Machitidwe 9:1-43

9  Koma Saulo anapitiriza kuopseza ophunzira+ a Ambuye komanso anali wofunitsitsa kuwapha.+ Choncho anapita kwa mkulu wa ansembe  kukamupempha zikalata za chilolezo zopita nazo kumasunagoge a ku Damasiko. Anapempha zikalatazo kuti akakapeza wina aliyense wotsatira Njirayo,*+ mwamuna kapena mkazi, akabwere naye ku Yerusalemu ali womangidwa.  Ali pa ulendo wakewo, anayandikira Damasiko. Mwadzidzidzi anangoona ngwee! kuwala kochokera kumwamba kutamuzungulira.+  Pamenepo anagwa pansi ndipo anamva mawu akumuuza kuti: “Saulo, Saulo n’chifukwa chiyani ukundizunza?”+  Iye anati: “Mbuyanga, ndinu ndani kodi?” Anamuyankha kuti: “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.+  Komabe nyamuka,+ ulowe mumzindawo, ndipo ukauzidwa zoyenera kuchita.”  Amuna amene anali naye limodzi pa ulendowo,+ anangoima chilili kusowa chonena.+ Iwo anamva ndithu mawuwo,+ koma sanaone munthu aliyense.  Tsopano Saulo anaimirira, koma ngakhale anali atatsegula maso, sanali kuona chilichonse.+ Choncho anamugwira dzanja ndi kumulondolera njira ndipo analowa naye mu Damasiko.  Saulo anakhala masiku atatu osatha kuona,+ osadya kapena kumwa kanthu. 10  Mu Damasiko munali wophunzira wina dzina lake Hananiya.+ Ndiyeno Ambuye analankhula naye m’masomphenya kuti: “Hananiya!” Iye anayankha kuti: “Ine, Ambuye.” 11  Ambuyewo anamuuza kuti: “Nyamuka, upite kumsewu wotchedwa Msewu Wowongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu wa ku Tariso, dzina lake Saulo.+ Iyeyo akupemphera, 12  ndipo m’masomphenya waona munthu dzina lake Hananiya, amene anafika ndi kumuika manja kuti ayambenso kuona.”+ 13  Koma Hananiya anayankha kuti: “Ambuye, ndamva kwa anthu ambiri za munthu ameneyu. Ndamva zoipa zambiri zimene anachitira oyera anu ku Yerusalemu. 14  Ndipo panopo ansembe aakulu amupatsa mphamvu kuti amange onse oitana pa dzina lanu.”+ 15  Koma Ambuye anamuuza kuti: “Nyamuka uzipita, chifukwa munthu ameneyu ndi chiwiya changa chochita kusankhidwa+ chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina,+ komanso kwa mafumu+ ndi ana a Isiraeli. 16  Pakuti ndidzamuonetsa bwinobwino zopweteka zonse zimene ayenera kumva chifukwa cha dzina langa.”+ 17  Choncho Hananiya anapita ndi kukalowa m’nyumbamo. Ndiyeno anamuika manja n’kunena kuti: “M’bale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene waonekera kwa iwe pamsewu umene wadzera, wandituma ine. Wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona ndi kutinso udzazidwe ndi mzimu woyera.”+ 18  Nthawi yomweyo m’maso mwa Saulo munagwa tinthu tooneka ngati mamba a nsomba, ndipo anayambanso kuona. Kenako anapita kukabatizidwa, 19  ndipo atadya chakudya anapezanso mphamvu.+ Kwa masiku angapo anakhala ndi ophunzira ku Damasiko.+ 20  Nthawi yomweyo anayamba kulalikira za Yesu m’masunagoge,+ kuti Ameneyu ndiye Mwana wa Mulungu. 21  Onse omumvetsera anadabwa kwambiri ndipo anali kunena kuti: “Kodi munthu uyu si uja anavutitsa koopsa+ oitana pa dzina limeneli a ku Yerusalemu? Kodi si chimenenso anabwerera kuno, kuti adzawagwire ndi kuwatengera kwa ansembe aakulu atawamanga?”+ 22  Koma Saulo anapitiriza kupeza mphamvu zambiri, ndipo anali kuthetsa nzeru Ayuda okhala mu Damasiko powafotokozera mfundo zomveka zotsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+ 23  Tsopano patapita masiku ambiri, Ayudawo anasonkhana pamodzi ndi kupangana zoti amuphe.+ 24  Koma chiwembu chawocho chinadziwika kwa Saulo. Komabe iwo anali kuyang’anira mosamala m’zipata zonse usana ndi usiku kuti amuphe.+ 25  Choncho usiku, ophunzira ake anamuika m’dengu ndi kumutulutsira pawindo la mpanda, n’kumutsitsira kunja.+ 26  Atafika ku Yerusalemu+ anayesetsa kuti agwirizane ndi ophunzira kumeneko. Koma onse ankamuopa, chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunzira. 27  Choncho Baranaba anamuthandiza+ mwa kupita naye kwa atumwi. Kumeneko iye anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Saulo anaonera Ambuye+ amene analankhula naye pamsewu.+ Anawafotokozeranso mmene Saulo analankhulira molimba mtima ku Damasiko+ m’dzina la Yesu. 28  Pamenepo anapitiriza kukhala nawo, n’kumayenda momasuka mu Yerusalemu, ndiponso anali kulankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye.+ 29  Ndipo anali kulankhulana ndi kutsutsana ndi Ayuda olankhula Chigiriki. Koma iwo anayesa kupeza njira yoti amuphere.+ 30  Abale atazindikira zimenezi, anam’tengera ku Kaisareya ndi kumutumiza ku Tariso.+ 31  Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira. 32  Tsopano pamene Petulo anali kuyendayenda m’madera onse, anafikanso kwa oyera amene anali kukhala ku Luda.+ 33  Kumeneko anapeza munthu wina dzina lake Eneya. Popeza kuti anali wakufa ziwalo, anakhala ali chigonere pabedi lake kwa zaka 8. 34  Ndiyeno Petulo anamuuza kuti:+ “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa.+ Dzuka ndi kuyala bwino bedi lakoli.” Nthawi yomweyo anadzuka. 35  Onse okhala mu Luda ndi m’chigwa cha Sharoni+ anamuona, ndipo anatembenukira kwa Ambuye.+ 36  Koma ku Yopa+ kunali wophunzira wina dzina lake Tabita, dzina limene polimasulira limatanthauza Dorika.* Tabita anali kuchita ntchito zabwino zambiri,+ ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka. 37  Ndipo m’masiku amenewo iye anadwala n’kumwalira. Choncho anamusambitsa ndi kumugoneka m’chipinda cham’mwamba. 38  Popeza kuti Luda anali pafupi ndi Yopa,+ ophunzirawo atamva kuti Petulo ali mumzinda umenewu, anatumiza amuna awiri kukamudandaulira kuti: “Chonde mufike kwathuku msanga.” 39  Pamenepo Petulo ananyamuka n’kupita nawo limodzi. Atafika kumeneko, iwo anamutengera m’chipinda cham’mwamba chija. Ndipo akazi onse amasiye anabwera kwa iye akulira ndi kumuonetsa malaya ambiri akunja ndi amkati+ amene Dorika anali kusoka pamene anali nawo.+ 40  Koma Petulo anatulutsa anthu onse,+ ndiyeno anagwada pansi ndi kupemphera. Kenako anatembenukira mtembowo ndi kunena kuti: “Tabita, dzuka!” Pamenepo mayiyo anatsegula maso ake, ndipo mmene anaona Petulo, anadzuka n’kukhala tsonga.+ 41  Tsopano Petulo anamupatsa dzanja lake ndi kumuimiritsa.+ Atatero anaitana oyerawo ndi akazi amasiye aja, ndipo anamupereka kwa iwo ali wamoyo.+ 42  Izi zinadziwika mu Yopa monse, ndipo ambiri anakhala okhulupirira mwa Ambuye.+ 43  Kwa masiku angapo Petulo anakhalabe mu Yopa+ kwa munthu wina wofufuta zikopa, dzina lake Simoni.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “Njirayo” akutanthauza moyo ndi chiphunzitso chachikhristu.
Dzina lakuti “Dorika” n’chimodzimodzi ndi lakuti “Tabita.” Mayina onsewa amatanthauza “Mbawala.”