphatso zambiri, komanso pamene tinali kunyamuka ulendo wathu, anatipatsa zinthu zochuluka zimene tinali kuzisowa. 11  Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pangalawa ya ku Alekizandiriya.+ Ngalawa imeneyi inaima pachilumbapo kuyembekezera kuti nyengo yachisanu ithe, ndipo inali ndi chizindikiro cha “Ana Amapasa a Zeu.” 12  Kenako tinafika padoko ku Surakusa ndipo tinakhala pamenepo masiku atatu. 13  Pochoka kumeneko, tinazungulira ndi kukafika ku Regio. Patapita tsiku limodzi, kunayamba kuwomba mphepo ya kum’mwera, ndipo pa tsiku lachiwiri tinafika ku Potiyolo. 14  Kumeneko tinapeza abale ndipo anatichonderera kuti tikhale nawo masiku 7. Kenako tinapitiriza ulendo kulowera ku Roma. 15  Abale akumeneko atamva za ife, anabwera kudzatichingamira ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo. Paulo atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.+ 16  Pamapeto pake, titalowa mu Roma, Paulo analoledwa+ kumakhala yekha ndi msilikali womulondera. 17  Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana pamodzi, anawauza kuti: “Amuna inu, abale anga, ngakhale kuti sindinachite kanthu kotsutsana ndi anthu kapena mwambo wa makolo athu,+ ndinagwidwa mu Yerusalemu ndi kuperekedwa m’manja mwa Aroma monga mkaidi.+ 18  Ndipo iwowa atafufuza,+ anali ofunitsitsa kundimasula,+ pakuti sanapeze chifukwa mwa ine choyenera chilango cha imfa.+ 19  Koma Ayuda atapitiriza kutsutsa zimenezo, ndinakakamizika kupempha+ kudzaonekera kwa Kaisara, komatu sikuti ndinali ndi kanthu koti ndidzaneneze mtundu wanga ayi. 20  Pa chifukwa chimenechi, ndinapempha kuti ndikuoneni ndi kulankhula nanu, pakuti ndamangidwa ndi unyolo uwu+ chifukwa cha chiyembekezo+ cha Isiraeli.” 21  Iwo anamuyankha kuti: “Ife sitinalandire makalata alionse ochokera ku Yudeya onena za iwe. Palibenso aliyense mwa abale amene afika kuno, amene wanena kapena kukambapo choipa chilichonse chokhudza iwe. 22  Komabe tikufuna kumva maganizo ako, chifukwa kunena zoona, ife tonse timadziwa kuti gulu lampatuko limeneli+ amalinenera zoipa kwina kulikonse.”+ 23  Pamenepo iwo anapangana naye tsiku, ndipo anabwera mwaunyinji kumene iye anali kukhala. Chotero kuyambira m’mawa mpaka madzulo, anawafotokozera nkhani yonse pochitira umboni mokwanira za ufumu wa Mulungu.+ Anachitira umboniwo mwa kugwiritsa ntchito mfundo zokopa zokhudza Yesu, kuchokera m’chilamulo cha Mose+ ndi mu Zolemba za aneneri.+ 24  Ena anayamba kukhulupirira+ zimene ananenazo, koma ena sanakhulupirire.+ 25  Choncho, popeza anali kutsutsana okhaokha, anayamba kuchoka, koma Paulo ananenabe mawu amodzi awa: “Mzimu woyera unanena zoona kwa makolo anu kudzera mwa Yesaya mneneri. 26  Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma osazindikira ngakhale pang’ono. Kupenya mudzapenya ndithu, koma osaona ngakhale pang’ono.+ 27  Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Iwo atseka maso awo, kuti asaone ndi maso awo, asamve ndi makutu awo ndi kuti asazindikire ndi mtima wawo n’kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+ 28  Chotero dziwani kuti njira ya Mulungu yopulumutsira anthu, yatumizidwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo mosakayikira, iwo adzaimvetsera.”+ 29 * —— 30  Choncho Paulo anakhalabe m’nyumba yake yolipira kwa zaka ziwiri zathunthu,+ ndipo onse obwera kudzamuona anali kuwalandira ndi manja awiri. 31  Anali kuwalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, mwaufulu wonse wa kulankhula+ popanda choletsa.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.