Machitidwe 19:1-41

19  Nthawi inayake, Apolo+ ali ku Korinto, Paulo anadzera kumadera a kumtunda mpaka anafika ku Efeso.+ Kumeneko anapezako ophunzira ena,  ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandira mzimu woyera+ mutakhala okhulupirira?” Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu sitinamvepo kuti kuli mzimu woyera.”+  Iye anawafunsanso kuti: “Nanga munabatizidwa ubatizo wamtundu wanji?” Iwo anayankha kuti: “Tinabatizidwa ubatizo wa Yohane.”+  Pamenepo Paulo anati: “Yohane anabatiza anthu ubatizo umene unali chizindikiro chakuti munthu walapa.+ Anali kuuza anthu kuti akhulupirire amene anali kubwera m’mbuyo mwake,+ kutanthauza Yesu.”  Atamva zimenezi, anthuwo anabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.+  Ndiyeno Paulo atawaika manja,+ mzimu woyera unafika pa iwo, ndipo anayamba kulankhula malilime ndi kunenera.+  Onse pamodzi anali amuna pafupifupi 12.  Kwa miyezi itatu, anali kupita kusunagoge+ kumene anali kulankhula molimba mtima. Kumeneko anali kukamba nkhani ndi kuwafotokozera mfundo zokhutiritsa zokhudza ufumu+ wa Mulungu.  Koma ena anapitiriza kuumitsa mitima yawo osakhulupirira,+ ndipo anali kunena zonyoza Njirayo+ pamaso pa khamu la anthu. Choncho iye anawachokera+ n’kuchotsanso ophunzirawo pakati pawo.+ Ndipo tsiku ndi tsiku anali kukamba nkhani m’holo pasukulu ya Turano. 10  Izi zinachitika kwa zaka ziwiri,+ moti onse okhala m’chigawo cha Asia,+ Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye. 11  Mulungu anapitiriza kuchita ntchito zamphamvu zodabwitsa kudzera mwa Paulo.+ 12  Moti anthu anali kutenga ngakhale mipango yopukutira thukuta ndi maepuloni amene akhudza thupi la Paulo n’kupita nazo kwa odwala,+ ndipo matenda awo anali kutheratu. Mizimu yoipa nayonso inali kutuluka.+ 13  Koma Ayuda ena oyendayenda amene anali kutulutsa ziwanda,+ anayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu+ pofuna kuchiritsa anthu okhala ndi mizimu yoipa. Anali kunena kuti: “Ndikukulamulani+ mwa Yesu amene Paulo akumulalikira.” 14  Choncho panali ana aamuna 7 a Sikeva, wansembe wamkulu wachiyuda, amene anali kuchita zimenezi. 15  Koma mzimu woipa poyankha unawauza kuti: “Ine Yesu ndikumudziwa,+ ndipo Paulo ndikumudziwanso bwino.+ Nanga inuyo ndinu ndani?” 16  Kenako, munthu amene anali ndi mzimu woipa uja anawalumphira.+ Analimbana nawo mmodzimmodzi ndi kuwagonjetsa onsewo, mwakuti anatuluka m’nyumbamo ndi kuthawa ali maliseche komanso atavulala. 17  Izi zinadziwika kwa onse, Ayuda ndi Agiriki amene anali kukhala ku Efeso. Chotero onse anagwidwa ndi mantha,+ ndipo dzina la Ambuye Yesu linapitirira kulemekezedwa.+ 18  Anthu ambiri amene anakhala okhulupirira anali kubwera kudzaulula machimo+ awo ndi kufotokoza poyera zoipa zimene anali kuchita. 19  Ndithudi, ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga+ anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000. 20  Choncho mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndi kugonjetsa zopinga zambiri.+ 21  Tsopano izi zitatha, Paulo anatsimikiza mumtima mwake kupita ku Yerusalemu,+ kudzera ku Makedoniya+ ndi ku Akaya. Iye anati: “Ndikakafika kumeneko, ndiyeneranso kukaona ku Roma.”+ 22  Choncho ku Makedoniya anatumizako awiri mwa anthu amene anali kumutumikira, omwe ndi Timoteyo+ ndi Erasito.+ Koma iye anatsalira m’chigawo cha Asia kwa kanthawi ndithu. 23  Pa nthawi yomweyo panabuka chisokonezo chachikulu+ chokhudzana ndi Njirayo.+ 24  Panali munthu wina wosula siliva dzina lake Demetiriyo. Amisiri anali kupeza phindu lochuluka chifukwa cha ntchito yake yopanga tiakachisi tasiliva ta Atemi.+ 25  Choncho Demetiriyo anasonkhanitsa amisiriwo, limodzi ndi anthu ogwira ntchito yokhudzana ndi zinthu zimenezo.+ Ndiyeno anawauza kuti: “Amuna inu, mukudziwa bwino kuti chuma chathu chimachokera m’ntchito imeneyi.+ 26  Tsopano mukuona ndipo mukumva za Paulo ameneyu, kuti si mu Efeso+ mokha muno mmene wakopa anthu ambirimbiri ndi kuwapatutsira ku chikhulupiriro china. Wachita zimenezi pafupifupi m’chigawo chonse cha Asia. Iye akumanena kuti milungu yopangidwa ndi manja+ si milungu ayi. 27  Ndipo chimene chikuopsa kwambiri si kunyozeka kwa ntchito yathu kokha ayi, komanso kachisi wa mulungu wamkulu wamkazi Atemi+ adzayesedwa wopanda pake. Ndipotu aliyense m’chigawo chonse cha Asia komanso padziko lapansi kumene kuli anthu amalemekeza Atemi. Koma chifukwa cha zimene Paulo akunena ulemerero umenewo watsala pang’ono kuti utheretu.” 28  Atamva zimenezi anthuwo anakwiya kwambiri ndi kuyamba kufuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” 29  Pamenepo mumzindawo munadzaza chisokonezo, ndipo onse pamodzi anathamangira m’bwalo la masewera, atagwira Gayo ndi Arisitako n’kuwakokera m’bwalomo. Gayo ndi Arisitako+ anali anzake a Paulo amene anali kuyenda naye ndipo kwawo kunali ku Makedoniya. 30  Choncho Paulo anafuna kulowa mkati mwa khamu la anthulo, koma ophunzira sanamulole. 31  Ngakhalenso ena oyang’anira zikondwerero ndi masewera, amene anali anzake anamutumizira uthenga womuchonderera kuti asaike moyo wake pachiswe mwa kulowa m’bwalo la maseweralo. 32  Kunena zoona, khamu lonse linali pa chipwirikiti, ena anali kufuula zina enanso zina.+ Mwakuti ambiri a iwo sanadziwe n’komwe chifukwa chimene anasonkhanira pamodzi. 33  Choncho iwo anatulutsa Alekizanda m’khamulo, ndipo Ayuda anamukankhira kutsogolo. Kenako Alekizanda anatambasula dzanja lake kuti alankhule podziteteza kwa anthuwo. 34  Koma iwo atazindikira kuti iye ndi Myuda, onse pamodzi anafuula kwa maola pafupifupi awiri kuti: “Wamkulu+ ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” 35  Pamapeto pake, woyang’anira mzinda atakhalitsa chete+ khamu la anthulo, anati: “Anthu inu a mu Efeso, alipo kodi munthu amene sadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo woyang’anira kachisi wa Atemi wamkulu ndi chifaniziro chimene chinagwa kuchokera kumwamba? 36  Chotero, popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, muyenera kudekha, musachite zinthu mopupuluma.+ 37  Pakuti mwabweretsa anthu awa amene si akuba mu akachisi kapena onyoza mulungu wathu wamkaziyo. 38  Choncho ngati Demetiriyo+ ndi amisiri ali nawowa akuimba mlandu munthu, pamakhala masiku a milandu+ ndipo abwanamkubwa+ alipo. Akasumirane kumeneko. 39  Koma ngati mukufuna zina zoposa pamenepa, zimenezo ziyenera kukagamulidwa pabwalo lovomerezeka. 40  Chifukwa kunena zoona, kuopsa kwa zimene zachitika lerozi n’kwakuti angathe kutiimba nazo mlandu woukira boma. Palibiretu chifukwa chomveka chimene tingapereke pa chipolowe chimene chachitikachi.” 41  Atanena zimenezi,+ anauza osonkhanawo kuti achoke pamalowo.+

Mawu a M'munsi