Machitidwe 8:1-40

8  Ndiyeno Saulo anali kuvomereza za kupha Sitefano.+ Tsiku limenelo, panabuka chizunzo chachikulu+ choukira mpingo umene unali mu Yerusalemu. Onse anabalalikira+ m’zigawo za Yudeya ndi Samariya, kupatulapo atumwi okha.  Koma amuna ena oopa Mulungu anatenga Sitefano ndi kukamuika m’manda,+ ndipo anamulira kwambiri.+  Tsopano Saulo anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Anali kulowa m’nyumba ndi nyumba, ndi kukokera panja amuna ndi akazi omwe, n’kukawaponya m’ndende.+  Komabe, amene anabalalitsidwa aja anapita m’zigawozo akulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.+  Koma Filipo anapita kumzinda wa Samariya+ ndi kuyamba kulalikira za Khristu kwa anthu akumeneko.  Makamu a anthu anali kutchera khutu ndi mtima umodzi ndi kumvetsera zimene Filipo anali kunena. Iwo anali kumvetsera ndi kuona zizindikiro zimene iye anali kuchita.  Kumeneko kunali anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yonyansa,+ ndipo inali kufuula mokweza mawu ndi kutuluka. Ndipo anthu ambiri amene anali akufa ziwalo+ ndi olumala anali kuchiritsidwa.  Choncho mumzindawo munali chimwemwe chachikulu.+  Tsopano mumzindawo munalinso munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanachitike, iyeyu anali kuchita zamatsenga+ ndi kudabwitsa anthu onse mu Samariya. Anali kudzitamandira kuti anali wopambana.+ 10  Chotero onse, aang’ono ndi aakulu omwe, anali kumumvetsera ndi kunena kuti: “Munthu uyu ndiyedi Mphamvu ya Mulungu, imene tingati ndi Yaikulu.” 11  Chotero anali kumumvetsera chifukwa anawadabwitsa ndi zamatsenga zakezo kwa nthawi yaitali. 12  Koma iwo atakhulupirira Filipo, amene anali kulengeza uthenga wabwino wonena za ufumu wa Mulungu+ ndi za dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.+ 13  Simoni uja nayenso anakhala wokhulupirira. Atabatizidwa, sanali kusiyana ndi Filipo+ kulikonse. Moti anali kudabwa poona zizindikiro ndi ntchito zamphamvu zazikulu zikuchitika. 14  Pamene atumwi ku Yerusalemu anamva kuti Asamariya alandira mawu a Mulungu,+ anawatumizira Petulo ndi Yohane. 15  Iwo anapitadi kumeneko ndipo anawapempherera kuti alandire mzimu woyera.+ 16  Pa nthawiyi n’kuti mzimu woyerawo usanafike pa aliyense wa iwo, koma anali atangobatizidwa chabe m’dzina la Ambuye Yesu.+ 17  Chotero atumwiwo anayamba kuika manja awo pa anthuwo,+ ndipo analandira mzimu woyera. 18  Tsopano Simoni uja ataona kuti atumwiwo, mwa kungoika manja pa anthuwo, mzimu woyera unali kuperekedwa, anafuna kuwapatsa ndalama.+ 19  Iye ananena kuti: “Inenso mundipatseko mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndizimuika manja azilandira mzimu woyera.” 20  Koma Petulo anamuuza kuti: “Siliva wakoyo awonongeke nawe limodzi, chifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulere ya Mulungu ungaipeze ndi ndalama.+ 21  Ulibe gawo kapena mbali mu ntchito imeneyi, pakuti mtima wako si wowongoka pamaso pa Mulungu.+ 22  Chotero lapa choipa chakochi, ndipo upemphe kwa Yehova mopembedzera+ kuti ngati n’kotheka, maganizo oipa a mtima wakowo akhululukidwe. 23  Pakuti ndaona kuti ndiwe ndulu yaululu+ ndipo mwa iwe mwadzaza kusalungama.”+ 24  Poyankha Simoni uja anati: “Amuna inu, ndipemphereni chonde kwa Yehova mopembedzera+ kuti zonse mwanenazo zisandigwere.” 25  Choncho atatha kuchitira umboni mokwanira ndi kulankhula mawu a Yehova, anabwerera ku Yerusalemu. Pamene anali kubwerera anali kulengeza uthenga wabwino m’midzi yambiri ya Asamariya.+ 26  Koma mngelo wa Yehova+ analankhula kwa Filipo kuti: “Nyamuka ndi kulowera kum’mwera, kumsewu wochokera ku Yerusalemu kupita ku Gaza.” (Umenewu ndi msewu wa m’chipululu.) 27  Choncho, ananyamuka ndi kupita. Kumeneko anakumana ndi nduna+ ya ku Itiyopiya,+ munthu waulamuliro pansi pa Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Iye anali woyang’anira chuma chonse cha mfumukaziyo. Iyeyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu,+ 28  ndipo tsopano anali kubwerera kwawo. Ndunayi ili pa ulendo wobwerera kwawo itakhala m’galeta* lake, inali kuwerenga mokweza m’buku la mneneri Yesaya.+ 29  Ndiyeno mzimu unauza+ Filipo kuti: “Yandikira galeta lakelo uyende naye limodzi.” 30  Filipo anathamanga m’mbali mwa galetalo ndi kumumva akuwerenga mokweza m’buku la Yesaya mneneri. Ndipo Filipo anafunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” 31  Poyankha iye anati: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Pamenepo anachonderera Filipo kuti akwere ndi kukhala naye m’galetamo. 32  Ndime ya m’Malemba imene anali kuwerenga mokwezayo, mawu ake ndi awa: “Iye anamutengera kokamupha ngati nkhosa. Ngati mwana wa nkhosa wongokhala chete pamene akumumeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+ 33  Pamene anali kumuchitira zinthu zochititsa manyazi, anamuchotsera chiweruzo chomuyenera.+ Ndani angafotokoze tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo ake? Chifukwa moyo wake wachotsedwa padziko lapansi.”+ 34  Poyankha nduna ija inauza Filipo kuti: “Ndiuzeni chonde, Kodi mneneriyu akunena za ndani? Za iye mwini kapena za munthu wina?” 35  Pamenepo Filipo, anayambira pa Lemba+ limeneli kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu.+ 36  Akuyenda choncho mumsewumo, anapeza madzi ambiri, ndipo nduna ija inati: “Taonani! Si awa madzi ambiri. Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?”+ 37 * —— 38  Atatero analamula galetalo kuti liime. Ndipo onse awiri Filipo ndi nduna ija, anatsika ndi kulowa m’madzimo ndipo anaibatiza. 39  Atatuluka m’madzimo, mzimu wa Yehova unachotsa Filipo mwamsanga pamalopo,+ ndipo nduna ija sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40  Koma Filipo anapezeka ali ku Asidodi, ndipo anayendayenda m’deralo ndi kulengeza+ uthenga wabwino m’mizinda yonse mpaka anafika ku Kaisareya.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.