Machitidwe 6:1-15
6 Tsopano m’masiku amenewo, pamene ophunzirawo anali kuchulukirachulukira, Ayuda olankhula Chigiriki+ anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chiheberi. Chifukwa chakuti akazi amasiye achigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagawidwe ka chakudya cha tsiku ndi tsiku.+
2 Chotero atumwi 12 aja anaitana khamu la ophunzira ndi kunena kuti: “N’kosayenera kuti ife tisiye ntchito yophunzitsa mawu a Mulungu n’kuyamba kugawa chakudya.+
3 Chotero abale, fufuzani+ pakati panu amuna 7 a mbiri yabwino, amene ali ndi mzimu komanso nzeru zochuluka,+ kuti ife tiwaike kukhala oyang’anira ntchito yofunikayi.
4 Koma ife tidzipereka ndithu pa kupemphera ndi pa utumiki wokhudza mawu a Mulungu.”+
5 Mawu amenewa anasangalatsa khamu lonselo, mwakuti anasankha Sitefano, mwamuna wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndi mzimu woyera.+ Anasankhanso Filipo,+ Purokoro, Nikanora, Timoni, Paremena ndi Nikolao wa ku Antiokeya amene anali wotembenukira ku Chiyuda.
6 Ndiyeno anawaimiritsa pamaso pa atumwiwo, ndipo atapemphera, atumwiwo anaika manja+ awo pa iwo.
7 Pamenepo mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira ponseponse.+ Chiwerengero cha ophunzira chinali kuwonjezeka kwambiri mu Yerusalemu.+ Ndipo ansembe ambirimbiri+ anakhala okhulupirira.+
8 Tsopano Sitefano, anali wodzazidwa ndi chisomo komanso mphamvu, ndipo anali kuchita zodabwitsa ndi zizindikiro zazikulu+ pakati pa anthu.
9 Ndiyeno panafika amuna ena a gulu lotchedwa Sunagoge wa Omasulidwa, ndi ena a ku Kurene, a ku Alekizandiriya,+ komanso ena ochokera ku Kilikiya+ ndi ku Asia, kudzatsutsana ndi Sitefano.
10 Koma iwo sanathe kulimbana ndi nzeru+ zimene anasonyeza komanso mzimu woyera umene unali kumutsogolera pamene anali kulankhula.+
11 Kenako mwamseri ananyengerera amuna ena kuti anene kuti:+ “Tamumva ife ameneyu akulankhula mawu onyoza+ Mose ndi Mulungu.”
12 Pamenepo ananyanyula mitima ya anthu, akulu ndi alembi. Ndiyeno anamufikira mwadzidzidzi n’kumugwira, ndipo anapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda.+
13 Kumeneko anabweretsa mboni zonama,+ zimene zinati: “Munthu uyu sakuleka kulankhula mawu onyoza malo oyera ano ndi Chilamulo.+
14 Mwachitsanzo, ife tinamumva iyeyu akunena kuti Yesu Mnazareti uja adzawononga malo oyera ano ndi kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”
15 Ndipo pamene onse amene anakhala m’bwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda anamuyang’anitsitsa,+ anaona kuti nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.+